Yesaya 61:1-11

61  Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+ pakuti Yehova wandidzoza+ kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+ Wandituma kuti ndikamange zilonda za anthu osweka mtima,+ ndikalengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+ ndiponso ndikatsegule maso a akaidi.+  Wandituma kuti ndikalengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,+ ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu.+ Wanditumanso kuti ndikatonthoze anthu onse olira,+  ndiponso kuti anthu onse amene akulirira Ziyoni ndiwapatse nsalu yovala kumutu m’malo mwa phulusa,+ ndiwapatse mafuta kuti azisangalala+ m’malo molira, ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda m’malo mokhala otaya mtima.+ Iwo adzatchedwa mitengo ikuluikulu ya chilungamo,+ yobzalidwa ndi Yehova+ kuti iyeyo akongole.+  Iwo adzamanganso malo amene akhala owonongeka kwa nthawi yaitali.+ Adzamanga malo amene anasakazidwa kalekale.+ Adzakonzanso mizinda yowonongedwa,+ malo amene akhala osakazidwa ku mibadwomibadwo.  “Alendo adzabwera n’kumaweta ziweto zanu.+ Anthu ochokera kwina+ adzakhala olima minda yanu ndi osamalira minda yanu ya mpesa.+  Inuyo mudzatchedwa ansembe a Yehova.+ Anthu adzakutchani atumiki+ a Mulungu wathu.+ Mudzadya zinthu zochokera ku mitundu ya anthu+ ndiponso mudzalankhula za inuyo mokondwera, chifukwa cha chuma ndi ulemerero zimene mudzapeze kwa mitunduyo.+  M’malo mwa manyazi, mudzalandira zinthu zochuluka kuwirikiza kawiri,+ ndipo m’malo mochita manyazi, anthu anga adzafuula ndi chisangalalo chifukwa cha gawo lawo.+ Iwo adzakhala ndi gawo lowirikiza kawiri m’dziko lawo,+ ndipo adzasangalala mpaka kalekale.+  Pakuti ine Yehova ndimakonda chilungamo.+ Ndimadana ndi zauchifwamba ndi kupanda chilungamo.+ Ndidzawapatsa malipiro awo mokhulupirika,+ ndipo ndidzachita nawo pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale.+  Ana awo adzadziwika pakati pa mitundu ya anthu,+ ndipo mbadwa zawo zidzadziwika pakati pa anthu osiyanasiyana. Onse owaona adzazindikira+ kuti iwo ndi ana odalitsidwa ndi Yehova.”+ 10  Ndithu ine ndidzakondwera mwa Yehova.+ Moyo wanga udzasangalala ndi Mulungu wanga.+ Pakuti iye wandiveka zovala zachipulumutso.+ Wandiveka malaya akunja achilungamo odula manja,+ ngati mkwati amene wavala chovala chakumutu mofanana ndi wansembe,+ ndiponso ngati mkwatibwi amene wavala zinthu zake zodzikongoletsera.+ 11  Pakuti monga momwe dziko lapansi limatulutsira zomera zake, ndiponso monga momwe munda umameretsera zinthu zimene zabzalidwa mmenemo,+ momwemonso Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzameretsa chilungamo+ ndi chitamando pamaso pa mitundu yonse.+

Mawu a M'munsi