Yesaya 9:1-21

9  Komabe mdima wake sudzakhala ngati wa pa nthawi imene dzikolo linali m’masautso, ngati kale pamene anthu ankanyoza dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali.+ Koma patsogolo pake anthu analilemekeza dzikolo,+ dera limene kuli njira ya m’mphepete mwa nyanja, m’chigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.+  Anthu amene anali kuyenda mu mdima, aona kuwala kwakukulu.+ Anthu amene anali kukhala m’dziko la mdima wandiweyani,+ kuwala kwawawalira.+  Mwachulukitsa mtundu,+ mwaupangitsa kusangalala kwambiri.+ Iwo asangalala pamaso panu ngati mmene amasangalalira pa nthawi yokolola,+ ngati anthu amene amasangalala akamagawana katundu amene alanda.+  Pakuti goli la katundu wawo,+ ndodo yomwe inali pamapewa awo, ndiponso ndodo ya amene anali kuwakusira ku ntchito,+ mwazithyolathyola ngati pa tsiku limene Amidiyani anagonjetsedwa.+  Nsapato iliyonse ya munthu woyenda mwamgugu+ ndi chovala choviikidwa m’magazi, zakhala zoyenera kutenthedwa pamoto ngati nkhuni.+  Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+  Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+  Yehova anatumiza mawu otsutsana ndi Yakobo, ndipo mawuwo anafikira Isiraeli.+  Mawu onsewa anthu adzawadziwa.+ Efuraimu ndi anthu okhala ku Samariya,+ adzawadziwa mawuwo chifukwa cha kudzikweza kwawo ndiponso chifukwa cha mwano wa mumtima mwawo. Pakuti iwo anena kuti:+ 10  “Nyumba za njerwa n’zimene zagwazi, koma ife timanga zina za miyala yosema.+ Mitengo ya mkuyu ndi imene yathyoledwayi, koma m’malo mwake ife tipezerapo mitengo ya mkungudza.”+ 11  Yehova adzakweza adani a Rezini pamwamba kwambiri kuti alimbane naye, ndipo adzalimbikitsa adani a Isiraeli.+ 12  Siriya adzachokera kum’mawa+ ndipo Afilisiti adzachokera kumadzulo.+ Iwo adzadya Isiraeli ndi pakamwa potsegula.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+ 13  Anthuwo sanabwerere kwa amene akuwamenya+ ndipo sanafunefune Yehova wa makamu,+ 14  chotero Yehova adzadula mutu+ ndi mchira+ wa Isiraeli. Adzadulanso mphukira ndi udzu* tsiku limodzi.+ 15  Munthu wokalamba ndi wolemekezeka kwambiri ndiye mutu,+ ndipo mneneri wopereka malangizo abodza ndiye mchira.+ 16  Amene akutsogolera anthuwa ndiwo amene akuwasocheretsa,+ ndipo amene akutsogoleredwawo ndiwo amene akusokonezedwa.+ 17  N’chifukwa chake Yehova sadzasangalalira ngakhale anyamata awo,+ ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye* ndi akazi awo amasiye, pakuti onsewo ndi opanduka+ ndi ochita zoipa ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru. Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+ 18  Pakuti kuipa kwayaka ngati moto,+ ndipo kudzanyeketsa zitsamba zaminga ndi udzu.+ Kuipako kudzayaka m’zitsamba zowirira za m’nkhalango,+ ndipo utsi wa mitengoyo udzakwera m’mwamba kuti tolo!+ 19  Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova wa makamu, dzikolo layaka moto ndipo anthu adzakhala ngati chakudya cha motowo.+ Palibe amene adzamvere chisoni aliyense, ngakhale m’bale wake.+ 20  Munthu adzacheka kumbali yake yakumanja, koma adzakhala ndi njala. Adzadya kumanzere kwake, koma sadzakhuta.+ Aliyense adzadya mnofu wa dzanja lake.+ 21  Manase adzadya Efuraimu ndipo Efuraimu adzadya Manase. Awiriwa adzaukira Yuda pamodzi.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “mlulu.”
Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”