Genesis 41:1-57
41 Patapita zaka ziwiri zathunthu, Farao analota maloto.+ Analota kuti waimirira m’mbali mwa mtsinje wa Nailo.
2 Kenako iye anaona ng’ombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Ng’ombezo zinali zokongola m’maonekedwe ndi zonenepa, ndipo zinali kudya udzu wa m’mbali mwa mtsinjewo.+
3 Anaonanso ng’ombe zina 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailowo pambuyo pa zoyambazo. Zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda,+ ndipo zinaima pambali pa zinazo m’mbali mwa mtsinjemo.
4 Tsopano ng’ombe zonyansa ndi zowondazo zinayamba kudya ng’ombe 7 zooneka bwino ndi zonenepa zija.+ Kenako Farao anagalamuka.+
5 Koma Farao anagonanso n’kulota maloto ena. M’malotowa anaona ngala za tirigu 7 zikutuluka paphesi limodzi. Ngalazo zinali zokhwima ndi zazikulu bwino.+
6 Anaonanso ngala zina 7 zikutuluka pambuyo pa zoyambazo.+ Ngalazo zinali zonyala ndi zowauka ndi mphepo yakum’mawa.+
7 Ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zokhwima ndi zazikulu bwinozo.+ Kenako Farao anagalamuka, n’kuona kuti anali maloto.
8 Kutacha m’mawa, Farao anavutika kwambiri ndi maganizo.+ Chotero anaitanitsa ansembe onse amatsenga+ ndi amuna anzeru+ onse a mu Iguputo, n’kuwafotokozera maloto akewo.+ Koma palibe amene anatha kum’masulira Farao malotowo.
9 Kenako mkulu wa operekera chikho uja anauza Farao+ kuti: “Lero ndinene zolakwa zanga.+
10 Inuyo a Farao munatikwiyira kwambiri ife atumiki anu.+ Ineyo ndi mkulu wa ophika mkate munatitsekera m’ndende ya kunyumba kwa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+
11 Kundendeko tonse awiri tinalota maloto usiku umodzi. Aliyense analota maloto ake okhala ndi tanthauzo lakelake.+
12 Tinalinso ndi mnyamata wina wachiheberi+ kumeneko. Iyeyo anali wantchito wa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ Titamufotokozera maloto athu,+ anatimasulira matanthauzo ake. Aliyense anam’masulira malinga ndi maloto amene analota.
13 Zimene anamasulirazo n’zimene zinachitikadi. Ineyo ndinabwezeretsedwa pa ntchito,+ koma mnzangayo anapachikidwa.”+
14 Tsopano Farao anatuma anthu kukatenga Yosefe+ kundendeko,+ kuti abwere naye mofulumira. Choncho Yosefeyo anameta bwinobwino,+ kenako anasintha zovala+ n’kukaonekera pamaso pa Farao.
15 Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: “Ine ndalota maloto, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kuwamasulira. Koma ndamva kuti iweyo ukamva maloto umatha kumasulira.”+
16 Pamenepo Yosefe anayankha Farao kuti: “Yemwe anene uthenga wokhudza moyo wa inu Farao ndi Mulungu osati ine.”+
17 Farao anafotokozera Yosefe kuti: “Ndinalota nditaimirira m’mbali mwa mtsinje wa Nailo.
18 Ndiyeno ndinaona ng’ombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Ng’ombezo zinali zonenepa ndi zooneka bwino, ndipo zinayamba kudya udzu wa m’mbali mwa mtsinjewo.+
19 Kenako ndinaonanso ng’ombe zina 7 zikutuluka mumtsinjewo pambuyo pa zoyamba zija. Ng’ombe zimenezi zinali zamaonekedwe onyansa ndi zowonda.+ Sindinaonepo ng’ombe zonyansa ngati zimenezo m’dziko lonse la Iguputo.
20 Ng’ombe zowonda ndi zonyansazo zinayamba kudya ng’ombe 7 zonenepa zija.+
21 Koma zitadya zinzakezo, mimba za ng’ombe zowondazo sizinaoneke kuti mwalowa kanthu, popeza ng’ombezo zinaonekabe zowonda ngati poyamba.+ Pamenepo ndinagalamuka.
