Yesaya 22:1-25

22  Uwu ndi uthenga wokhudza chigwa cha masomphenya:+ Kodi chachitika n’chiyani kuti anthu ako onse akwere pamadenga?+  Iwe unali mzinda wodzaza ndi chipwirikiti, waphokoso, komanso unali mudzi wokondwa.+ Anthu ako amene aphedwa, sanaphedwe ndi lupanga ndiponso sanaphedwe kunkhondo.+  Olamulira ako onse ankhanza+ athawa nthawi imodzi.+ Atengedwa ukaidi popanda kugwiritsa ntchito uta. Anthu ako onse amene apezeka atengedwa ukaidi limodzi.+ Iwo anali atathawira kutali.  N’chifukwa chake ndanena kuti: “Musandiyang’anitsitse. Ine ndikulira mopwetekedwa mtima+ ndipo anthu inu musaumirire kunditonthoza pamene ndikulirira mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe walandidwa katundu.+  Pakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, wabweretsa tsiku lachisokonezo,+ la kugonjetsedwa+ ndiponso lothetsa nzeru+ m’chigwa cha masomphenya. Kumeneko mpanda ukugwetsedwa+ ndipo kufuula kukumvekera m’phiri.+  Elamu+ watenga kachikwama koikamo mivi. Iye wakwera galeta lankhondo lonyamula anthu lokokedwa ndi mahatchi, ndipo Kiri+ wasolola chishango.  M’zigwa zako zabwino koposa mudzadzaza magaleta ankhondo. Ndithu mahatchi adzaima m’malo awo pachipata,  ndipo wina adzachotsa chophimba cha Yuda. M’tsiku limenelo, udzayang’ana kunyumba ya nkhalango yosungiramo zida zankhondo.+  Anthu inu mudzaona ming’alu ya Mzinda wa Davide pakuti idzakhala yambiri,+ ndipo mudzatunga madzi a m’dziwe lakumunsi.+ 10  Mudzawerenga nyumba za ku Yerusalemu ndipo mudzagwetsanso nyumba kuti mulimbitsire khoma lake.+ 11  Mudzakumba dziwe pakati pa makoma awiri, losungiramo madzi a dziwe lakale.+ Simudzayang’ana Wolipanga Wamkulu ndipo amene analipanga kalekalelo simudzamuona. 12  “M’tsiku limenelo, Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ adzalamula anthu kuti alire,+ agwetse misozi, amete mipala ndiponso avale ziguduli m’chiuno.+ 13  Komatu anthuwo adzakondwera ndi kusangalala. Adzapha ng’ombe ndi nkhosa. Adzadya nyama ndi kumwa vinyo.+ Iwo adzati, ‘Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.’”+ 14  Yehova wa makamu wandiuza+ kuti: “‘Cholakwa ichi sichidzaphimbidwa+ kufikira anthu inu mutafa.’+ Akutero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa.” 15  Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pita kwa Sebina,+ kapitawo woyang’anira nyumba ya mfumu,+ ukamuuze kuti, 16  ‘Kodi kuno kuli wachibale wako aliyense, ndipo kodi m’bale wako anaikidwa kuno kuti iweyo udzigobere manda kunoko?’+ Iye wagoba manda ake pamwamba pa phiri lamiyala. Akudzikonzera malo opumulirako m’thanthwe. 17  ‘Iwe mwamuna wamphamvu, tamvera! Yehova akuponya pansi mwamphamvu, ndipo akugwira mwamphamvu. 18  Ndithu iye adzakukulunga mwamphamvu ngati mpira n’kukuponyera kudziko lalikulu. Iweyo udzafera kumeneko ndipo magaleta ako ankhondo aulemerero adzakhala ochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako. 19  Ndidzakuchotsa pampando wako ndipo munthu wina adzakukokera pansi n’kukuchotsa pa udindo wako.+ 20  “‘M’tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga+ Eliyakimu,+ mwana wa Hilikiya.+ 21  Iyeyo ndidzamuveka mkanjo wako ndipo lamba wako ndidzamumanga mwamphamvu m’chiuno mwake.+ Ulamuliro wako ndidzaupereka m’manja mwake ndipo iye adzakhala tate wa anthu okhala mu Yerusalemu ndi a m’nyumba ya Yuda.+ 22  Ndidzaika makiyi+ a nyumba ya Davide paphewa pake. Iye akatsegula palibe amene azidzatseka ndipo akatseka palibe amene azidzatsegula.+ 23  Ndidzamukhomerera ngati chikhomo pamalo okhalitsa.+ Iye adzakhala ngati mpando wachifumu waulemerero kunyumba ya bambo ake.+ 24  Anthu adzapachika pa iyeyo ulemerero wonse wa nyumba ya bambo ake: mbadwa ndi mphukira, kutanthauza mitundu yonse ya ziwiya zing’onozing’ono, mitundu yonse ya ziwiya zolowa, ndi mitundu yonse ya mitsuko ikuluikulu.’ 25  “Yehova wa makamu wanena kuti: ‘M’tsiku limenelo chikhomo+ chimene chinakhomedwa pamalo okhalitsa chidzachotsedwa.+ Chidzazulidwa ndipo chidzagwa pansi. Katundu amene anapachikidwapo adzagwa pansi n’kuwonongeka, pakuti Yehova ndiye wanena zimenezi.’”+

Mawu a M'munsi