Yesaya 55:1-13

55  Inu nonse amene mukumva ludzu,+ bwerani mudzamwe madzi.+ Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye.+ Inde bwerani mudzagule vinyo+ ndi mkaka+ popanda ndalama ndiponso popanda mtengo wake.+  N’chifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya, ndipo n’chifukwa chiyani mukuvutika kugwirira ntchito zinthu zimene sizikhutitsa?+ Tcherani khutu kwa ine kuti mudye zabwino,+ ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambiri ndi zakudya zamafuta.+  Tcherani khutu+ lanu ndipo bwerani kwa ine.+ Mvetserani ndipo mudzakhalabe ndi moyo.+ Ine ndidzachita nanu pangano lokhalapo mpaka kalekale+ lokhudza kukoma mtima kwanga kosatha kosonyezedwa kwa Davide, kumene kuli kokhulupirika.+  Taonani! Ine ndamupereka+ iye monga mboni+ kwa mitundu ya anthu,+ ndiponso monga mtsogoleri+ ndi wolamulira+ wa mitundu ya anthu.  Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,+ ndipo anthu a mtundu wosakudziwa adzathamangira kwa iwe+ chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ ndiponso chifukwa cha Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakukongoletsa.+  Anthu inu funafunani Yehova pamene iye akupezekabe.+ Muitaneni akadali pafupi.+  Munthu woipa asiye njira yake+ ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.+ Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+ Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.+  “Maganizo a anthu inu si maganizo anga,+ ndipo njira zanga si njira zanu,”+ akutero Yehova.  “Pakuti monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi,+ momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu,+ ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.+ 10  Pakuti monga momwe mvula ndi chipale chofewa zimagwera kuchokera kumwamba, osabwereranso kumeneko mpaka zitanyowetsa kwambiri nthaka n’kumeretsa zomera ndi kuzibereketsa,+ wobzala mbewu n’kupatsidwa zokolola komanso wakudya n’kupatsidwa chakudya,+ 11  ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+ 12  “Pakuti anthu inu mudzachoka ndi chisangalalo+ ndipo mudzafika ndi mtendere.+ Mapiri ndi zitunda zidzakusangalalirani ndi mfuu yachisangalalo,+ ndipo mitengo yonse yakutchire idzawomba m’manja.+ 13  M’malo mwa chitsamba chaminga padzamera mtengo wa mkungudza.+ M’malo mwa chomera choyabwa padzamera mtengo wa mchisu.+ Zimenezi zidzamutchukitsa Yehova,+ ndipo zidzakhala chizindikiro choti sichidzachotsedwa mpaka kalekale.”+

Mawu a M'munsi