Yesaya 42:1-25

42  Taonani mtumiki wanga+ amene ndamugwiritsitsa,+ amene ndamusankha,+ ndiponso amene moyo wanga ukukondwera naye.+ Ine ndaika mzimu wanga mwa iye,+ ndipo iye adzabweretsa chilungamo kwa anthu a mitundu ina.+  Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.+  Bango lophwanyika sadzalithyola,+ ndipo chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima sadzachizimitsa. Iyeyo adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.+  Iye sadzatsala pang’ono kuzima kapena kuphwanyidwa mpaka atakhazikitsa chilungamo padziko lapansi.+ Zilumba zidzadikirira lamulo lake.+  Mulungu woona Yehova, amene analenga kumwamba+ ndiponso Wokutambasula Wamkulu,+ amene anakhazikitsa dziko lapansi+ ndi zonse zimene zili mmenemo,+ amene anapereka mpweya+ kwa anthu amene ali mmenemo,+ ndi mzimu kwa anthu amene amayenda padzikopo,+ iye wanena kuti:  “Ineyo Yehova pochita zinthu mwachilungamo, ndinakuitana+ ndipo ndinakugwira dzanja.+ Ndidzakuteteza ndiponso ndidzakupereka monga pangano kwa anthu+ ngati kuwala kwa mitundu ya anthu,+  kuti ukatsegule maso a akhungu,+ ukatulutse mkaidi m’ndende ya mdima+ ndiponso kuti ukatulutse m’ndende anthu amene ali mu mdima.+  “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli,+ ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense+ kapena kupereka ulemerero wanga+ kwa zifaniziro zogoba.+  “Zinthu zoyamba zachitika,+ koma ndikukuuzani zinthu zatsopano. Zisanayambe kuonekera, ndimakuuzani.”+ 10  Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+ M’tamandeni kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ M’tamandeni inu amuna amene mumadalira nyanja+ ndi zonse zokhala mmenemo, ndiponso inu zilumba ndi anthu okhala m’zilumbazo.+ 11  Chipululu+ ndi mizinda ya kumeneko, ndiponso midzi ya ku Kedara zikweze mawu awo.+ Anthu okhala m’dera lamatanthwe+ afuule mokondwera. Anthu afuule kuchokera pamwamba pa mapiri. 12  Anthu am’patse Yehova ulemerero,+ ndipo anthu a m’zilumba anene za ulemerero wake.+ 13  Yehova adzanyamuka ngati munthu wamphamvu.+ Ngati wankhondo, iye adzachita zinthu modzipereka kwambiri.+ Iye adzafuula, ndithu adzafuula mfuu yankhondo,+ ndipo adzakhala wamphamvu kuposa adani ake.+ 14  “Ndakhala phee kwa nthawi yaitali.+ Ndinangokhala chete.+ Ndakhala ndikudziletsa.+ Tsopano ndibuula, ndipuma movutikira, ndipo ndipuma mwawefuwefu pa nthawi imodzimodziyo, ngati mkazi amene akubereka.+ 15  Ndidzawononga+ mapiri ndi zitunda. Ndidzaumitsa zinthu zonse zimene zinamera mmenemo. Mitsinje ndidzaisandutsa zilumba ndipo madambo ndidzawaumitsa.+ 16  Anthu akhungu ndidzawayendetsa m’njira imene sakuidziwa.+ Ndidzawadutsitsa mumsewu umene sakuudziwa.+ Malo amdima ndidzawasandutsa kuwala pamaso pawo,+ ndipo malo okumbikakumbika ndidzawasalaza.+ Zimenezi ndi zimene ndidzawachitire ndipo sindidzawasiya.”+ 17  Anthu amene akudalira zifaniziro zosema, amene akuuza zifaniziro zopangidwa ndi chitsulo chosungunula kuti: “Ndinu milungu yathu,” adzathawa ndipo adzachita manyazi kwambiri.+ 18  Inu ogontha imvani. Inu akhungu yang’anani kuti muone.+ 19  Ndani amene ali wakhungu? Mtumiki wanga ndiye wakhungu. Ndani amene ali wogontha ngati mtumiki wanga amene ndamutuma? Ndani amene ali wakhungu ngati munthu amene wapatsidwa mphoto, kapena amene ali wakhungu ngati mtumiki wa Yehova?+ 20  Iwe waona zinthu zambiri, koma sunachitepo kanthu.+ Makutu ako akhala ali otseguka koma sunamvetsere.+ 21  Chifukwa cha chilungamo chake,+ Yehova walemekeza ndi kukweza malamulo ake mokondwera.+ 22  Koma anthu amenewa agwidwa ndipo atengedwa.+ Onsewa anagwera m’maenje ndipo akhala akubisidwa m’ndende.+ Atengedwa popanda wowalanditsa.+ Agwidwa popanda wonena kuti: “Bwererani nawo!” 23  Ndani pakati panu amene adzamvetsere zinthu zimenezi? Ndani adzatchere khutu ndi kumvetsera zinthu zimene zidzamuthandize m’tsogolo?+ 24  Ndani wachititsa kuti Yakobo angokhala zofunkha ndiponso kupereka Isiraeli kwa anthu olanda? Kodi si Yehova amene iwo am’chimwira, amene sanafune kuyenda m’njira zake ndipo sanasunge malamulo ake?+ 25  Choncho Mulungu anali kuwakhuthulira mkwiyo, ukali wake, ndi nkhondo yoopsa.+ Nkhondoyo inali kuwapsereza+ koma iwo sanazindikire.+ Inapitiriza kuwatentha koma iwo sanaganizire chilichonse mumtima mwawo.+

Mawu a M'munsi