Yesaya 28:1-29

28  Tsoka kwa chisoti chaulemerero cha zidakwa za ku Efuraimu!+ Chisoticho changokhala ngati nkhata yamaluwa yokongola, imene maluwa ake akufota. Nkhata yamaluwayo yavalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde, kumene zidakwa zoledzera ndi vinyozo zimakhala.  Taonani! Yehova ali ndi winawake wamphamvu ndi wanyonga.+ Monga mvula yamabingu ndi yamatalala,+ mvula yamphepo yowononga, ndiponso monga mvula yamabingu ya madzi amphamvu osefukira,+ iye adzagwetsera pansi chisoti chaulemererocho mwamphamvu.  Zisoti zaulemerero za zidakwa za ku Efuraimu, zidzapondedwapondedwa ndi mapazi.+  Nkhata yamaluwa yokongola imene maluwa ake akufota,+ yomwe ili pamwamba pa phiri m’chigwa chachonde, idzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kucha+ chilimwe chisanafike, imene munthu akaiona amaithyola n’kuimeza msangamsanga.  M’tsiku limenelo, Yehova wa makamu adzakhala ngati chisoti chokongoletsera+ ndiponso ngati nkhata yamaluwa yokongola+ kwa anthu ake otsala.+  Adzakhalanso ngati mzimu wa chilungamo kwa munthu wopereka chiweruzo,+ ndiponso adzakhala ngati mphamvu kwa anthu opitikitsa adani amene afika pachipata kudzamenyana nawo.+  Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Ansembe ndi aneneri+ asochera chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Asokonezeka chifukwa cha vinyo. Akuyenda uku ndi uku+ chifukwa cha chakumwa choledzeretsa. Sakuonanso bwino ndipo zochita zawo zikusonyeza kuti sakuganiza bwino.  Pakuti matebulo onse adzaza masanzi.+ Paliponse pali masanzi okhaokha.  Kodi iyeyo akufuna aphunzitse ndani kudziwa zinthu,+ ndipo akufuna achititse ndani kumvetsetsa uthenga umene wanenedwa?+ Kodi ifeyo akutiyesa ana amene asiya kuyamwa, amene achotsedwa kubere?+ 10  Pakuti ndi “lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo, chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera, apa pang’ono, apo pang’ono.”*+ 11  Pakuti iye adzalankhula kwa anthu awa kudzera mwa anthu achibwibwi+ ndiponso olankhula lilime lachilendo,+ 12  anthu amene wawauza kuti: “Awa ndiye malo opumira. Pumitsani munthu wotopa. Amenewa ndiwo malo ampumulo,” koma amene sanafune kumva.+ 13  Kwa iwowo mawu a Yehova adzakhaladi “lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo, chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera,+ apa pang’ono, apo pang’ono,” kuti akagwe chagada n’kuthyoka, kukodwa ndi kugwidwa.+ 14  Chotero imvani mawu a Yehova inu anthu odzitama, inu atsogoleri+ a anthu awa amene muli mu Yerusalemu: 15  Pakuti anthu inu mwanena kuti: “Ife tachita pangano ndi Imfa.+ Taona masomphenya limodzi ndi Manda.+ Ngati madzi osefukira atadutsa kuno, safika kwa ife pakuti bodza talisandutsa pothawirapo pathu,+ ndiponso tabisala m’chinyengo.”+ 16  Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikuika mwala mu Ziyoni+ kuti ukhale maziko. Umenewu ndi mwala+ wapakona woyesedwa,+ wamtengo wapatali,+ woti ukhale maziko olimba.+ Palibe munthu woukhulupirira amene adzade nkhawa.+ 17  Chilungamo+ ndidzachisandutsa chingwe choyezera+ ndipo ndidzachisandutsanso chipangizo chowongolera.* Mvula yamatalala+ idzakokolola malo othawirapo abodza + ndipo madzi adzasefukira pamalo obisalako.+ 18  Pangano lanu limene mwachita ndi Imfa lidzatha,+ ndipo masomphenya anu amene mwaona ndi Manda sadzagwira ntchito.+ Madzi osefukira akadzadutsa+ adzakukokololani.+ 19  Nthawi iliyonse imene akudutsa, azidzakutengani anthu inu+ chifukwa azidzadutsa m’mawa uliwonse. Azidzadutsanso usana ndi usiku ndipo adzangokhala chinthu chonjenjemeretsa,+ kuti ena amvetse uthenga umene wanenedwa.” 20  Pakuti bedi lafupika kwambiri moti munthu sangathe kugonapo mowongoka bwinobwino, ndipo nsalu yofunda yachepa kwambiri moti sikukwanira kuti munthu afunde bwinobwino. 21  Yehova adzaimirira monga mmene anachitira paphiri la Perazimu.+ Adzakalipa ngati mmene anachitira m’chigwa cha kufupi ndi Gibeoni+ kuti achite ntchito yake. Ntchito yakeyo ndi yodabwitsa. Adzakalipa kuti achite zochita zake. Zochita zakezo n’zachilendo.+ 22  Tsopano musakhale anthu onyoza+ chifukwa zingwe zanu zingakhale zolimba, pakuti ndamva kuchokera kwa Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ kuti dziko lonse laweruzidwa kuti liwonongedwe.+ 23  Anthu inu tcherani khutu ndipo mvetserani mawu anga. Khalani tcheru ndipo mverani zonena zanga. 24  Kodi wolima munda ndi pulawo amangokhalira kulima nthawi zonse,+ kuphwanya zibuma, ndi kusalaza dothi, osabzala mbewu?+ 25  Kodi iye akasalaza dothilo si paja amawazapo chitowe chakuda ndiponso amafesapo chitowe chamtundu wina?+ Kodi si paja amabzalanso tirigu, mapira+ ndi balere m’malo ake,+ ndipo m’mphepete mwa mundawo+ amabzalamo mbewu zinanso?*+ 26  Mulungu amalangiza+ munthu moyenerera ndipo amam’phunzitsa.+ 27  Pakuti anthu sapuntha chitowe chakuda ndi chida chopunthira+ ndipo pachitowe chamtundu wina sayendetsapo mawilo a ngolo yopunthira mbewu. Nthawi zambiri chitowe chakuda amachipuntha ndi ndodo+ ndipo chitowe chamtundu wina amachipuntha ndi kamtengo. 28  Kodi tirigu amene ali popunthira mbewu, amamuphwanya? Munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo mosalekeza.+ Iye amayendetsa magudumu ake opunthira, ndi mahatchi ake, koma saphwanya tiriguyo.+ 29  Izi zachokeranso kwa Yehova wa makamu+ amene zolinga zake ndi zabwino kwambiri, ndiponso amene wachita zopambana kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Pa Chiheberi vesi limeneli lili ngati kandakatulo kobwerezabwereza, kokhala ngati kanyimbo ka ana.
Chimenechi chinali chipangizo chimene anali kuchigwiritsa ntchito pofuna kuonetsetsa kuti pamalo pakhale pa fulati.
Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “mbewu zinanso” akutanthauza mtundu wa tirigu wosakoma kwenikweni umene unali kulimidwa ku Iguputo kale.