Yesaya 52:1-15
52 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu zako+ iwe Ziyoni. Vala zovala zako zokongola+ iwe Yerusalemu, mzinda woyera.+ Pakuti mwa iwe simudzabweranso munthu wosadulidwa ndi wodetsedwa.+
2 Dzuka pafumbi pamene ulipo.+ Sansa fumbilo, khala pamalo aulemu iwe Yerusalemu. Masula zingwe zimene zili m’khosi mwako, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni wogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+
3 Pakuti Yehova wanena kuti: “Anthu inu munagulitsidwa popanda malipiro alionse,+ ndipo mudzawomboledwanso popanda ndalama.”+
4 Pakuti Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Poyamba anthu anga anapita ku Iguputo kuti akakhale ngati alendo.+ Ndiyeno Asuri anawapondereza popanda chifukwa.”
5 “Tsopano kodi pamenepa ndichitepo chiyani?” akutero Yehova. “Pakuti anthu anga anatengedwa popanda malipiro alionse.+ Amene anali kuwalamulira ankangokhalira kufuula.+ Nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu, dzina langa anali kulichitira chipongwe,”+ akutero Yehova.
6 “Pa chifukwa chimenecho anthu anga adzadziwa dzina langa.+ Adzalidziwa pa chifukwa chimenecho m’tsiku limenelo, pakuti ineyo ndi amene ndikulankhula.+ Ndithu ndineyo.”
7 Mapazi+ a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino, ndi okongola kwabasi!+ Munthu yemwe akulengeza za mtendere,+ yemwe akubweretsa uthenga wabwino wa zinthu zabwino kuposa kale,+ yemwe akulengeza za chipulumutso,+ yemwe akuuza Ziyoni kuti: “Mulungu wako wakhala mfumu.”+
8 Tamvera! Alonda ako+ akufuula.+ Onse akufuula pamodzi mokondwera. Pamene Yehova azidzasonkhanitsanso okhala mu Ziyoni,+ iwo adzaona ndi maso awo.+
9 Inu malo osakazidwa a mu Yerusalemu, sangalalani nonse pamodzi ndipo fuulani mokondwa,+ pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo wawombola Yerusalemu.+
10 Yehova waika pamtunda dzanja lake loyera kuti mitundu yonse ione,+ ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.+
11 Tembenukani! Tembenukani! Tulukani mmenemo!+ Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa.+ Chokani pakati pake!+ Khalani oyera, inu amene mukunyamula ziwiya za Yehova.+
12 Anthu inu simudzatuluka mwachipwirikiti, komanso simudzachoka chothawa.+ Pakuti Yehova azidzayenda patsogolo panu,+ ndipo Mulungu wa Isiraeli azidzalondera kumbuyo kwanu.+
13 Taona! Mtumiki wanga+ azidzachita zinthu mwanzeru.+ Iye adzakhala ndi udindo wapamwamba ndipo adzakwezedwa ndi kulemekezedwa kwambiri.+
14 Monga momwe anthu ambiri anamuyang’anira modabwa,+ pakuti nkhope yake inali yoipa kwambiri+ kuposa ya munthu wina aliyense, ndiponso maonekedwe ake+ anali oipa kuposa a ana a anthu,
15 momwemonso iye adzadabwitsa mitundu yambiri.+ Mafumu adzatseka pakamwa pawo akadzamuona,+ chifukwa iwo adzaona zimene sanauzidwepo, ndipo adzaganizira zimene sanamvepo.+