Yesaya 30:1-33

30  Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamva,+ amene amakonda kuchita zofuna zawo osati zofuna zanga,+ amene amapanga mgwirizano mwa kuthira pansi chakumwa monga nsembe motsutsana ndi zofuna zanga,* kuti awonjezere tchimo pa tchimo,+  amene akupita ku Iguputo+ osafunsira kwa ine,+ ndiponso amene akupita ku Iguputo kuti akapeze chitetezo kwa Farao ndi kukabisala mumthunzi wa Iguputo.+  Chitetezo cha Farao chidzakhala chochititsa manyazi kwa amuna inu,+ ndipo kubisala mumthunzi wa Iguputo kudzakhala chinthu chopereka chitonzo.+  Pakuti akalonga ake afika ku Zowani,+ ndipo nthumwi zake zafika mpaka ku Hanesi.  Aliyense adzachita manyazi ndi anthu opanda phindu, osathandiza ndi osapindulitsa, omwe ndi ochititsa manyazi ndi otonzetsa.”+  Uwu ndi uthenga wokhudza zilombo zokhala kum’mwera:+ Podutsa m’dziko lamavuto+ ndi la zowawa, la mikango ndi kulira kwa akambuku, la mphiri ndi la njoka zothamanga zaululu wamoto,+ iwo anyamulira chuma chawo pamsana pa abulu akuluakulu.+ Anyamuliranso katundu wawo pamalinunda a ngamila. Koma zinthu zimenezi zidzakhala zopanda phindu kwa anthu amenewa.  Aiguputo ndi anthu achabechabe ndipo sadzakuthandizani chilichonse.+ Choncho ndinawatcha kuti, “Rahabi.+ Iwo sadzachita chilichonse.”  “Tsopano lemba zimenezi pacholembapo, iwo akuona. Uzilembe m’buku+ kuti m’tsogolo zidzakhale umboni mpaka kalekale.+  Pakuti amenewa ndi anthu opanduka,+ ana ochita zachinyengo,+ amene safuna kumva malamulo a Yehova,+ 10  amene auza anthu oona masomphenya kuti: ‘Lekani kuona masomphenya,’ ndipo anthu olosera zam’tsogolo awauza kuti: ‘Musamalosere zoona zokhudza ife.+ Muzilankhula kwa ife zabwino zokhazokha. Muziona masomphenya abodza.+ 11  Patukani panjira. Dzerani njira ina.+ Musatiuzenso za Woyera wa Isiraeli.’”+ 12  Chotero Woyera wa Isiraeli wanena kuti: “Anthu inu mwakana mawu anga+ n’kumadalira kuba mwachinyengo. Mukudalira zinthu zachinyengo ndipo mukukhulupirira zinthu zimenezo.+ 13  Pa chifukwa chimenechi, kwa inu cholakwa chanuchi chidzakhala ngati mpanda wautali kwambiri umene wang’aluka penapake n’kupendekeka,+ umene ukhoza kugwa mwadzidzidzi, mosayembekezereka.+ 14  Munthu adzaugwetsa ngati mmene amaphwanyira mtsuko waukulu wadothi,+ mtsukowo n’kuphwanyikiratu wonse n’kungokhala tizidutswatizidutswa, ndipo patizidutswapo osapezeka ngakhale phale loti n’kupalira moto kapena kutungira madzi padambo.”+ 15  Pakuti Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Anthu inu mukabwerera kwa ine n’kusiya zimene mukuchita, mudzapulumuka. Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”+ Koma inu simunafune.+ 16  Ndipo munanena kuti: “Ayi, ife tidzakwera pamahatchi n’kuthawa!”+ N’chifukwa chake mudzathawe. Munanenanso kuti: “Tidzakwera pamahatchi othamanga kwambiri!”+ N’chifukwa chake anthu okuthamangitsani adzakhale othamanga kwambiri.+ 17  Anthu 1,000 adzanjenjemera chifukwa cha mawu oopseza a munthu mmodzi.+ Ndipo chifukwa cha mawu oopseza a anthu asanu, inuyo mudzathawa mpaka mudzatsala ochepa ngati mtengo wautali wa pangalawa wozikidwa pamwamba pa phiri, ndiponso ngati mtengo wozikidwa pamwamba pa phiri laling’ono kuti ukhale chizindikiro.+ 18  Chotero Yehova azidzayembekezera kuti akukomereni mtima+ ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo,+ pakuti Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo.+ Odala+ ndi anthu onse amene amamuyembekezera.+ 19  Anthu a ku Ziyoni+ akadzabwerera n’kukakhala ku Yerusalemu,+ iwe sudzaliranso.