Yesaya 57:1-21

57  Wolungama wawonongedwa,+ koma palibe amene zikum’khudza.+ Anthu amene amasonyeza kukoma mtima kosatha akusonkhanitsidwira kwa akufa+ popanda wozindikira kuti munthu wolungamayo wafa ndipo wathawa tsoka.+  Iye amalowa mumtendere.+ Aliyense woyenda mowongoka+ amapita kukapuma+ m’manda.*+  “Koma anthu inu bwerani pafupi,+ inu ana a mayi wolosera zam’tsogolo,+ mbewu ya munthu wachigololo ndi ya mkazi wochita uhule:+  Kodi mukusangalala chifukwa cha kuvutika kwa ndani?+ Kodi mukuyasamulira ndani pakamwa panu, ndi kum’tulutsira lilime?+ Kodi inu si inu ana a machimo, mbewu ya chinyengo,+  amene mumadzutsa chilakolako chanu pakati pa mitengo ikuluikulu+ ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+ Kodi si inu amene mumapha ana m’zigwa* pakati pa matanthwe?+  “Gawo lako linali pamodzi ndi miyala yosalala ya m’chigwa.+ Iwo ndiwo anali gawo lako.+ Iwe unawathirira nsembe yachakumwa,+ ndiponso unawapatsa mphatso. Kodi ine ndingadzitonthoze ndi zinthu zimenezo?+  Bedi lako unaliika pamwamba pa phiri lalitali ndi lokwezeka.+ Unapitanso kumeneko kukapereka nsembe.+  Unaika chizindikiro chachikumbutso chako kuseri kwa chitseko ndi kuseri kwa felemu.+ Iwe unavula n’kukwera mtunda kupita kumeneko uli kutali ndi ine. Unakulitsa bedi lako,+ ndipo unachita nawo pangano. Unkakonda kugona nawo pabedi+ ndipo unaona chiwalo cha mwamuna.  Iwe unatsetserekera kwa Meleki utatenga mafuta, ndipo unachulukitsa mafuta ako onunkhira.+ Unapitiriza kutumiza nthumwi zako kutali kwambiri moti mpaka unatsitsira zochita zako m’Manda.+ 10  Wakhala ukugwira ntchito mwamphamvu m’njira zako zambirimbiri.+ Sunanene kuti, ‘N’zopanda phindu!’ Wapezanso mphamvu zina.+ N’chifukwa chake sunadwale.+ 11  “Kodi unachita mantha ndi ndani kuti uyambe kuopa,+ mpaka kuyamba kunama?+ Koma sunakumbukire ine.+ Palibe chimene unaganizira mumtima mwako.+ Popeza ine ndinakhala chete ndipo sindinachitepo kanthu pa zochita zako,+ iweyo sunali kundiopa.+ 12  Ineyo ndidzanena za chilungamo chako+ ndi ntchito zako,+ kuti sizidzakupindulira.+ 13  Ukamafuula popempha thandizo, zinthu zimene unasonkhanitsa sizidzakupulumutsa,+ koma mphepo idzaziulutsa zonsezo+ ndipo mpweya udzazitenga. Koma munthu wobisala mwa ine+ adzalandira dziko ndipo adzatenga phiri langa loyera.+ 14  Ndiyeno wina adzati, ‘Anthu inu, konzani msewu! Konzani msewu anthu inu! Lambulani msewu.+ Chotsani chopinga chilichonse panjira ya anthu anga.’”+ 15  Pakuti Wapamwamba ndi Wokwezeka,+ yemwe adzakhalepo kwamuyaya+ ndiponso yemwe dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti: “Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyera.+ Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa,+ kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+ 16  Pakuti ine sindidzatsutsana nanu mpaka kalekale, ndiponso sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale.+ Popeza chifukwa cha ine, mzimu wa munthu ukhoza kufooka,+ ngakhalenso zinthu zopuma zimene ineyo ndinapanga.+ 17  “Ine ndinakwiya chifukwa cha phindu lachinyengo limene analipeza mosayenera.+ Ndinakwiya ndipo ndinamulanga. Ndinabisa nkhope yanga chifukwa cha mkwiyo.+ Koma iye ankangoyendabe ngati wopanduka+ m’njira ya mtima wake. 18  Ine ndaona njira zake. Ndinayamba kumuchiritsa+ ndi kumutsogolera,+ ndiponso ndinamutonthoza+ iyeyo ndi anthu ake amene anali kulira.”+ 19  “Ndikulenga chipatso cha milomo.+ Mtendere wosatha udzakhala kwa yemwe ali kutali ndiponso kwa yemwe ali pafupi,+ ndipo ndidzam’chiritsa,”+ akutero Yehova. 20  “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuwinduka, imene ikukanika kukhala bata, imene madzi ake akuvundula zomera za m’nyanjamo ndiponso matope. 21  Oipa alibe mtendere,”+ akutero Mulungu wanga.

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “pabedi.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.