Yesaya 39:1-8

39  Pa nthawi imeneyo, Merodaki-baladani+ mwana wa Baladani mfumu ya Babulo,+ anatumiza makalata ndi mphatso+ kwa Hezekiya atamva kuti iye anadwala koma tsopano wapezanso mphamvu.+  Chotero Hezekiya anasangalala ndi alendowo+ ndipo anawaonetsa nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu,+ mafuta abwino, zonse za m’nyumba yake yosungiramo zida zankhondo,+ ndi chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse m’nyumba yake+ ndi mu ufumu wake wonse.+  Pambuyo pake, mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya n’kuifunsa kuti:+ “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+  Ndiyeno Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani m’nyumba mwanu?”+ Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili m’nyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”  Tsopano Yesaya anauza Hezekiya kuti:+ “Imvani mawu a Yehova wa makamu.  ‘Kukubwera masiku amene zinthu zonse zimene zili m’nyumba mwako, ndi zonse zimene makolo ako akhala akusunga kufikira lero, anthu adzazitenga n’kupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,’+ watero Yehova.  ‘Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna za panyumba+ ya mfumu ya ku Babulo.’”+  Pamenepo Hezekiya anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwalankhulawa ndi abwino.”+ Anapitiriza kuti: “Chifukwa bata* ndi mtendere+ zidzapitirira m’masiku anga.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “choonadi.”