Yesaya 38:1-22
38 M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.+ Choncho mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anabwera kwa iye n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita,+ chifukwa iweyo ufa ndithu. Sukhala ndi moyo.’”+
2 Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova.+
3 Iye anapemphera kuti: “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+
4 Tsopano Yehova analankhula+ ndi Yesaya kuti:
5 “Pita, kauze Hezekiya kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako+ wanena kuti: “Ndamva pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Tsopano ndiwonjezera zaka 15 pa masiku ako.+
6 Ndidzalanditsa iweyo ndi mzindawu m’manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzateteza mzinda uno.+
7 Chizindikiro chochokera kwa Yehova, chakuti Yehova adzakwaniritsadi mawu amene walankhula, ndi ichi:+
8 Ndichititsa mthunzi wa dzuwa+ umene wapita kale kutsogolo pamasitepe a Ahazi, kuti ubwerere m’mbuyo masitepe 10.”’”+ Choncho dzuwa linabwerera m’mbuyo pang’onopang’ono masitepe 10 pa masitepe pomwe linali litapita kale kutsogolo.+
9 Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala+ n’kuchira, analemba zotsatirazi.+
10 Ine ndinati: “Pakatikati pa masiku anga ndidzalowa pazipata+ za Manda.Ndidzamanidwa zaka zanga zotsala.”+
11 Ndanena kuti: “Sindidzamuona Ya.* Ndithu Ya sindidzam’penya m’dziko la amoyo.+Anthu sindidzawaonanso. Ndidzakhala ndi anthu okhala kudziko limene kulibe moyo.
12 Malo anga okhala ali ngati hema wa abusa. Mitengo yake yazulidwa ndipo hemayo wachotsedwapo.+Ndakulunga moyo wanga ngati munthu wowomba nsalu.Winawake wandidula+ ngati mmene amadulira nsalu kuchowombera nsalu akamaliza kuiwomba.Kuyambira m’mawa mpaka usiku mumandipereka ku zowawa.+
13 Ndadzitonthoza mpaka m’mawa.+Mafupa anga onse, iye akungokhalira kuwaphwanya ngati mkango.+Kuyambira m’mawa mpaka usiku mukungokhalira kundipereka ku zowawa.+
14 Ndikungokhalira kulira ngati namzeze* kapena pumbwa.*+Ndikungokhalira kubuula ngati njiwa.+
Maso anga akupenyetsetsa kumwamba motopa. Choncho ndinati:+‘Inu Yehova ine ndapanikizika. Chonde ndithandizeni.’+
15 Kodi ndinene kuti chiyani? Kodi iyeyo andiuza kuti chiyani?+Iyeyonso wachitapo kanthu.+Zaka zanga zonse, ndikungokhalira kuyenda ndili khuma chifukwa cha chisoni cha mtima wanga.+
16 ‘Ndi mawu anu, anthu amakhalabe ndi moyo inu Yehova, ndipo mofanana ndi wina aliyense, mzimu wanga umapeza moyo kudzera mu zochita zanu.+Inu mudzandibwezera thanzi langa n’kundisiya ndi moyo.+
17 M’malo mopeza mtendere ndinapeza zowawa, zowawatu zedi!+Inuyo mwamamatira moyo wanga ndipo mwauteteza kuti usapite kudzenje la chiwonongeko.+Pakuti machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.+
18 Pakuti Manda sangakutamandeni.+ Imfa singakulemekezeni.+Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kukhulupirika kwanu.+
19 Munthu wamoyo, amene akupuma, ndi amene angakutamandeni,+Ngati mmene ineyo ndikuchitira lero.+Bambo akhoza kuphunzitsa+ ana ake za kukhulupirika kwanu.
20 Inu Yehova bwerani mudzandipulumutse,+ ndipo tidzaimba nyimbo zimene ine ndinapeka. Ndidzaimba ndi zoimbira za zingwe+Kunyumba ya Yehova masiku onse a moyo wathu.’”+
21 Kenako Yesaya anati: “Anthu atenge nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndipo azikhukhutize pachithupsa+ chimene ali nacho kuti achire.”+
22 Pa nthawiyi, Hezekiya anati: “Kodi chizindikiro chakuti ndidzapita kunyumba ya Yehova n’chiyani?”+
Mawu a M'munsi
^ Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”
^ Mbalame imeneyi ena amati “nyapwere.”