Yesaya 8:1-22

8  Yehova anandiuza kuti: “Tenga cholembapo chachikulu+ ndipo ulembepo ndi cholembera wamba, kuti: ‘Maheri-salala-hasi-bazi.’*  Ndikufuna mboni zokhulupirika kuti zindichitire umboni.+ Mbonizo zikhale wansembe Uriya+ ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.”  Kenako ndinakhala malo amodzi ndi mneneri wamkazi ndipo iye anatenga pakati. Pambuyo pake anabereka mwana wamwamuna.+ Tsopano Yehova anandiuza kuti: “Um’patse dzina lakuti Maheri-salala-hasi-bazi,  popeza mwanayo asanadziwe kuitana+ kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ anthu adzanyamula chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya n’kupita naye pamaso pa mfumu ya Asuri.”+  Yehova anandiuzanso kuti:  “Popeza anthu awa akana+ madzi a ku Silowa+ amene amayenda pang’onopang’ono, ndipo atengeka+ ndi Rezini ndiponso mwana wa Remaliya,+  Yehova akuwabweretsera+ Mtsinje*+ wa madzi ambiri ndi amphamvu, womwe ndi mfumu ya Asuri+ ndi ulemerero wake wonse.+ Iyo idzadzaza timitsinje take tonse n’kusefukira mpaka m’mphepete mwa mitsinje yake yonse,  ndipo idzadutsa mu Yuda yense. Idzadutsa ngati madzi osefukira,+ ndipo idzafika mpaka m’khosi.+ Idzatambasula mapiko ake+ mpaka m’lifupi mwa dziko lako, iwe Emanueli.”+  Inu mitundu ya anthu, vulazani anthu, koma inuyo muphwanyidwaphwanyidwa. Inu nonse amene muli kumalekezero a dziko lapansi, tamverani.+ Nyamulani zida zankhondo+ koma muphwanyidwaphwanyidwa.+ Nyamulani zida zankhondo koma muphwanyidwaphwanyidwa. 10  Konzani zochita, koma zidzalephereka.+ Nenani zoti anthu achite, koma sizidzachitidwa, chifukwa Mulungu ali nafe.+ 11  Dzanja lamphamvu la Yehova linali pa ine, ndipo pofuna kuti andipatutse kuti ndisayende panjira ya anthu awa, iye anati: 12  “Anthu inu musamanene kuti: ‘Chiwembu!’ pa nkhani zonse zimene anthu awa amanena kuti: ‘Chiwembu!’+ Musamaope zimene iwo amaopa ndipo musamanjenjemere nazo.+ 13  Yehova wa makamu ndi amene muyenera kumuona kuti ndi woyera,+ ndipo iyeyo ndi amene muyenera kumuopa.+ Iye ndi amene ayenera kukuchititsani kunjenjemera.”+ 14  Iye akhale ngati malo opatulika.+ Koma kwa nyumba zonse ziwiri za Isiraeli, iye akhale ngati mwala wopunthwitsa ndiponso ngati mwala wokhumudwitsa.+ Akhalenso ngati msampha ndi khwekhwe kwa anthu okhala mu Yerusalemu.+ 15  Anthu ambiri pakati pawo adzapunthwa n’kugwa ndi kuthyoka, ndipo adzakodwa n’kugwidwa.+ 16  Kulunga umboni.+ Mata lamulo pakati pa ophunzira anga.+ 17  Ine ndiziyembekezera Yehova,+ amene wabisira nkhope yake nyumba ya Yakobo,+ ndipo ndithu ndiziyembekezera iyeyo.+ 18  Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa+ tili ngati zizindikiro+ ndiponso ngati zozizwitsa mu Isiraeli, zochokera kwa Yehova wa makamu amene amakhala m’phiri la Ziyoni.+ 19  Akakuuzani anthu inu kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu+ kapena kwa anthu amene ali ndi mzimu wolosera zam’tsogolo, omwe amalira ngati mbalame+ ndiponso amalankhula motsitsa mawu,” kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake?+ Kodi tizifunsira kwa anthu akufa kuti athandize anthu amoyo?+ 20  Funsirani kwa lamulo ndi umboni!+ Ndithu iwo azingonena zinthu zogwirizana ndi mawu amenewa,+ koma sadzaona kuwala kwa m’bandakucha.+ 21  Aliyense adzadutsa m’dzikolo akuzunzika ndiponso ali ndi njala.+ Chifukwa chakuti ali ndi njala ndiponso wakwiya, adzatukwana mfumu yake ndi Mulungu+ wake ndipo azidzayang’ana kumwamba. 22  Iye adzayang’ana padziko lapansi koma adzangoonapo kuzunzika, mdima,+ kuda, nthawi zovuta ndi zakuda bii, zopanda kuwala.+

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza kuti, “Fulumira Iwe Zofunkha, kapena Kufulumirira Zofunkha. Iye Wabwera Mofulumira ku Zolanda.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.