Yesaya 44:1-28

44  “Tsopano mvetsera, iwe Yakobo mtumiki wanga,+ ndi iwe Isiraeli amene ndakusankha.+  Yehova, amene anakupanga+ ndiponso amene anakuumba,+ amene anali kukuthandiza ngakhale pamene unali m’mimba,+ wanena kuti, ‘Usachite mantha,+ iwe mtumiki wanga Yakobo, ndiponso iwe Yesuruni,+ amene ndakusankha.  Pakuti ndidzapatsa madzi munthu waludzu,+ ndipo ndidzaika timitsinje tamadzi pamalo ouma.+ Ndidzatsanulira mzimu wanga pambewu yako+ ndi madalitso anga pa mbadwa zako.  Iwo adzaphuka ngati udzu wobiriwira,+ ndiponso ngati mitengo ya msondodzi+ m’mphepete mwa ngalande zamadzi.  Uyu adzati: “Ine ndine wa Yehova.”+ Uyo adzadzitcha dzina la Yakobo,+ ndipo wina adzalemba padzanja lake kuti: “Wa Yehova.” Munthu winanso adzadzipatsa dzina la Isiraeli.’+  “Yehova, Mfumu ya Isiraeli,+ Womuwombola iye,+ Yehova wa makamu, wanena kuti: ‘Ine ndine woyamba ndi womaliza,+ ndipo palibenso Mulungu kupatulapo ine.+  Ndani ali ngati ine?+ Ayankhe molimba mtima kuti apereke umboni wake kwa ine.+ Monga momwe ine ndachitira kuyambira nthawi imene ndinakhazikitsa anthu akalekale,+ iwo anene zinthu zimene zichitike posachedwa ndi zimene zidzachitike m’tsogolo.  Anthu inu musachite mantha ndipo musathedwe nzeru.+ Kodi sindinachititse aliyense wa inu kuti amve kuyambira nthawi imeneyo? Kodi sindinakuuzeni zimenezi?+ Inu ndinu mboni zanga.+ Kodi palinso Mulungu kupatulapo ine?+ Ayi, palibe Thanthwe.+ Sindikudziwapo aliyense.’”  Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,+ ndipo mafano awo okondedwa adzakhala opanda phindu.+ Monga mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+ kuti anthu opanga mafanowo achite manyazi.+ 10  Kwa aliyense amene wapanga mulungu kapena kuumba fano lopangidwa ndi chitsulo chosungunula,+ lidzakhala lopanda phindu ngakhale pang’ono.+ 11  Anzake onse adzachita manyazi,+ ndipotu amisiriwo ndi anthu ochokera kufumbi. Onsewo adzasonkhana pamodzi.+ Adzaima chilili. Adzachita mantha. Onsewo adzachitira limodzi manyazi.+ 12  Munthu wogoba zitsulo ndi chogobera watentha chitsulocho ndi makala amoto. Wachiwongola ndi nyundo, ndipo wakhala ali jijirijijiri kuchiumba ndi dzanja lake lamphamvu.+ Wamva njala ndipo alibe mphamvu. Sanamwe madzi, chotero watopa. 13  Mmisiri wosema mtengo watambasula chingwe choyezera. Waulemba ndi choko chofiira. Wausema ndi sompho ndipo waulemberera ndi chida cholembera mizere yozungulira. Pang’ono ndi pang’ono waupanga kuti uzioneka ngati munthu,+ ngati kukongola kwa anthu, kuti uzikhala m’nyumba.+ 14  Pali munthu amene ntchito yake ndi yogwetsa mitengo ya mkungudza. Iye amasankha mtengo wamtundu winawake, waukulu kwambiri, n’kuusiya kuti ukule n’kukhwima pakati pa mitengo ya m’nkhalango.+ Iye anabzala mtengo wa paini, ndipo mvula yaukulitsa kwambiri. 15  Tsopano mtengowo wafika poti munthu akhoza kuusandutsa nkhuni. Chotero iye watenga mbali ya mtengowo kuti asonkhere moto woti aziwotha. Wayatsa motowo n’kuphikapo mkate. Wasemanso mulungu woti azimugwadira.