Yesaya 40:1-31

40  “Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,” akutero Mulungu wanu anthu inu.+  “Mulankhuleni Yerusalemu momufika pamtima.+ Muuzeni mofuula kuti ntchito yake yogwira mokakamizidwa yatha,+ ndiponso kuti zolakwa zake zalipiridwa.+ Pakuti kuchokera m’dzanja la Yehova, iye walandira malipiro okwanira a machimo ake onse.”+  Tamverani! Winawake akufuula m’chipululu kuti:+ “Konzani njira ya Yehova+ anthu inu! Wongolani msewu wa Mulungu wathu wodutsa m’chipululu.+  Chigwa chilichonse chikwezedwe m’mwamba,+ ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zitsitsidwe.+ Malo okumbikakumbika asalazidwe ndipo malo azitundazitunda akhale chigwa.+  Ulemerero wa Yehova ndithu udzaonekera+ ndipo anthu onse adzauonera limodzi,+ pakuti pakamwa pa Yehova m’pamene panena zimenezi.”+  Tamvera! Winawake akunena kuti: “Lankhula mofuula!”+ Ndiye wina akuti: “Ndilankhule mofuula za chiyani?” “Anthu onse ali ngati udzu wobiriwira ndipo kukoma mtima kwawo konse kosatha kuli ngati maluwa akutchire.+  Udzu wobiriwirawo wauma ndipo maluwawo afota+ chifukwa mpweya wa Yehova wauzirapo.+ Ndithu anthu ali ngati udzu wobiriwira.+  Udzu wobiriwirawo wauma. Maluwawo afota.+ Koma mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”+  Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Ziyoni,+ kwera phiri lalitali.+ Lankhula mwamphamvu ndiponso mofuula, iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.+ Fuula! Usachite mantha.+ Uza mizinda ya ku Yuda kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu.”+ 10  Taonani! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabwera ngati wamphamvu ndipo dzanja lake lizidzalamulira m’malo mwa iyeyo.+ Mphoto yake ili ndi iyeyo+ ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.+ 11  Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa.+ Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake,+ ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.+ Nkhosa zoyamwitsa adzayenda nazo mosamala.+ 12  Ndani anayezapo madzi onse a m’nyanja pachikhatho cha dzanja lake?+ Ndani anayezapo kumwamba konse ndi dzanja lake?+ Ndani anayezapo fumbi lonse la padziko lapansi ndi mbale imodzi yokha yoyezera?+ Ndani anayezapo mapiri ndi muyezo, kapena ndani anayezapo zitunda pa sikelo? 13  Ndani anayezapo mzimu wa Yehova? Ndi munthu uti amene angamupatse malangizo kapena kumuphunzitsa kanthu?+ 14  Kodi anafunsirapo nzeru kwa ndani kuti amuthandize kumvetsetsa zinthu? Ndani amamuphunzitsa njira ya chilungamo? Ndani amamuphunzitsa kuti azidziwa zinthu,+ ndipo ndani amamuphunzitsa kuti akhale womvetsa bwino zinthu?+ 15  Taonani! Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko, ndipo kwa iye ili ngati fumbi pasikelo.+ Iyetu amanyamula zilumba+ ngati kuti ndi fumbi. 16  Ngakhale mitengo yonse ya ku Lebanoni singakwane kusonkhezera moto kuti usazime, ndipo nyama zake zam’tchire+ si zokwanira kukhala nsembe yopsereza.+ 17  Mitundu yonse ndi yopanda pake pamaso pake.+ Amaiona ngati si kanthu n’komwe, ngati kuti iyo kulibe.+ 18  Kodi anthu inu Mulungu mungamuyerekezere ndi ndani,+ ndipo kodi mungapange chiyani choti mumufanizire nacho?+ 19  Mmisiri wapanga chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Mmisiri wina wa zitsulo wachikuta ndi golide,+ ndipo akuchipangira matcheni asiliva.+ 20  Munthu amasankha mtengo wosawola kuti ukhale ngati chopereka.+ Amafunafuna mmisiri waluso kuti amupangire chifaniziro chosema+ chimene sichingagwedezeke.+ 21  Kodi anthu inu simukudziwa? Kodi simunamve? Kodi simunauzidwe kuyambira pa chiyambi? Kodi simunamvetsetse umboni umene wakhalapo kuyambira pamene dziko lapansi linakhalapo?+ 22  Pali Winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lozungulira,+ limene okhalamo ake ali ngati ziwala. Iye anayala kumwamba ngati nsalu yopyapyala, ndipo anakutambasula ngati hema wokhalamo.+ 23  Iye amatsitsa anthu olemekezeka, ndipo amachititsa oweruza a padziko lapansi kuoneka ngati sanakhalepo n’komwe.+ 24  Iwo sanabzalidwe n’komwe ndipo sanafesedwe. Chitsa chawo sichinazike mizu munthaka.+ Munthu akhoza kungowauzira iwo n’kuuma,+ ndipo mphepo yamkuntho idzawauluza ngati mapesi.+ 25  “Koma kodi anthu inu mungandiyerekezere ndi ndani kuti ndifanane naye?” akutero Woyerayo.+ 26  “Kwezani maso anu kumwamba muone. Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?+ Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezizo malinga ndi chiwerengero chake, ndipo amaziitana potchula iliyonse dzina lake.+ Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa,+ ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu, palibe imene imasowa. 27  “N’chifukwa chiyani iwe Yakobo, iwe Isiraeli, ukunena kuti: ‘Njira yanga yabisika kwa Yehova,+ ndipo zoti anthu sakundichitira chilungamo Mulungu wanga sakuziona’?+ 28  Kodi iwe sukudziwa kapena kodi sunamve?+ Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.+ Iye satopa kapena kufooka.+ Palibe amene angadziwe zimene iyeyo amazimvetsa.+ 29  Iye amapereka mphamvu kwa munthu wotopa,+ ndipo wofooka amam’patsa nyonga zochuluka.+ 30  Anyamata adzatopa n’kufooka ndipo amuna achinyamata adzapunthwa, 31  koma anthu odalira+ Yehova adzapezanso mphamvu.+ Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Adzathamanga koma osafooka. Adzayenda koma osatopa.”+

Mawu a M'munsi