Yesaya 62:1-12
62 Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala phee,+ ndipo chifukwa cha Yerusalemu+ sindidzakhala chete mpaka kulungama kwake kutakhala ngati kuwala,+ ndiponso mpaka chipulumutso chake chitakhala ngati muuni woyaka moto.+
2 “Mitundu ya anthu idzaona kulungama kwako+ mkazi iwe,+ ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.+ Iwe udzatchedwa ndi dzina latsopano+ limene pakamwa pa Yehova padzasankhe.
3 Udzakhala chisoti chokongola m’dzanja la Yehova,+ ndiponso chisoti chachifumu m’dzanja la Mulungu wako.
4 Sudzatchedwanso mkazi wosiyidwa mpaka kalekale+ ndipo dziko lako silidzatchedwanso labwinja.+ Koma iweyo dzina lako lidzakhala “Ndimakondwera Naye,”+ ndipo dziko lako lidzatchedwa “Mkazi Wokwatiwa.” Pakuti Yehova adzakondwera nawe ndipo dziko lako lidzakhala ngati mkazi wokwatiwa.+
5 Pakuti monga momwe mnyamata amatengera namwali kuti akhale mkazi wake, ana ako aamuna adzakutenga kuti ukhale mkazi wawo.+ Monga momwe mkwati amakhalira wachimwemwe chifukwa cha mkwatibwi,+ Mulungu wako adzakhala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe.+
6 Iwe Yerusalemu, ine ndaika alonda pamakoma a mpanda wako.+ Nthawi zonse, tsiku lonse lathunthu ndi usiku wonse wathunthu, iwo asakhale chete.+
“Inu amene mukutchula dzina la Yehova,+ musakhale chete.+
7 Musaleke kumukumbutsa mpaka atakhazikitsa Yerusalemu monga chinthu chofunika kutamandidwa padziko lapansi.”+
8 Yehova walumbira ndi dzanja lake lamanja+ ndiponso ndi mkono wake wamphamvu+ kuti: “Sindidzaperekanso mbewu zanu kwa adani anu ngati chakudya,+ ndipo alendo sadzamwanso vinyo wanu watsopano+ amene munachita kumuvutikira.
9 Koma anthu amene anakolola mbewuzo ndi amene adzazidye, ndipo adzatamanda Yehova. Amene anasonkhanitsa vinyoyo ndi amene adzamumwe m’mabwalo anga oyera.”+
10 Tulukani! Tulukani pazipata anthu inu. Lambulani njira yodutsa anthu.+ Konzani msewu. Ukonzeni ndithu. Chotsanimo miyala.+ Akwezereni chizindikiro anthu a mitundu yosiyanasiyana.+
11 Taonani! Yehova wachititsa kuti mawu awa amveke mpaka kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi:+ “Anthu inu, uzani mwana wamkazi wa Ziyoni+ kuti, ‘Taona! Chipulumutso chako chikubwera.+ Taona! Mphoto imene iye akufuna kupereka ili ndi iyeyo,+ ndipo malipiro amene akufuna kupereka ali pamaso pake.’”+
12 Iwo adzatchedwa anthu oyera,+ owomboledwa ndi Yehova.+ Iweyo udzatchedwa “Mzinda Umene Anaufunafuna,” “Mzinda Umene Sanausiyiretu.”+