+ Mtengowo waupanga chifaniziro chosema+ ndipo akuchigwadira n’kumachilambira. 16  Hafu ya mtengowo waitentha pamoto. Hafu ina ya mtengowo wawotchera nyama imene wadya, ndipo wakhuta. Wawothanso moto wake ndipo wanena kuti: “Eya! Ndafundidwa. Ndaona kuwala kwa moto.” 17  Koma mtengo wotsalawo wapangira mulungu, wapangira chifaniziro chake chosema. Wachiweramira ndi kuchigwadira n’kumapemphera pamaso pake kuti: “Ndipulumutseni, pakuti ndinu mulungu wanga.”+ 18  Iwo sadziwa chilichonse+ ndipo samvetsetsa chilichonse+ chifukwa maso awo amatidwa kuti asamaone,+ ndipo mitima yawo ndi yosazindikira zinthu.+ 19  Palibe amene akuganiza mumtima mwake+ kapena amene akudziwa zinthu, kapenanso amene ali womvetsa zinthu+ kuti adzifunse kuti: “Hafu ya mtengowu ndasonkhera moto ndipo pamakala ake ndaphikapo mkate. Ndawotchanso nyama n’kudya. Koma kodi wotsalawu ndipangire chinthu chonyansa?+ Kodi zoona ndiweramire mtengo woumawu?” 20  Iye akudya phulusa.+ Mtima wake umene wanyengedwa wamusocheretsa.+ Iye sakupulumutsa moyo wake kapena kunena kuti: “Kodi chinthu chimene chili m’dzanja langa lamanjachi si chonyenga?”+ 21  “Kumbukira zinthu zimenezi iwe Yakobo,+ ndiponso iwe Isiraeli, pakuti ndiwe mtumiki wanga.+ Ine ndiye amene ndinakuumba.+ Iweyo ndiwe mtumiki wanga. Iwe Isiraeli, ine sindikuiwala.+ 22  Ndidzafafaniza zolakwa zako ngati kuti ndaziphimba ndi mtambo,+ ndi machimo ako ngati kuti ndawaphimba ndi mitambo yambiri. Bwerera kwa ine,+ ndipo ine ndikuwombola.+ 23  “Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ pakuti Yehova wachitapo kanthu.+ Fuulani mosangalala,+ inu malo otsika kwambiri a dziko lapansi.+ Mapiri+ inu ndiponso iwe nkhalango ndi inu mitengo yonse ili mmenemo, kondwani ndi kufuula ndi chisangalalo. Pakuti Yehova wawombola Yakobo ndipo wasonyeza kukongola kwake pa Isiraeli.”+ 24  Yehova, Wokuwombola+ ndiponso amene anakuumba kuyambira uli m’mimba, wanena kuti: “Ine Yehova ndachita zonse. Ndinatambasula ndekha kumwamba,+ ndi kukhazikitsa dziko lapansi.+ Kodi ndani anali nane? 25  Ndimalepheretsa zizindikiro za anthu olankhula zinthu zopanda pake, ndipo ndine amene ndimachititsa olosera kuchita zamisala.+ Ndine amene ndimachititsa anthu anzeru kubwerera kumbuyo, ndiponso amene ndimachititsa nzeru zawo kukhala zopusa.+ 26  Ndine amene ndimachititsa mawu a mtumiki wanga kukwaniritsidwa ndiponso amene ndimakwaniritsa mawu onse amene atumiki anga analengeza.+ Ndine amene ndikunena za Yerusalemu kuti, ‘Muzidzakhala anthu.’+ Ndikunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti, ‘Idzamangidwanso,+ ndipo malo ake osakazidwa ndidzawamanganso.’+ 27  Ndine amene ndikuuza madzi akuya kuti, ‘Iphwa ndipo mitsinje yako yonse ndidzaiumitsa.’+ 28  Ndine amene ndikunena za Koresi+ kuti, ‘Iye ndi m’busa wanga ndipo adzakwaniritsa bwinobwino zonse zimene ndikufuna,’+ ngakhale zimene ndanena zokhudza Yerusalemu zakuti, ‘Adzamangidwanso,’ ndi zokhudza kachisi zakuti, ‘Maziko ako adzamangidwa.’”+

Mawu a M'munsi