Yesaya 34:1-17
34 Mitundu inu, bwerani pafupi kuti mumve.+ Inu mitundu ya anthu,+ mvetserani. Dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo zimvetsere.+ Nthaka ya padziko lapansi+ ndi zonse zimene zili pamenepo zimve.+
2 Pakuti Yehova wakwiyira mitundu yonse.+ Wapsera mtima asilikali awo onse.+ Iye awawononga ndipo awapha.+
3 Anthu awo ophedwa adzatayidwa, ndipo fungo loipa la mitembo yawo lidzakwera m’mwamba.+ Mapiri adzasungunuka chifukwa cha magazi awo.+
4 Makamu onse akumwamba adzawola.+ Kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu wolembapo.+ Makamu onse akumwambawo adzafota ngati mmene masamba amafotera pamtengo wa mpesa n’kuthothoka, ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.+
5 “Pakuti lupanga langa+ lidzakhala magazi okhaokha kumwambako. Lupangalo lidzatsikira pa Edomu+ ndi pa anthu amene ndikufuna kuwawononga+ mogwirizana ndi chilungamo changa.
6 Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha+ ndipo lidzaterera ndi mafuta. Lidzadzaza magazi a nkhosa zamphongo zing’onozing’ono ndi a mbuzi zamphongo. Lidzaterera ndi mafuta+ a impso za nkhosa zamphongo, pakuti Yehova adzapereka nsembe ku Bozira ndipo adzapha nyama zambiri m’dziko la Edomu.+
7 Ng’ombe zamphongo zam’tchire+ zidzatsetserekera nawo kumeneko, zing’onozing’ono ndi zamphamvu zomwe.+ Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha, ndipo fumbi lawo lidzanona ndi mafuta.”+
8 Pakuti Yehova ali ndi tsiku lobwezera adani ake,+ ndi chaka chopereka chilango, chifukwa cha zolakwa zimene Ziyoni anachitiridwa.+
9 Mitsinje yake* idzasintha n’kukhala phula. Fumbi lake lidzakhala sulufule, ndipo dziko lake lidzakhala ngati phula loyaka moto.+
10 Usana ndi usiku, motowo sudzazima. Utsi wake uzidzakwera m’mwamba mpaka kalekale.+ Dzikolo lidzakhala louma ku mibadwomibadwo.+ Mpaka muyaya palibe amene adzadutseko.+
11 Mbalame zotchedwa vuwo ndi nungu zidzakhala kumeneko. Komanso akadzidzi a makutu ataliatali ndi akhwangwala azidzakhala kumeneko.+ Iye adzatambasulira dzikolo chingwe choyezera+ malo opanda kanthu, ndiponso miyala yoyezera kuwongoka kwa chinthu.
12 Palibe aliyense wochokera pa anthu ake olemekezeka amene adzakhale mfumu, ndipo akalonga ake onse adzatha.+
13 Minga zidzamera pansanja zake zokhalamo. Zomera zoyabwa ndi zitsamba zaminga zidzamera pamalo ake otetezeka,+ ndipo iye adzakhala malo okhala mimbulu+ ndi bwalo la nthiwatiwa.+
14 Nyama zokhala kumadera opanda madzi zidzakumana ndi nyama zolira mokuwa, ndipo ngakhale ziwanda zooneka ngati mbuzi,*+ zizidzaitanizana kumeneko. Mbalame yotchedwa lumbe izidzasangalalako n’kupezako malo okhala.+
15 Kumeneko, njoka yodumpha idzakonzako chisa chake n’kuikira mazira. Idzakhalira mazirawo n’kuswa tiana, ndipo idzatisonkhanitsa pansi pa mthunzi wake. Mbalame zotchedwa akamtema+ zidzasonkhana kumeneko iliyonse ndi mwamuna wake.
16 Fufuzani m’buku+ la Yehova ndipo muwerenge mokweza. Palibe ndi imodzi yomwe imene ikusowekapo.+ Zonsezo sizilephera kupeza mwamuna, chifukwa pakamwa pa Yehova ndi pamene palamula.+ Mzimu wake ndi umene wazisonkhanitsa pamodzi.+
17 Iye ndi amene waziponyera maere, ndipo dzanja lake lazigawira malowo ndi chingwe choyezera.+ Zidzakhala kumeneko mpaka kalekale. Kudzakhala kwawo ku mibadwomibadwo.