Yesaya 29:1-24
29 “Tsoka kwa Ariyeli!*+ Tsoka kwa Ariyeli, tauni imene Davide anamangako msasa.+ Anthu inu, pitirizani kuchita zikondwerero+ zanu chaka ndi chaka.
2 Ariyeli ndidzamukhwimitsira zinthu,+ ndipo padzakhala kulira ndi kumva chisoni.+ Kwa ine, iye adzakhala ngati malo osonkhapo moto paguwa lansembe la Mulungu.+
3 Ine ndidzamanga misasa mokuzungulira mbali zonse kuti ndichite nawe nkhondo. Ndidzamanga mpanda wa mitengo yosongoka mokuzungulira, ndipo ndidzamanga chiunda choti ndidzamenyerepo nkhondo pomenyana nawe.+
4 Iweyo udzatsika moti uzidzalankhula uli pansi penipeni. Mawu ako azidzamveka otsika ngati akuchokera m’fumbi.+ Mawuwo adzachokera m’dothi ngati a wolankhula ndi mizimu, ndipo adzamveka ngati kulira kwa mbalame kuchokera m’fumbi.+
5 Khamu la anthu achilendo lidzasanduka fumbi losalala,+ ndipo khamu la olamulira ankhanza+ lidzakhala ngati mankhusu amene akuuluzika.+ Zimenezi zidzachitika mwadzidzidzi, mosayembekezereka.+
6 Yehova wa makamu adzatembenukira kwa iwe kuti akupulumutse ndi mabingu, zivomezi, phokoso lalikulu, mphepo yamkuntho, ndi lawi la moto wowononga.”+
7 Khamu la mitundu yonse imene ikuchita nkhondo ndi Ariyeli,+ onse amene akumenyana naye ndi kumumangira nsanja zomenyerapo nkhondo, ndiponso amene akumukhwimitsira zinthu,+ adzaona ngati za m’maloto, za m’masomphenya a usiku.
8 Inde, zidzawachitikira ngati pamene munthu wanjala akulota kuti akudya, kenako n’kudzidzimuka n’kuona kuti m’mimba mwake mulibe kanthu,+ kapena ngati pamene munthu waludzu akulota kuti akumwa madzi, n’kudzidzimuka n’kuona kuti adakali wotopa ndipo kukhosi kwake n’kouma. Umu ndi mmene zidzachitikire ndi khamu lonse la mitundu imene ikuchita nkhondo ndi phiri la Ziyoni.+
9 Anthu inu, dabwani ndipo chitani kukamwa yasa!+ Matani maso anu kuti musaone.+ Iwo aledzera,+ koma osati ndi vinyo. Akudzandira, koma osati chifukwa cha chakumwa choledzeretsa.+
10 Pakuti Yehova wakukhuthulirani mzimu wa tulo tatikulu+ ndipo watseka maso anu, omwe ndi aneneri.+ Waphimba mitu yanu,+ imene ndi anthu amasomphenya.+
11 Kwa anthu inu, masomphenya a chilichonse akhala ngati mawu a m’buku limene lamatidwa kuti lisatsegulidwe,+ limene alipereka kwa munthu wodziwa kuwerenga, n’kumuuza kuti: “Werenga bukuli mokweza.” Koma iye n’kunena kuti: “Sindingathe kuliwerenga, chifukwa ndi lomatidwa.”+
12 Kenako bukulo laperekedwa kwa munthu wosadziwa kuwerenga, n’kumuuza kuti: “Werenga bukuli mokweza,” koma iye n’kuyankha kuti: “Sindidziwa kuwerenga m’pang’ono pomwe.”
13 Yehova wanena kuti: “Popeza anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha+ koma mtima wawo auika kutali ndi ine,+ ndiponso amangophunzira malamulo a anthu n’kumaganiza kuti kuchita zimenezo ndiye kundiopa,+
14 ine ndidzachitanso zodabwitsa ndi anthu awa.+ Ndidzazichita m’njira yodabwitsa, pogwiritsira ntchito chinthu chodabwitsa. Nzeru za anthu awo anzeru zidzatha, ndipo kumvetsetsa zinthu kwa anthu awo ozindikira kudzabisika.”+
15 Tsoka kwa anthu amene abisa patali kwambiri zolinga zawo, pozibisira Yehova,+ amene zochita zawo zimachitikira m’malo a mdima,+ ndipo amati: “Ndani akutiona, ndipo ndani akudziwa zimene tikuchita?”+
16 Anthu inu ndinu opotoka maganizo kwabasi! Kodi woumba zinthu ndi dongo angafanane ndi dongolo?+ Kodi chinthu chochita kupangidwa chingamunene amene anachipanga, kuti: “Iye uja sanandipange”?+ Komanso kodi chinthu chochita kuumbidwa chingamunene amene anachiumba, kuti: “Iye uja sanasonyeze kuti ndi womvetsa zinthu”?+
17 Kodi si pangotsala kanthawi kochepa kuti Lebanoni asanduke munda wa zipatso,+ ndiponso kuti munda wa zipatsowo udzangokhala ngati nkhalango?+
18 M’tsiku limenelo, ogontha adzamva mawu a m’buku.+ Ngakhale maso a anthu akhungu adzamasuka ku mdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.+
19 Ofatsa+ adzawonjezera kukondwa mwa Yehova, ndipo ngakhale osauka pakati pa anthu adzasangalala ndi Woyera wa Isiraeli,+
20 chifukwa wolamulira wankhanza adzafika pamapeto pake,+ ndipo wodzitama adzatha.+ Onse okhala tcheru kuti achitire anzawo zoipa+ adzaphedwa,
21 amene amachimwitsa munthu ndi mawu ake,+ amene amatchera msampha munthu wodzudzula ena pachipata,+ ndiponso amene amagwiritsira ntchito mfundo zopanda umboni pokankhira pambali munthu wolungama.+
22 Chotero Yehova, amene anawombola Abulahamu, wanena izi kwa nyumba ya Yakobo:+ “Tsopano Yakobo sachita manyazi. Tsopano nkhope yake sikhala yakugwa,+
23 pakuti akaona ana ake pakati pake, ntchito ya manja anga,+ iwo adzayeretsa dzina langa.+ Adzayeretsadi Woyera wa Yakobo,+ ndipo adzalemekeza kwambiri Mulungu wa Isiraeli.+
24 Anthu amene akuganiza molakwa mumtima mwawo adzamvetsa zinthu, ndipo ngakhale amene akudandaula adzalandira malangizo.”+
Mawu a M'munsi
^ Mwina kutanthauza, “Malo Osonkhapo Moto a Paguwa Lansembe la Mulungu,” amene anali Yerusalemu.