Yesaya 7:1-25

7  Tsopano m’masiku a Ahazi mwana wa Yotamu mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda, Rezini+ mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anabwera ku Yerusalemu kudzachita nkhondo koma analephera kulanda mzindawo.+  Ndiyeno kunyumba ya Davide kunapita uthenga wakuti: “Dziko la Siriya layamba kudalira dziko la Efuraimu.”+ Choncho mtima wa Ahazi ndi wa anthu ake unayamba kunjenjemera, ngati mmene mitengo ya m’nkhalango imagwederera ndi mphepo.+  Tsopano Yehova anauza Yesaya kuti: “Pita ukakumane ndi Ahazi. Upite ndi mwana wako Seari-yasubu.*+ Ukakumane ndi Ahaziyo pamapeto pa ngalande+ yochokera kudziwe lakumtunda, m’mphepete mwa msewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+  Ukamuuze kuti, ‘Ganizira mofatsa zochita zako.+ Usatekeseke kapena kuchita mantha. Mtima wako usaope+ zikuni ziwiri zimene zikungofuka utsi, zomwe zatsala pang’ono kunyekeratu. Usaope mkwiyo waukulu wa Rezini mfumu ya Siriya ndiponso usaope mwana wa Remaliya,+  popeza Siriya ndi Efuraimu ndiponso mwana wa Remaliya akukonzera zoipa ndipo anena kuti:  “Tiyeni tikamenyane ndi dziko la Yuda. Tikalisakaze, tikalilande ndipo tikaligonjetse. Tikaike mfumu ina kuti izilamulira dzikolo. Mfumu yake ikhale mwana wa Tabeeli.”+  “‘Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sizitheka ndipo sizichitika.+  Pakuti mutu wa Siriya ndiwo Damasiko, ndipo mutu wa Damasiko ndiwo Rezini. Pakamatha zaka 65, Efuraimu adzakhala ataphwanyidwaphwanyidwa moti sadzakhalanso mtundu wa anthu.+  Mutu wa Efuraimu ndiwo Samariya,+ ndipo mutu wa Samariya ndiwo mwana wa Remaliya.+ Anthu inu mukakhala opanda chikhulupiriro, simukhalitsa.”’”+ 10  Yehova analankhulanso ndi Ahazi kuti: 11  “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako.+ Chikhoza kukhala chozama ngati Manda kapena chachitali ngati malo okwera.” 12  Koma Ahazi anati: “Sindipempha, ndipo sindimuyesa Yehova.” 13  Chotero mneneriyo anati: “Tamverani inu a nyumba ya Davide. Kodi mukuona ngati n’zazing’ono kuti muzitopetsa anthu, ndiponso kuti mutopetse Mulungu wanga?+ 14  Choncho Yehovayo akupatsani chizindikiro anthu inu: Tamverani! Mtsikana+ adzatenga pakati+ ndipo adzabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli. 15  Iye azidzadya mafuta a mkaka ndi uchi pofika nthawi imene adzadziwe kukana choipa ndi kusankha chabwino.+ 16  Mwanayo asanafike podziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino,+ nthaka ya mafumu awiri amene ukuchita nawo mantha ofika podwala nawowo, idzakhala itasiyidwiratu.+ 17  Yehova adzabweretsera iweyo,+ anthu ako, ndi nyumba ya bambo ako masiku amene sanakhaleponso kuyambira tsiku limene Efuraimu anapatukana ndi Yuda.+ Iye adzakubweretserani mfumu ya Asuri.+ 18  “M’tsiku limenelo, Yehova adzaimbira likhweru ntchentche zimene zili kumalekezero a ngalande za mtsinje wa Nailo wa ku Iguputo, ndi njuchi+ zimene zili m’dziko la Asuri.+ 19  Zinthu zimenezi zidzabwera zonse n’kutera m’zigwa* zokhala ndi maphompho, m’ming’alu ya m’matanthwe, patchire lonse lokhala ndi zitsamba zaminga, ndiponso pamalo onse omwetserapo ziweto.+ 20  “M’tsiku limenelo, pogwiritsira ntchito lezala lobwereka la kuchigawo cha ku Mtsinje,*+ pogwiritsira ntchito mfumu ya Asuri,+ Yehova adzameta tsitsi la kumutu ndi tsitsi la m’mapazi, ndipo lezalalo lidzachotseratu ngakhale ndevu.+ 21  “M’tsiku limenelo, munthu adzapulumutsa ng’ombe yaing’ono ndiponso nkhosa ziwiri.+ 22  Chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka, iye azidzadya mafuta a mkaka, popeza mafuta a mkaka ndi uchi+ n’zimene munthu aliyense wotsala m’dzikolo azidzadya. 23  “M’tsiku limenelo, pamalo alionse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000, yokwana ndalama zasiliva 1,000,+ padzakhala tchire la zitsamba zaminga ndi udzu.+ 24  Anthu azidzapita kumeneko atanyamula mivi ndi mauta,+ chifukwa m’dziko lonselo mudzamera tchire la zitsamba zaminga ndi udzu. 25  Kumapiri onse amene anthu anali kulambulako ndi makasu kuti achotse zomera zovutitsa, sadzapitakonso chifukwa choopa tchire la zitsamba zaminga ndi udzu. Malowo adzakhala odyetserako ng’ombe zamphongo ndi opondapondako nkhosa.”+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza kuti, “Otsala Ochepa (kapena, Otsala) Adzabwerera.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.