Yesaya 46:1-13

46  Beli+ wawerama+ ndipo Nebo wagwada. Mafano awo+ akhala katundu wa nyama zakutchire ndi wa nyama zoweta. Mafanowo angokhala katundu wolemera kwa nyama zotopa.  Milungu imeneyi idzawerama, ndipo yonse pamodzi idzagwada pansi. Singapulumutse zifaniziro zawo+ zimene zanyamulidwa ngati katundu, koma idzatengedwa kupita ku ukapolo.+  “Inu a nyumba ya Yakobo ndimvetsereni. Ndimvetsereni inu nonse otsala a m’nyumba ya Isiraeli,+ inu amene ndinakunyamulani kuyambira pamene munabadwa, ndiponso inu amene ndinakusamalirani kuyambira pamene munatuluka m’mimba.+  Ine sindisintha ngakhale kwa wokalamba,+ ndipo munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.+ Ndithu ineyo ndidzachitapo kanthu+ kuti ndiwatenge, ndiwanyamule ndi kuwapulumutsa.+  “Kodi anthu inu mungandifanizire ndi ndani,+ kapena mungandiyerekezere ndi ndani?+  Pali anthu amene amakhuthula golide m’zikwama, ndi kuyeza siliva pasikelo. Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo iye amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+ Kenako anthuwo amayamba kuweramira ndi kugwadira mulunguyo.+  Iwo amamunyamula pamapewa awo.+ Amamutenga n’kukamuika pamalo ake ndi kumuimika bwinobwino. Mulunguyo sayenda kuchoka pamalo akewo.+ Ngakhale munthu atamufuulira, iye sayankha. Sapulumutsa munthu kumavuto ake.+  “Anthu inu kumbukirani izi kuti mulimbe mtima. Muziganizire mumtima mwanu,+ inu anthu ochimwa.+  Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,+ kuti ine ndine Mulungu+ ndipo palibenso Mulungu wina,+ kapena aliyense wofanana ndi ine.+ 10  Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+ 11  Ine ndi amene ndidzaitane mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa.+ Ndidzaitana munthu kuti adzachite zolingalira zanga kuchokera kutali.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.+ Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.+ 12  “Tamverani inu anthu osamva,+ inu anthu amene muli kutali ndi chilungamo.+ 13  Ine ndabweretsa pafupi chilungamo changa.+ Chilungamocho sichili kutali,+ ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa.+ Ndidzapereka chipulumutso mu Ziyoni, ndipo Isiraeli ndidzam’patsa kukongola kwanga.”+

Mawu a M'munsi