Yesaya 26:1-21

26  M’tsiku limenelo,+ m’dziko la Yuda+ mudzaimbidwa nyimbo+ yakuti: “Ife tili ndi mzinda wolimba.+ Iye waika chipulumutso ngati mipanda ndiponso ngati chiunda chomenyerapo nkhondo.*+  Anthu inu, tsegulani zipata+ kuti mtundu wolungama, umene ukuchita zinthu mokhulupirika ulowe.+  Anthu amene ali ndi mtima wosagwedezeka mudzawateteza powapatsa mtendere wosatha,+ chifukwa amadalira inu.+  Anthu inu muzidalira Yehova+ nthawi zonse, pakuti Ya* Yehova ndiye Thanthwe+ mpaka kalekale.  “Pakuti iye watsitsa anthu okhala pamalo okwezeka,+ okhala m’mudzi wokwezeka.+ Mudziwo wautsitsa. Wautsitsira pansi, waugwetsa mpaka pafumbi.+  Phazi lidzaupondaponda. Mapazi a munthu wosautsika ndi mapazi a anthu onyozeka, adzaupondaponda.”+  Njira ya munthu wolungama ndi yowongoka.+ Popeza inu ndinu wochita zowongoka, mudzasalaza njira ya munthu wolungama.+  Inu Yehova, ife tayembekezera inu pofunafuna njira yanu ya chilungamo.+ Mtima wathu wakhala ukulakalaka kuti ukumbukire dzina lanu, ndi zimene dzinalo limaimira.+  Usiku, mtima wanga umakulakalakani.+ Ndithu ndimakufunafunani ndi mtima wonse,+ chifukwa mukadzaweruza dziko lapansi,+ anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzira chilungamo.+ 10  Ngakhale munthu woipa atachitiridwa zabwino, sangaphunzire chilungamo.+ M’dziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zopanda chilungamo+ ndipo sadzaona ukulu wa Yehova.+ 11  Inu Yehova, dzanja lanu lakwezeka,+ koma iwo sakuliona.+ Iwo adzaona mmene mukudziperekera kwa anthu anu, ndipo adzachita manyazi.+ Ndithu, moto+ wanu udzanyeketsa adani anu. 12  Inu Yehova, mudzachita chilungamo kuti mutipatse mtendere,+ pakuti ntchito zathu zonse tazikwanitsa chifukwa cha inu.+ 13  Inu Yehova Mulungu wathu, ife takhalapo m’manja mwa ambuye ena kupatula inu.+ Koma chifukwa cha thandizo lanu, timatha kutchula dzina lanu.+ 14  Iwo afa. Sadzakhalanso ndi moyo.+ Iwo ndi akufa+ ndipo sadzaukanso.+ Pa chifukwa chimenechi, mwawatembenukira kuti muwawononge n’cholinga choti asadzatchulidwenso.+ 15  Mwakulitsa mtundu, inu Yehova. Mwakulitsa mtundu+ ndipo mwadzilemekeza.+ Mwafutukulira kutali malire onse a dzikolo.+ 16  Inu Yehova, pa nthawi ya masautso iwo atembenukira kwa inu.+ Mutawalanga, akhuthulira mitima yawo kwa inu m’pemphero lonong’ona.+ 17  Chifukwa cha inu Yehova, ife takhala ngati mkazi wapakati amene watsala pang’ono kubereka, amene akumva zowawa za pobereka, amene akulira ndi ululu wa pobereka.+ 18  Ife tinali ndi pakati, tinamva zowawa za pobereka,+ koma takhala ngati tabereka mphepo. Palibe chipulumutso chenicheni chimene tapeza m’dzikoli,+ ndipo sitikuberekanso anthu ena oti akhale panthaka ya dziko lapansili.+ 19  “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo.+ Anthu anga amene anafa adzadzuka ndi kuimirira.+ Inu anthu okhala m’fumbi, dzukani, fuulani mokondwera!+ Pakuti mame anu+ ali ngati mame a maluwa,+ ndipo dziko lapansi lidzabereka anthu amene anafa.+ 20  “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko.+ Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.+ 21  Pakuti taonani! Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala kuti adzaimbe mlandu anthu okhala m’dzikoli.+ Magazi amene dzikoli linakhetsa lidzawaonetsa poyera,+ ndipo silidzabisanso anthu amene linapha.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.