Yesaya 13:1-22
13 Uwu ndi uthenga wokhudza Babulo,+ umene Yesaya mwana wa Amozi+ anaona m’masomphenya:
2 “Amuna inu, imikani chizindikiro+ paphiri la miyala yokhayokha. Afuulireni! Akodoleni ndi dzanja,+ kuti adzalowe pamakomo a anthu olemekezeka.+
3 Ine ndapereka lamulo kwa opatulika anga.+ Ndaitananso anthu anga amphamvu oti asonyeze mkwiyo wanga.+ Amenewa ndi anthu anga okondwa kwambiri.
4 Tamverani! M’mapiri mukumveka phokoso la khamu la anthu, phokoso ngati la anthu ambiri.+ Tamverani! Kukumveka chisokonezo cha maufumu, cha mitundu imene yasonkhanitsidwa pamodzi.+ Yehova wa makamu akusonkhanitsira asilikali ku nkhondo.+
5 Iwo akuchokera kudziko lakutali.+ Akuchokera kumalekezero a kumwamba. Yehova akubwera ndi zida za mkwiyo wake, kuti asakaze dziko lonse lapansi.+
6 “Fuulani, anthu inu,+ chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi.+ Lidzabwera ngati kuti Wamphamvuyonse akulanda zinthu.+
7 N’chifukwa chake anthu onse adzataya mtima, ndipo mitima ya anthu onse idzasungunuka.+
8 Anthu asokonezeka.+ Nsautso ndi zowawa za pobereka zawagwera. Iwo akumva zowawa ngati mkazi amene akubereka.+ Akuyang’anana modabwa. Nkhope zawo zafiira ndi mantha.+
9 “Taonani! Tsiku la Yehova likubwera. Tsikulo n’lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto. Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chodabwitsa,+ ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa a m’dzikolo.+
10 Pakuti nyenyezi zakumwamba ndi magulu a nyenyezi a Kesili+ sizidzawala. Dzuwa lidzachita mdima potuluka, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
11 Nthaka ndidzaibwezera zoipa zake,+ ndipo anthu oipa ndidzawabwezera zolakwa zawo. Kunyada kwa anthu odzikuza ndidzakuthetsa, ndipo ndidzatsitsa olamulira ankhanza ndi odzikweza.+
12 Ndidzachititsa kuti anthu azisowa kwambiri kuposa golide woyengedwa bwino,+ ndiponso ndidzachititsa kuti anthu ochokera kufumbi azisowa kwambiri kuposa golide wa ku Ofiri.+
13 Chifukwa cha zimenezi, ndidzachititsa kuti kumwamba kugwedezeke+ ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera n’kuchoka m’malo mwake, chifukwa cha ukali wa Yehova wa makamu,+ pa tsiku limene mkwiyo wake udzayake.+
14 Monga insa imene ikuthamangitsidwa ndiponso monga ziweto zopanda wozikusa,+ aliyense wa iwo adzatembenukira kwa anthu ake, ndipo aliyense wa iwo adzathawira kudziko lake.+
15 Aliyense amene adzapezedwe adzabooledwa ndipo aliyense amene adzagwidwe limodzi ndi anthu ena onse pa nthawiyo, adzaphedwa ndi lupanga.+
16 Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa, iwo akuona.+ Katundu wa m’nyumba zawo adzalandidwa, ndipo akazi awo adzagwiriridwa.+
17 “Ndidzachititsa Amedi kuti awaukire.+ Iwowa amaona kuti siliva si kanthu, ndipo sasangalala ndi golide.
18 Ndi mauta awo, adzaphwanyaphwanya ngakhale anyamata awo.+ Iwo sadzamvera chisoni zipatso za m’mimba.+ Diso lawo silidzamvera chisoni ana aamuna.
19 Babulo, amene ndi chokongoletsera maufumu,+ chinthu chokongola ndi chonyadira cha Akasidi,+ adzakhala ngati pamene Mulungu anagonjetsa Sodomu ndi Gomora.+
20 M’Babulo simudzakhalanso anthu,+ ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwomibadwo.+ Kumeneko Mluya sadzakhomako hema wake, ndipo abusa sadzagonekako ziweto zawo.
21 Nyama zam’tchire zokhala kumadera opanda madzi zidzagona kumeneko, ndipo nyumba za anthu amene anali kukhala kumeneko zidzadzaza ndi akadzidzi.+ Nthiwatiwa zizidzakhala kumeneko, ndipo ziwanda zooneka ngati mbuzi* zizidzadumphadumpha kumeneko.+
22 Mimbulu izidzalira munsanja zake zokhalamo,+ ndipo njoka zikuluzikulu zizidzakhala m’nyumba zachifumu zokongola. Nyengo yake yatsala pang’ono kufika, ndipo masiku ake sadzatalikitsidwa.”+
Mawu a M'munsi
^ Zimenezi zikuimira ziwanda kapena nyama zenizeni zimene anthu akaziona ankayamba kuganiza za ziwanda.