Yesaya 10:1-34
10 Tsoka kwa amene akukhazikitsa malamulo oipa,+ ndi kwa amene amangokhalira kulemba malamulo obweretsa mavuto kwa anthu.
2 Iwo amachita zimenezi n’cholinga choti asamvetsere mlandu wa anthu onyozeka ndiponso kuti anthu anga osautsika awalande chilungamo.+ Amateronso kuti atenge akazi amasiye ngati katundu wolanda ndiponso kuti atenge ana amasiye.*+
3 Kodi anthu inu mudzatani pa tsiku limene adzatembenukire kwa inu+ ndi kukubweretserani chiwonongeko chochokera kutali?+ Mudzathawira kwa ndani kuti akuthandizeni+ ndipo ulemerero wanu mudzausiya kuti?+
4 Palibe chimene mudzachite, koma mudzagwada pakati pa akaidi ndiponso muzidzagwa pakati pa anthu amene aphedwa.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
5 “Eya! Msuri+ ndiye ndodo ya mkwiyo wanga+ komanso chikwapu chosonyezera ukali wanga chimene chili m’dzanja lake.
6 Ndidzamutumiza kuti akalimbane ndi mtundu wopanduka,+ ndipo ndidzamulamula kuti akalimbane ndi anthu amene andikwiyitsa. Ndidzamuuza+ kuti akalande zinthu zambiri, akatenge katundu wambiri, ndiponso akapondeponde anthuwo ngati matope a mumsewu.+
7 Ngakhale iye atakhala kuti si wotero, adzafunabe kuchita zimenezi. Ngakhale mtima wake utakhala kuti si wotero, adzakonza zoti achite zimenezi, chifukwa chakuti mumtima mwake amaganiza zowononga+ ndiponso zoti awonongeretu mitundu yambiri.+
8 Pakuti iye adzanena kuti, ‘Kodi akalonga anga si mafumunso?+
9 Kodi Kalino+ sali ngati Karikemisi?+ Kodi Hamati+ sali ngati Aripadi?+ Kodi Samariya+ sali ngati Damasiko?+
10 Nthawi iliyonse imene dzanja langa lafikira maufumu olambira milungu yopanda phindu, omwe zifaniziro zawo zogoba n’zambiri kuposa zimene zili ku Yerusalemu ndi ku Samariya,+
11 kodi sizidzachitika kuti monga momwe ndidzachitire kwa Samariya ndi kwa milungu yake yopanda phindu,+ ndi mmenenso ndidzachitire kwa Yerusalemu ndi kwa mafano ake?’+
12 “Yehova akadzatsiriza ntchito yake yonse m’phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu, ndidzalanga mfumu ya Asuri chifukwa cha zipatso za mwano wa mumtima mwake ndiponso chifukwa cha kudzikuza kwa maso ake onyada.+
13 Pakuti iye wanena kuti, ‘Ndi mphamvu za dzanja langa ndiponso ndi nzeru zanga, ndidzachitapo kanthu+ chifukwa ndine wodziwa zinthu. Ndidzachotsa malire a mitundu ya anthu,+ ndipo zinthu zimene anasunga ndidzazilanda.+ Monga munthu wamphamvu, ndidzagwetsa anthu okhala mmenemo.+
14 Dzanja langa+ lidzafikira chuma+ cha mitundu ya anthu ngati likupisa m’chisa. Ngati mmene munthu amatengera mazira amene asiyidwa, ine ndidzatenga dziko lonse lapansi. Sipadzakhala aliyense wokupiza mapiko ake kapena wotsegula pakamwa pake, kapenanso wolira ngati mbalame.’”
15 Kodi nkhwangwa ingadzikuze kuposa munthu amene akuigwiritsa ntchito? Kapena kodi chochekera matabwa chingadzikweze kuposa munthu amene akuchigwiritsa ntchito? Kodi chikwapu chinganyamule munthu amene wachinyamula m’mwamba, ndiponso kodi ndodo inganyamule m’mwamba munthu amene si mtengo?+
16 Chotero Ambuye woona, Yehova wa makamu azidzatumizira anthu ake* onenepa nthenda yowondetsa,+ ndipo pansi pa ulemerero wake pazidzangoyaka, ngati kuyaka kwa moto.+
17 Kuwala kwa Isiraeli+ kudzasanduka moto+ ndipo Woyera wake adzasanduka lawi la moto.+ Iye adzayaka n’kunyeketsa udzu wake* ndi zitsamba zake zaminga+ pa tsiku limodzi.
18 Mulungu adzathetseratu ulemerero wa nkhalango yake* ndi wa munda wake wa zipatso,+ ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuonda.+
19 Mitengo yotsala ya m’nkhalango mwake idzakhala yochepa kwambiri, moti kamnyamata kadzatha kulemba chiwerengero chake.+
20 M’tsiku limenelo, otsala a Isiraeli+ ndi opulumuka a nyumba ya Yakobo sadzadaliranso yemwe akuwamenya,+ koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova, Woyera wa Isiraeli.+
21 Otsala ochepa adzabwerera.* Otsala a Yakobo adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.+
22 Pakuti iwe Isiraeli, ngakhale anthu ako atakhala ngati mchenga wa kunyanja,+ otsala ochepa okha pakati pawo ndi amene adzabwerere.+ Chiwonongeko+ chimene Mulungu wakonzera anthu awa chidzabwera mwachilungamo ngati madzi osefukira,+
23 chifukwa chakuti Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabweretsa chiwonongeko+ ndi chiweruzo chokhwima pakatikati pa dziko lonselo.+
24 Chotero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa,+ wanena kuti: “Anthu anga amene mukukhala m’Ziyoni,+ musachite mantha chifukwa cha Msuri amene anali kukukwapulani ndi chikwapu+ ndiponso kukumenyani ndi ndodo, ngati mmene Iguputo anali kuchitira.+
25 Pakuti pakangodutsa kanthawi kochepa, kudzudzulako+ kudzatha ndipo mkwiyo wanga udzawayakira, moti adzatha.+
26 Yehova wa makamu adzam’kwapula ndi chikwapu+ ngati mmene anagonjetsera Midiyani pathanthwe la Orebi.+ Ndodo yake idzakhala panyanja+ ndipo adzaikweza m’mwamba ngati mmene anachitira ndi Iguputo.+
27 “M’tsiku limenelo, katundu wake adzachoka paphewa panu,+ ndipo goli lake lidzachoka m’khosi mwanu.+ Golilo lidzathyoledwa+ chifukwa cha mafuta.”
28 Iye waukira Ayati.+ Wadutsa ku Migironi. Waika katundu wake ku Mikimasi.+
29 Wadutsa powolokera mtsinje. Usiku agona ku Geba.+ Rama+ wanjenjemera ndipo Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, wathawa.
30 Iwe mwana wamkazi wa Galimu,+ fuula kwambiri. Khala tcheru, iwe Laisa. Iwenso Anatoti wosautsika, khala tcheru!+
31 Madimena wathawa. Anthu okhala ku Gebimu abisala.
32 Kukadali masana, iye aima ku Nobu.+ Ndi dzanja lake, iye akuopseza phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri limene pali Yerusalemu.+
33 Taonani! Ambuye woona, Yehova wa makamu, akuthyola nthambi ndipo zikugwa ndi chimkokomo.+ Nthambi zitalizitali zikudulidwa, ndipo zam’mwamba zatsitsidwa.+
34 Iye wadula ndi nkhwangwa zitsamba zowirira za m’nkhalango, ndipo wamphamvu adzagwetsa mitengo ya ku Lebanoni.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”