Yesaya 16:1-14

16  Anthu inu, tumizani nkhosa yamphongo kwa wolamulira wa dziko.+ Muitumize kuchokera ku Sela kudutsa kuchipululu mpaka kukafika kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.+  Pamalo owolokera chigwa cha Arinoni,+ ana aakazi a Mowabu adzakhala ngati mbalame yomwe ikuthawa, itathamangitsidwa pachisa chake.+  “Anthu inu, perekani malangizo. Chitani zimene zagamulidwa.+ “Chititsani kuti masana, mthunzi wanu uphimbe malo aakulu ndiponso uchititse mdima ngati wa usiku.+ Bisani anthu obalalika.+ Musaulule aliyense amene akuthawa.+  Anthu anga obalalika akhale ngati alendo mwa iwe Mowabu.+ Iwo abisale mwa iwe pothawa wolanda,+ pakuti wopondereza anthu wafika pamapeto ake. Kulanda kwatha. Opondaponda anzawo atha padziko lapansi.+  “Mpando wachifumu ndithu udzakhazikika ndi kukoma mtima kosatha.+ Mfumu idzakhala pampandowo n’kumalamulira mokhulupirika muhema wa Davide.+ Izidzaweruza n’kumafunafuna chilungamo, ndipo izidzachita mwachangu zinthu zoyenera.”+  Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, kuti ndi wonyada kwambiri.+ Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, ndi mkwiyo wake.+ Zolankhula zake zodzitukumula sizidzachitika.+  Chotero Mowabu adzalira mofuula chifukwa cha tsoka lake. Aliyense wokhala m’Mowabu ndithu adzalira mofuula.+ Omenyedwawo adzalirira mphesa zouma zoumba pamodzi za ku Kiri-hareseti,+  chifukwa minda ya m’mapiri ya ku Hesiboni+ yafota. Eni ake a mitundu ya anthu athyola nthambi za mitengo ya mpesa ya ku Sibima+ zodzaza ndi mphesa zakupsa. Nthambizo zinafika mpaka ku Yazeri.+ Zinafika mpaka kuchipululu. Mphukira zake zinasiyidwa kuti zizingodzikulira pazokha. Zinafika mpaka kunyanja.  N’chifukwa chake ndidzalirire mtengo wa mpesa wa ku Sibima ngati mmene ndinachitira polirira Yazeri.+ Ndidzakunyowetsa kwambiri ndi misozi yanga iwe Hesiboni+ ndi Eleyale,+ chifukwa chakuti kufuula kwakugwera m’chilimwe ndi pa nthawi ya zokolola zako.+ 10  Kukondwera ndi kusangalala zachotsedwa m’munda wako wa zipatso, ndipo m’minda ya mpesa mulibe mfuu yachisangalalo. Mulibe aliyense amene akufuula.+ Mopondera mphesa mulibe amene akuponda vinyo.+ Ndachititsa kuti kufuula kulekeke.+ 11  N’chifukwa chake mkati mwanga mukunjenjemera ngati zingwe za zeze chifukwa cha Mowabu,+ ndipo m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha Kiri-hareseti.+ 12  Kenako zinaoneka kuti Mowabu anatopa pamalo okwezeka,+ ndipo anapita kumalo opatulika kukapemphera+ koma sizinathandize.+ 13  Awa ndi mawu okhudza Mowabu amene Yehova ananena kalekale. 14  Koma tsopano Yehova wanena kuti: “Pomatha ndendende zaka zitatu,*+ ulemerero+ wa Mowabu udzatha. Iye adzachititsidwa manyazi ndipo adzakumana ndi chipwirikiti chamtundu uliwonse. Otsala mwa iye adzakhala ochepa kwambiri ndiponso opanda mphamvu.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Pomatha zaka zitatu, malinga ndi zaka za munthu waganyu.” Nthawi imene munthu waganyu anali kugwira ntchito sanali kuiwonjezera kapena kuichepetsa. Chotero, izi zikutanthauza kuti nthawi ya kutha kwa ulemerero wa Mowabu inali yosasinthika.