Yesaya 48:1-22
48 Mverani izi inu a m’nyumba ya Yakobo, inu amene mumadzitcha ndi dzina la Isiraeli,+ amene munatuluka kuchokera m’madzi a Yuda,+ amene mumalumbira pa dzina la Yehova,+ ndiponso inu amene mumaitana Mulungu wa Isiraeli,+ koma osati m’choonadi kapena m’chilungamo.+
2 Pakuti iwo amadzitcha kuti amakhala mumzinda woyera,+ ndipo amadalira Mulungu wa Isiraeli+ amene dzina lake ndi Yehova wa makamu.+
3 “Ndanena zinthu zoyambirira kuchokera pa nthawi imeneyo. Zinatuluka pakamwa panga, ndipo ndinazichititsa kumveka.+ Mwadzidzidzi, ndinazichita ndipo zinachitikadi.+
4 Podziwa kuti ndinu olimba,+ ndi kuti mtsempha wa khosi lanu uli ngati chitsulo,+ ndiponso kuti mphumi yanu ili ngati mkuwa,+
5 ine ndinakuuzani zonse kuyambira nthawi imeneyo. Ndinakuuzani zisanachitike,+ kuti musadzanene kuti, ‘Fano langa ndi limene lachita zimenezi, ndipo chifaniziro changa chosema komanso chifaniziro changa chopangidwa ndi chitsulo chosungunula, n’zimene zalamula zimenezi.’+
6 Inuyo mwazimva.+ Onani zonsezo.+ Kodi simudzazifotokozera ena?+ Kuyambira panopa ine ndikukuuzani zinthu zatsopano. Ndakuuzani zinthu zobisika zimene simunali kuzidziwa.+
7 Zinthu zimene ndikulengazi n’zatsopano, si zinthu zakale ayi. Ndi zinthu zimene simunazimvepo m’mbuyomu. Ndikuchita izi chifukwa munganene kuti, ‘Ifetu tinali kuzidziwa kale zimenezi.’+
8 “Komanso, inu simunafune kumva+ kapena kumvetsa zimenezi. Kuyambira pa nthawi imeneyo kupita m’tsogolo, simunatsegule khutu lanu. Pakuti ine ndinkadziwa ndithu kuti inu munali kuchita zachinyengo,+ ndipo mwatchedwa ‘wochimwa chibadwire.’+
9 Ndidzabweza mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa,+ ndipo chifukwa cha ulemerero wanga, ine ndidzadziletsa kuti ndisakuwonongeni.+
10 Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+ Ndinakusankhani pamene munali m’ng’anjo ya masautso.+
11 Ndithu, ndidzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa.+ Pakuti munthu angalekerere bwanji dzina lake likuipitsidwa?+ Ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina aliyense.+
12 “Ndimvere iwe Yakobo, iwe Isiraeli amene ndinakuitana. Ine sindinasinthe.+ Ine ndine woyamba.+ Ndinenso womaliza.+
13 Komanso dzanja langa linayala maziko a dziko lapansi,+ ndipo dzanja langa lamanja linatambasula kumwamba.+ Ndimafuulira maziko a dziko lapansi ndi kumwamba, kuti ziimirire.+
14 “Sonkhanani pamodzi anthu nonsenu kuti mumve.+ Ndani pakati pawo ananenapo zinthu zimenezi? Iye amene Yehova wamukonda+ adzachitira Babulo zimene akufuna.+ Dzanja lake lidzakhala pa Akasidi.+
15 Ineyo ndalankhula, komanso ndamuitana.+ Ndamubweretsa, ndipo ndidzachititsa kuti zochita zake zimuyendere bwino.+
16 “Bwerani pafupi ndi ine anthu inu. Mvetserani izi. Kuyambira pa chiyambi, ine sindinalankhulirepo m’malo obisika.+ Pamene zinthu zonenedwazo zinayamba kuchitika, ine ndinalipo.”
Tsopano Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine ndiponso watumiza mzimu wake.+
17 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.+
18 Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga!+ Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje,+ ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.+
19 Mbadwa zanu zochokera mkati mwa matupi anu zidzakhala ngati mchenga.+ Dzina lawo silidzatha kapena kuwonongedwa pamaso panga.”+
20 Tulukani m’Babulo anthu inu!+ Thawani m’manja mwa Akasidi.+ Nenani zimenezi ndi mfuu yachisangalalo kuti zimveke.+ Zineneni mokuwa mpaka zimveke kumalekezero a dziko lapansi.+ Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+
21 Iwo sanamve ludzu+ ngakhale pamene iye anawayendetsa m’chipululu.+ Iye anawatulutsira madzi pathanthwe. Anang’amba thanthwe kuti madzi atulukepo.”+
22 Yehova wanena kuti, “Oipa alibe mtendere.”+