+ Mosakayikira, iye adzakukomera mtima akadzamva kulira kwako. Akadzangomva kulira kwakoko, iye adzakuyankha.+ 20  Yehova adzakupatsani masautso kuti akhale chakudya chanu, ndiponso adzakupatsani kuponderezedwa kuti kukhale madzi anu akumwa.+ Koma Mlangizi wako Wamkulu adzasiya kudzibisa ndipo maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.+ 21  Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako, akuti: “Njira ndi iyi.+ Yendani mmenemu anthu inu.” Yendani m’njira imeneyi kuti musasochere n’kulowera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 22  Zophimbira mafano anu ogoba asiliva ndi zokutira zifaniziro zanu zopangidwa ndi golide+ wosungunula,+ mudzaziona kuti ndi zonyansa+ ndipo mudzazitaya.+ Monga mkazi amene akusamba yemwe amataya monyansidwa kansalu kake, mudzanena kuti: “Nyansi zimenezi!”+ 23  Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munabzala munthaka,+ ndipo zokolola za munthakayo zidzakhala chakudya chopatsa thanzi.+ M’tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+ 24  Ng’ombe ndi abulu akuluakulu olima, zidzadya chakudya chokoma chosakaniza ndi zitsamba zowawasira, chimene mankhusu ake anauluzidwa pogwiritsa ntchito fosholo+ ndi chifoloko. 25  M’tsiku limene anthu ambiri adzaphedwe ndiponso limene nsanja zidzagwe, paphiri lililonse lalitali ndi paphiri lililonse laling’ono padzakhala timitsinje+ ndi ngalande zamadzi.+ 26  Kuwala kwa mwezi wathunthu kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa lowala kwambiri. Kuwala kwa dzuwa lowala kwambiri kudzawonjezereka maulendo 7+ ndipo kudzakhala ngati kuwala kwa masiku 7. Zimenezi zidzachitika m’tsiku limene Yehova adzachiritse mtundu wake wovulala+ ndi kupoletsa+ chilonda choopsa cha anthu ake, amene iyeyo anawavulaza powalanga. 27  Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali. Likubwera ndi mkwiyo woyaka+ ndiponso mitambo yolemera. Pamilomo yake padzaza mawu odzudzula ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+ 28  Mzimu wa Mulungu uli ngati mtsinje wosefukira umene wafika m’khosi,+ umene iye adzaugwiritsire ntchito posefa+ mitundu ya anthu monga zinthu zopanda pake. Pakamwa pa mitunduyo adzamangapo zingwe ngati zowongolera hatchi,+ zimene zidzawachititse kuyenda uku ndi uku.+ 29  Anthu inu mudzaimba nyimbo,+ ngati imene imaimbidwa usiku umene munthu amadziyeretsa pokonzekera chikondwerero.+ Mudzakhalanso ndi chimwemwe mumtima ngati munthu amene akuimba chitoliro+ popita kuphiri la Yehova,+ Thanthwe la Isiraeli.+ 30  Yehova adzapangitsa kuti ulemerero wa mawu ake+ umveke. Adzapangitsa kuti dzanja lake limene likutsika lionekere.+ Dzanjalo lidzatsika ndi mkwiyo waukulu,+ lawi la moto wowononga,+ mvula yamphamvu ndiponso yamkuntho+ ndi matalala.+ 31  Chifukwa cha mawu a Yehova, dziko la Asuri lidzagwidwa ndi mantha,+ ndipo iye adzalimenya ndi ndodo.+ 32  Ulendo uliwonse umene Yehova adzakwapule Asuri ndi ndodo yake, kudzamveka kulira kwa maseche ndi azeze.+ Pomenyana nawo, iye azidzazunguza zida zake uku ndi uku.+ 33  Malo otchedwa Tofeti*+ owonongerako Asuri akonzedwa kale. Malowo akonzedweranso mfumu yawo.+ Malo amene iye wakonzawo ndi ozama ndipo kuli moto waukulu ndi nkhuni zambiri. Mpweya wa Yehova ukuyatsa malowo ngati mtsinje wa sulufule.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mzimu wanga.”
Palembali mawu akuti “Tofeti” agwiritsidwa ntchito mophiphiritsa monga malo oyaka moto, ndipo akuimira chiwonongeko.