Yesaya 35:1-10

35  Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala.+ Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.+  Deralo lidzachitadi maluwa.+ Lidzasangalala ndipo lidzakondwera n’kufuula ndi chisangalalo.+ Lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni+ ndi kukongola kwa Karimeli+ ndiponso kwa Sharoni.+ Padzakhala anthu amene adzaone ulemerero wa Yehova+ ndi kukongola kwa Mulungu wathu.+  Anthu inu limbitsani manja ofooka ndiponso mawondo agwedegwede.+  Amene ali ndi nkhawa mumtima mwawo muwauze kuti:+ “Limbani mtima.+ Musachite mantha.+ Pakuti Mulungu wanu adzabwera n’kudzabwezera adani anu.+ Mulungu adzabwezera chilango.+ Iye adzabwera n’kukupulumutsani.”+  Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa,+ ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.+  Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.+ Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.+ Pakuti m’chipululu mudzatumphuka madzi ndipo m’dera lachipululu mudzayenda mitsinje.  Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi, ndipo malo aludzu adzakhala malo a akasupe amadzi.+ Kumalo okhala mimbulu,+ malo ake ousako, kudzakhala udzu wobiriwira, mabango ndi gumbwa.+  Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo.  Kumeneko sikudzakhala mkango ndipo nyama zolusa zakutchire sizidzafikako.+ Nyama zotere sizidzapezekako.+ Anthu ogulidwanso adzayenda mumsewuwo.+ 10  Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+

Mawu a M'munsi