Yesaya 17:1-14
17 Uwu ndi uthenga wokhudza Damasiko:+ “Taonani! Damasiko wachotsedwa kuti asakhalenso mzinda, ndipo wakhala bwinja, wakhala mulu wa zinthu zogumukagumuka.+
2 Mizinda ya Aroweri+ imene yasiyidwa m’mbuyo yangosanduka malo okhala ziweto, kumene ziwetozo zimagona pansi popanda woziopsa.+
3 Mu Efuraimu mulibenso mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,+ ndipo mu Damasiko mulibenso ufumu.+ Ulemerero wa anthu otsala mu Siriya udzatha ngati ulemerero wa ana a Isiraeli,” akutero Yehova wa makamu.+
4 “M’tsiku limenelo, ulemerero wa Yakobo udzachepa,+ ndipo thupi lake lonenepa lidzaonda.+
5 Munthu wokolola akamadzadula tirigu m’munda ndipo dzanja lake likamadzakolola ngala za tirigu,+ adzakhala ngati munthu wokunkha ngala za tirigu m’chigwa cha Arefai.+
6 M’dzikolo mudzangotsala zokunkha ngati mmene zimatsalira mumtengo wa maolivi akaugwedeza: pamwamba pa nthambi padzangokhala maolivi awiri kapena atatu akupsa. Panthambi zobala zipatso padzangokhala maolivi anayi kapena asanu okha,” akutero Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+
7 M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzayang’ana kumwamba, kwa amene anamupanga. Maso ake adzayang’anitsitsa Woyera wa Isiraeli.+
8 Iye sadzayang’ana maguwa a nsembe,+ omwe ndi ntchito ya manja ake.+ Sadzayang’anitsitsa zimene zala zake zapanga, kaya mizati yopatulika kapena maguwa ofukizirapo zonunkhira.+
9 M’tsiku limenelo mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzakhala ngati malo amene angosiyidwa m’nkhalango. Idzakhala ngati nthambi imene anthu angoisiya chifukwa cha ana a Isiraeli, ndipo idzakhala bwinja.+
10 Popeza waiwala+ Mulungu wa chipulumutso chako,+ ndipo Thanthwe+ la chitetezo chako sunalikumbukire, n’chifukwa chake ukulima minda yokongola n’kumabzalamo mphukira ya mlendo.
11 Masana ukhoza kuumangira mpanda wabwino munda wakowo, ndipo m’mawa ukhoza kuchititsa mbewu yako kuti iphuke. Koma zokolola zake zidzathawa m’tsiku la matenda ndi ululu wosachiritsika.+
12 Tsoka kwa mitundu ya anthu ambirimbiri amene akuchita chipwirikiti, amene akuwinduka ngati nyanja. Tsoka kwa magulu a mitundu ya anthu aphokoso, amene akusokosera ngati mkokomo wa madzi amphamvu.+
13 Mitundu ya anthu+ idzasokosera ngati mkokomo wa madzi ambiri. Iye adzawadzudzula,+ ndipo iwo adzathawira kutali. Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo m’mapiri ndiponso adzauluzika ngati tizitsotso touluzika ndi mphepo yamkuntho.+
14 Madzulo kudzakhala zoopsa zamwadzidzidzi. Kusanache, zidzachoka.+ Izi n’zimene zidzachitikire anthu otilanda zinthu, ndipo n’zimene zidzagwere anthu oba katundu wathu.+
Mawu a M'munsi
^ “Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa kumbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.