Yesaya 50:1-11

50  Yehova wanena kuti: “Kodi anthu inu, chili kuti chikalata chothetsera ukwati+ wa mayi wanu yemwe ndinamuthamangitsa?+ Kapena kodi anthu inu ndakugulitsani+ kwa munthu uti amene ndinali naye ngongole? Inutu mwagulitsidwa chifukwa cha zolakwa zanu,+ ndipo mayi wanu wathamangitsidwa chifukwa cha zochimwa zanu.+  N’chifukwa chiyani nditabwera sindinapeze aliyense?+ N’chifukwa chiyani nditaitana palibe amene anayankha?+ Kodi dzanja langa lafupika kwambiri moti silingathe kuwombola,+ kapena kodi mwa ine mulibe mphamvu zopulumutsira? Inetu ndimaumitsa nyanja+ pongoidzudzula chabe.+ Mitsinje ndimaisandutsa chipululu.+ Nsomba zake zimanunkha chifukwa chakuti mulibe madzi ndipo zimafa ndi ludzu.+  Kumwamba ndimakuveka mdima+ ndipo chiguduli ndimachisandutsa chophimba chake.”+  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino+ kuti ndidziwe mmene ndingamuyankhire munthu wotopa.+ Iye amandidzutsa m’mawa uliwonse. Amandidzutsa kuti makutu anga amve ngati anthu ophunzitsidwa bwino.+  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanditsegula khutu ndipo ineyo sindinapanduke.+ Sindinatembenukire kwina.+  Msana wanga ndinaupereka kwa ondimenya, ndipo masaya anga+ ndinawapereka kwa ozula ndevu. Nkhope yanga sindinaitchinjirize kuti isachitidwe zinthu zamanyazi ndi kulavuliridwa.+  Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza.+ N’chifukwa chake sindidzamva kuti ndanyozeka. Pa chifukwa chimenechi ndalimbitsa nkhope yanga ngati mwala wa nsangalabwi, ndipo ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.+  Amene adzanene kuti ndine wolungama ali pafupi.+ Ndani angalimbane nane? Tiyeni tikaonane pabwalo lamilandu.+ Kodi wotsutsana nane pa mlandu ndani?+ Abwere kufupi.+  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza. Ndani amene anganene kuti ndine wolakwa?+ Onsewo adzatha ngati chovala.+ Njenjete* idzawadya.+ 10  Ndani pakati panu amene amaopa+ Yehova ndi kumvera mawu a mtumiki wake?+ Ndani amayenda mu mdima wokhawokha+ ndipo alibe kuwala? Iye akhulupirire dzina la Yehova+ ndipo adalire Mulungu wake.+ 11  “Inu nonse amene mukuyatsa moto, amene mukuchititsa kuti uziwala n’kumathetheka, yendani m’kuwala kwa moto wanu, ndipo yendani pakati pa malawi a moto wothetheka umene mwayatsawo. Mudzalandira izi kuchokera m’dzanja langa: Mudzagona pansi mukumva ululu woopsa.+

Mawu a M'munsi

Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “njenjete” amatanthauza mtundu wa kachilombo kotchedwa kadziwotche kooneka ngati gulugufe, kamene kamadya zovala ngati mmene njenjete imachitira.