Yesaya 27:1-13

27  M’tsiku limenelo, Yehova+ adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa,+ lalikulu ndi lochititsa mantha kupha Leviyatani,*+ njoka yokwawa mwamyaa!+ Ndithu adzapha Leviyatani, njoka yoyenda mothamanga ndi mokhotakhota, ndipo adzapha chinjoka chachikulu chokhala m’nyanja.+  M’tsiku limenelo anthu inu mudzaimbire mkaziyo+ kuti: “Iwe ndiwe munda wa mpesa+ wotulutsa vinyo wathovu.  Ine Yehova ndine mlonda wa mundawo.+ Ndizidzauthirira nthawi zonse.+ Ndizidzaulondera usana ndi usiku kuti wina aliyense asauwononge.+  Ndaleka kumukwiyira.+ Munthu wina akaika zitsamba zaminga ndi udzu pamaso panga,+ ndidzazipondaponda ndi kuzitentha nthawi imodzi ndipo ndidzamenyana naye.+  Apo ayi, iye athawire kumalo anga achitetezo. Akhazikitse mtendere ndi ine. Iye akhazikitse mtendere ndi ine.”+  M’masiku amene akubwerawo, Yakobo adzamera mizu n’kukhala wamphamvu ngati mtengo. Isiraeli+ adzakhala ngati mtengo waukulu wa maluwa ambiri. Iwo adzabereka zipatso panthaka ya dziko lonse lapansi.+  Kodi iye akufunikira kumenyedwa ngati mmene akumenyedweramu? Kapena kodi iye akufunikira kuphedwa ngati mmene anthu ake akuphedweramu?+  Udzalimbana naye ndi mfuu yoopseza pomuthamangitsa. Iye adzamuthamangitsa ndi mphepo yake yamphamvu m’tsiku la mphepo ya kum’mawa.+  Chotero zolakwa za Yakobo zidzaphimbidwa mwa njira imeneyi.+ Zimenezi zidzachitika akadzachotsa tchimo lakelo,+ ndiponso akadzasandutsa miyala yonse ya paguwa lansembe kukhala miyala yofewa kwambiri yonyenyekanyenyeka, moti mizati yopatulika+ ndi maguwa ofukizirapo zonunkhira sizidzamangidwanso.+ 10  Pakuti mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri udzatsala wokhawokha. Malo odyetserako ziweto adzakhala opanda kanthu ndipo adzasiyidwa ngati chipululu.+ Kumeneko mwana wa ng’ombe azidzadya msipu ndipo azidzagona pansi. Iye adzadya nthambi zake.+ 11  Tinthambi take tikadzauma, akazi obwera kumeneko adzatithyola n’kutiyatsa.+ Pakuti anthuwo si omvetsa zinthu.+ N’chifukwa chake yemwe anawapanga sadzawachitira chifundo, ndipo yemwe anawaumba sadzawakomera mtima.+ 12  Inu ana a Isiraeli, monga momwe munthu amathyolera zipatso mumtengo n’kuzisonkhanitsa+ pamodzi chimodzi ndi chimodzi, Yehova adzakusonkhanitsani inu+ amene mwamwazikana m’dera loyambira ku Mtsinje*+ mpaka kukafika kuchigwa* cha Iguputo.+ 13  M’tsiku limenelo kudzalira lipenga lomveka kutali.+ Ndiyeno anthu amene akuwonongeka m’dziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana m’dziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira+ Yehova m’phiri loyera ku Yerusalemu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “ng’ona.” Mwina imeneyi inali ng’ona kapena chilombo cham’nyanja.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.