Yesaya 25:1-12

25  Inu Yehova, ndinu Mulungu wanga.+ Ndikukukwezani+ ndi kutamanda dzina lanu+ chifukwa mwachita zinthu zabwino kwambiri.+ Mwakwaniritsa zolinga zanu+ zakalekale ndipo mwachita zinthu mokhulupirika+ ndi modalirika.+  Mwasandutsa mzinda kukhala mulu wamiyala ndipo mudzi wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mwausandutsa bwinja logumukagumuka. Mzinda wa chitetezo champhamvu wa anthu achilendo mwauthetsa ndipo sudzamangidwanso mpaka kalekale.+  N’chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani. Mudzi wa mitundu yankhanza udzakuopani.+  Pakuti inu mwakhala malo achitetezo kwa munthu wonyozeka ndiponso malo achitetezo kwa munthu wosauka m’masautso ake.+ Mwakhala malo ousapo mvula yamkuntho ndi mthunzi+ wobisalirapo kutentha kwa dzuwa. Mwakhala wotero pamene anthu ankhanza akuwomba anzawo ngati mvula yamkuntho yowomba khoma.  Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsera kutentha m’dziko lopanda madzi, inu mumachepetsa phokoso la alendo.+ Nayonso nyimbo ya anthu ankhanza yaletsedwa.+  Yehova wa makamu adzakonzera anthu a mitundu yonse+ m’phiri ili,+ phwando la zakudya zabwinozabwino,+ phwando la vinyo wokoma kwambiri,* phwando la zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta a m’mafupa,+ ndiponso la vinyo+ wokoma kwambiri, wosefedwa bwino.+  M’phiri limeneli iye adzameza chophimba chimene chikuphimba anthu onse,+ ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse.  Iye adzameza imfa kwamuyaya+ ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.+ Adzachotsa kunyozeka kwa anthu ake padziko lonse lapansi,+ pakuti Yehova ndiye wanena zimenezi.  M’tsiku limenelo munthu adzati: “Taonani! Uyu ndiye Mulungu wathu.+ Chiyembekezo chathu chinali mwa iye+ ndipo iye watipulumutsa.+ Uyu ndi Yehova.+ Chiyembekezo chathu chinali mwa iye. Tiyeni tisangalale ndi kukondwera ndi chipulumutso chochokera kwa iye.”+ 10  Pakuti dzanja la Yehova lidzakhazikika paphiri limeneli,+ ndipo Mowabu adzapondedwapondedwa+ pamalo pake ngati mulu wa udzu umene umapondedwapondedwa pamalo opangira manyowa.+ 11  Iye adzatambasula manja ake n’kuwamenyetsa pakati pa mzindawo ngati mmene munthu wosambira amatambasulira manja ake n’kuwamenyetsa pamadzi akamasambira. Adzathetsa kunyada+ kwa mzindawo poumenya mwaluso ndi manja ake. 12  Iye adzagwetsa mzinda wokhala ndi mipanda yachitetezo italiitali yolimba kwambiri. Adzautsitsa n’kuugwetsera pansi, pafumbi.+

Mawu a M'munsi

Kapena, “vinyo yemwe nsenga zake zadikha pansi chifukwa chokhalitsa.”