Genesis 7:1-24

7  Pambuyo pake Yehova anauza Nowa kuti: “Lowa m’chingalawacho, iwe ndi banja lako,+ chifukwa iwe ndi amene ndakuona kuti ndiwe wolungama pakati pa m’badwo uwu.+  Pa nyama zilizonse zosadetsedwa utengepo zokwanira 7, yamphongo ndi yaikazi yake.+ Koma pa nyama zilizonse zodetsedwa utengepo ziwiri zokha, yamphongo ndi yaikazi yake.  Pa zolengedwa zilizonse zouluka m’mlengalenga, utengeponso zokwanira 7, chachimuna ndi chachikazi,+ kuti zisungike padziko lonse lapansi.+  Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse chimvula+ padziko lapansi kwa masiku 40, usana ndi usiku.+ Ndipo ndidzaseseratu chamoyo chilichonse padziko lapansi chimene ndinachipanga.”+  Choncho, Nowa anachita zonse motsatira zimene Yehova anamulamula.  Pamene chigumula chamadzi chinachitika padziko lapansi, Nowa anali ndi zaka 600.+  Pamenepo Nowa analowa m’chingalawacho, limodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake, ndi akazi a ana ake. Iwo analowamo madzi achigumula asanayambe.+  Nyama zilizonse zosadetsedwa, nyama zilizonse zodetsedwa, zolengedwa zilizonse zouluka, komanso zilizonse zokwawa pansi,+  zinalowa ziwiriziwiri m’chingalawa mmene munali Nowa, yamphongo ndi yaikazi, monga mmene Yehova analamulira Nowa. 10  Ndipo patapita masiku 7, madzi a chigumula anafika padziko lapansi. 11  M’chaka cha 600 cha moyo wa Nowa, m’mwezi wachiwiri,* pa tsiku la 17 la mweziwo, pa tsiku limeneli akasupe onse amadzi akuya* anaphulika ndipo zotsekera madzi akumwamba zinatseguka.+ 12  Ndiyeno chimvula chinakhuthuka padziko lapansi kwa masiku 40 usana ndi usiku.+ 13  Pa tsiku limeneli Nowa analowa m’chingalawacho. Analowa limodzi ndi ana ake, Semu, Hamu ndi Yafeti,+ ndiponso mkazi wake, ndi akazi atatu a ana akewo.+ 14  Iwo analowa pamodzi ndi nyama zakutchire zamtundu uliwonse,+ nyama zoweta zamtundu uliwonse, nyama zokwawa* pansi zamtundu uliwonse,+ zolengedwa zouluka zamtundu uliwonse,+ ndiponso mbalame zilizonse ndi zolengedwa zilizonse zamapiko.+ 15  Zamoyo zamtundu uliwonse, zokhala ndi mphamvu ya moyo+ m’thupi mwawo, zinali kupita ziwiriziwiri m’chingalawa mmene munali Nowa. 16  Zimene zinali kulowazo, zazimuna ndi zazikazi zamtundu uliwonse, zinalowa monga mmene Yehova anamulamulira Nowa. Kenako Yehova anatseka chitseko.+ 17  Chigumulacho chinapitirira padziko lapansi kwa masiku 40. Ndipo madzi anachulukirachulukira, moti anayamba kunyamula chingalawacho, mpaka chinali kuyandama pamwamba kwambiri kuchokera padziko lapansi. 18  Madziwo anapitirizabe kuwonjezeka koopsa padziko lapansi, ndipo chingalawachonso chinapitirizabe kuyandama pamwamba pa madzi.+ 19  Madziwo anawonjezeka kwambiri padziko lapansi moti anamiza mapiri onse ataliatali amene anali pansi pa thambo lonse.+ 20  Madziwo anakwera kwambiri kupitirira mapiri ataliataliwo ndi mikono 15.+ 21  Chotero zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, monga zolengedwa zouluka, nyama zoweta, nyama zakutchire, ndiponso tizilombo tonse tambirimbiri toyenda padziko lapansi, zinafa+ pamodzi ndi anthu onse.+ 22  Chilichonse chokhala ndi mpweya wa moyo* m’mphuno mwake, kutanthauza zonse zimene zinali pamtunda, zinafa.+ 23  Chotero, Mulungu anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi, kuyambira munthu mpaka nyama, zokwawa pansi mpaka zolengedwa zouluka m’mlengalenga, anazisesa zonse padziko lapansi.+ Koma Nowa yekha, pamodzi ndi amene anali naye limodzi m’chingalawacho, anapulumuka.+ 24  Ndipo madzi anamizabe dziko lapansi kwa masiku 150.

Mawu a M'munsi

“Mwezi wachiwiri” umene ukutchulidwa m’vesili unadzakhala mwezi wa 8 pakalendala yopatulika imene Yehova anapatsa Aisiraeli atatuluka m’dziko la Iguputo. Mwezi umenewu, wotchedwa Buli, unkayambira chapakati pa October n’kutha chapakati pa November. Onani Zakumapeto 13.
Mawu akuti “madzi akuya” m’vesili akutanthauza madzi akuthambo omwe analipo kuzungulira dziko lapansi. Madzi amenewa akutchulidwanso pa Ge 1:6, 7 kuti, ‘madzi . . . a pamwamba pa mlengalenga.’
Onani mawu a m’munsi pa Ge 1:24.
Onani Zakumapeto 4.