Yesaya 20:1-6

20  M’chaka chimene Tatani*+ anapita ku Asidodi,+ atatumidwa ndi Sarigoni mfumu ya Asuri,+ n’kukamenyana ndi mzinda wa Asidodi n’kuulanda,+  pa nthawi imeneyo Yehova analankhula kudzera mwa Yesaya mwana wa Amozi,+ kuti: “Pita+ ukavule chiguduli chimene chili m’chiuno mwako+ ndipo ukavulenso nsapato zimene zili kuphazi kwako.”+ Iye anakachitadi zimenezo, n’kumayenda wopanda zovala* ndiponso wopanda nsapato.+  Kenako Yehova anati: “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wayendera wopanda zovala ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu, kuti akhale chizindikiro+ ndi chenjezo kwa Iguputo+ ndi Itiyopiya,+  momwemonso mfumu ya Asuri idzagwira gulu la anthu ku Iguputo+ ndi ku Itiyopiya n’kupita nawo ku ukapolo kudziko lina, anyamata ndi nkhalamba, ali opanda zovala ndi opanda nsapato, ndiponso matako awo ali pamtunda. Pamenepo, umaliseche wa Iguputo udzaonekera.+  Iwo adzachita mantha ndiponso manyazi chifukwa chakuti anali kudalira Itiyopiya+ komanso chifukwa chakuti anali kusirira kukongola kwa Iguputo.+  M’tsiku limenelo, munthu wokhala m’dziko lino la m’mphepete mwa nyanja adzati, ‘Taonani zimene zachitikira dziko limene tinali kulidalira lija, limene tinathawirako kuti litithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya Asuri.+ Ndiye ifeyo atipulumutse ndani?’”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “mkulu wa asilikali.”
Kapena kuti “atavala zovala zam’kati zokha.”