Yesaya 24:1-23

24  Taonani! Yehova akuchotsa anthu onse m’dziko n’kulisiya lopanda kanthu.+ Iye wawononga dzikolo,+ n’kubalalitsa anthu okhalamo.+  Zidzakhala chimodzimodzi kwa anthuwo ndi kwa wansembe, kwa wantchito ndi kwa mbuye wake, kwa wantchito wamkazi ndi kwa mbuye wake wamkazi, kwa wogula ndi kwa wogulitsa, kwa wobwereketsa ndi kwa wobwereka, kwa wolandira chiwongoladzanja ndi kwa wopereka chiwongoladzanja.+  Anthu onse adzachotsedwa ndithu m’dzikolo ndipo katundu yense wa m’dzikolo adzatengedwa,+ pakuti Yehova ndiye wanena mawu amenewa.+  Dzikolo likulira+ ndipo likuzimiririka. Nthaka ya dziko lapansi yafota ndipo yazimiririka. Anthu apamwamba a m’dzikolo afota.+  Dzikolo laipitsidwa ndi anthu okhalamo,+ chifukwa alambalala malamulo,+ asintha malamulowo+ ndipo aphwanya pangano limene linayenera kukhalapo mpaka kalekale.+  N’chifukwa chake temberero lameza dzikolo,+ ndipo anthu okhala m’dzikolo apezeka ndi mlandu. Chotero anthu okhala m’dzikolo achepamo, ndipo anthu amene atsalamo ndi ochepa kwambiri.+  Vinyo watsopano akulira, ndipo mtengo wa mpesa wafota.+ Anthu onse amene anali kusangalala mumtima mwawo akuusa moyo.+  Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi maseche zasiya kumveka. Phokoso la anthu okondwa kwambiri silikumvekanso. Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi zeze zaleka kumveka.+  Anthu akumwa vinyo popanda nyimbo. Akamamwa chakumwa choledzeretsa, akumachimva kuwawa. 10  Mudzi umene anthu ake anachokamo wawonongedwa.+ Nyumba iliyonse yatsekedwa kuti munthu asalowemo. 11  Anthu akulira m’misewu chifukwa chosowa vinyo. Kusangalala konse kwatha. Chisangalalo cha dzikolo chachoka.+ 12  Panopa mumzindawo mukudabwitsa kwambiri. Chipata chaphwanyidwa ndipo changokhala mulu wazinyalala.+ 13  Chotero pakatikati pa dzikolo, pakati pa anthu a mitundu ina, anthu anga adzakhala ngati zipatso zotsala mumtengo wa maolivi,+ ndiponso ngati zokunkha zotsala anthu akakolola mphesa.+ 14  Iwo adzafuula mosangalala. Adzafuula mokondwa ali kunyanja, chifukwa cha kukwezeka kwa Yehova.+ 15  N’chifukwa chake iwo adzalemekeze Yehova+ m’chigawo cha kuwala.*+ M’zilumba zakunyanja adzalemekeza dzina la Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli. 16  Tamva nyimbo zikuimbidwa kumalekezero a dziko kuti:+ “Chokongoletsera ulemerero wa Wolungama.”+ Koma ine ndinati: “Ndatheratu!+ Ndatheratu ine! Kalanga ine! Anthu ochita zachinyengo achita zachinyengo.+ Iwo achita mwachinyengo pochita zinthu zachinyengo.”+ 17  Mantha, dzenje ndi msampha zili pa iwe, munthu wokhala m’dzikoli.+ 18  Aliyense wothawa phokoso la chinthu chochititsa mantha adzagwera m’dzenje,+ ndipo aliyense wotuluka m’dzenjemo adzagwidwa mumsampha. Pakuti zotsekera madzi akumwamba zidzatseguka+ ndipo maziko a dziko adzagwedezeka.+ 19  Dzikolo lang’alukiratu, lagwedezekeratu, lili dzandidzandi.+ 20  Dzikolo likudzandira ngati munthu woledzera. Likugwedezekera uku ndi uku ngati chisimba.+ Zolakwa za dzikolo n’zolemera+ ndipo lidzagwa nazo osadzukanso.+ 21  M’tsiku limenelo Yehova adzakumbukira makamu akumwamba ndi mafumu a padziko lapansi.+ 22  Iwo adzasonkhanitsidwa ngati akaidi amene akuwasonkhanitsira m’dzenje.+ Adzatsekeredwa m’ndende,+ ndipo pakadzapita masiku ochuluka adzakumbukiridwanso.+ 23  Mwezi wathunthu wachita manyazi. Dzuwa lowala lachitanso manyazi,+ pakuti Yehova wa makamu wakhala mfumu+ yaulemerero m’phiri la Ziyoni+ ndi mu Yerusalemu, pamaso pa anthu ake achikulire.+

Mawu a M'munsi

Mwina kutanthauza chigawo cha kum’mawa kapena kudera lakutali.