22 “Kenako, ndinalotanso maloto ena. Ndinalota ngala 7 za tirigu, zokhwima ndi zooneka bwino, zikutuluka paphesi limodzi.+
23 Ndinaonanso ngala zina 7 zikutuluka pambuyo pa zoyamba zija. Zimenezi zinali zonyala ndi zowauka ndi mphepo yakum’mawa.+
24 Ndiyeno ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zooneka bwinozo.+ Malotowo ndinawafotokoza kwa ansembe amatsenga,+ koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kundimasulira.”+
25 Pamenepo Yosefe anauza Farao kuti: “Maloto anu awiriwo tanthauzo lake n’limodzi. Mulungu woona wakudziwitsani zimene adzachite.+
26 Ng’ombe 7 zonenepazo zikuimira zaka 7. Chimodzimodzinso, ngala 7 zooneka bwinozo zikuimira zaka 7. Malotowa ndi amodzi.
27 Ng’ombe 7 zowonda ndi zonyansazo, zimene zinatuluka pambuyo pa zoyamba zija, zikuimira zaka 7. Koma ngala 7 zimenezo, zopanda kanthu ndi zowauka ndi mphepo yakum’mawa,+ zidzakhala zaka 7 za njala.+
28 Choncho, monga ndinakuuzirani inu Farao, Mulungu woona wakuonetsani zimene adzachita.+
29 “Kukubwera zaka 7 zimene kudzakhala chakudya chambiri m’dziko lonse la Iguputo.
30 Koma pambuyo pa zaka zimenezo, ndithudi padzabwera zaka 7 za njala. Chakudya chonse chochuluka chija m’dziko la Iguputo sichidzakumbukika m’pang’ono pomwe, ndipo njalayo idzawononga dziko lonse.+
31 Chifukwa cha njalayo, sikudzadziwika kuti m’dzikoli pa nthawi ina munali chakudya chambiri, pakuti njalayo idzakhaladi yoopsa kwambiri.
32 Popeza kuti inu mwalota kawiri malotowa, ndiye kuti Mulungu woona watsimikiza mtima kuchitadi zimenezi,+ ndipo azichita posachedwapa.+
33 “Tsopano mufunefune munthu wozindikira ndi wanzeru, ndipo mumuike kukhala woyang’anira dziko la Iguputo.+
34 Muike akapitawo m’dziko lino,+ ndipo iye azitenga gawo limodzi mwa magawo asanu a chakudya cha dziko la Iguputo pa zaka 7 za zokolola zambiri.+
35 Mwa lamulo lanu, m’zaka zimene kudzakhale chakudya chambiri, akapitawo amenewo azidzasonkhanitsira tirigu yense m’mizinda+ ndi kum’sunga bwino.
36 Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha dzikoli pa zaka 7 za njala imene idzagwe m’dziko la Iguputo,+ kuti anthu ndi ziweto asadzawonongeke ndi njalayo.”+
37 Zimene Yosefe ananena zinakomera Farao ndi antchito ake onse.+
38 Pamenepo Farao anafunsa antchito ake kuti: “Kodi pangapezekenso munthu wina wonga uyu, wokhala ndi mzimu wa Mulungu?”+
39 Kenako Farao anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziwitsa zonsezi,+ palibenso munthu wina wozindikira ndi wanzeru ngati iwe.+
40 Iweyo ukhala woyang’anira nyumba yanga,+ ndipo anthu anga onse azimvera iweyo.+ Ine ndikhala wokuposa pa ufumu wokha.”+
41 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Tsopano ndikukuika kukhala woyang’anira dziko lonse la Iguputo.”+
42 Atatero, Farao anavula mphete yake yachifumu+ kudzanja lake, n’kuiveka kudzanja la Yosefe. Anamuvekanso malaya amtengo wapatali, ndi tcheni chagolide m’khosi mwake.+
43 Ndiponso, anamukweza pagaleta* lachiwiri laulemu limene anali nalo,+ ndipo anthu anali kufuula patsogolo pake kuti, “A·vrékh!”* posonyeza kuti ndi wamkulu m’dziko lonse la Iguputo.
44 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Farao ndine, koma popanda chilolezo chako, palibe wina aliyense angachite* kanthu m’dziko lonse la Iguputo.”+
45 Farao atatero, anapatsa Yosefe dzina lakuti, Zafenati-panea.* Anam’patsanso mkazi dzina lake Asenati.+ Mtsikanayu anali mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni.+ Pamenepo Yosefe anayamba kuyendera dziko la Iguputo.+
46 Yosefe anali ndi zaka 30+ pamene anayamba kutumikira Farao, mfumu ya Iguputo.
Kenako anachoka pamaso pa Farao n’kuyamba kuyendera dziko lonse la Iguputo.
47 Pa zaka zonse 7 za chakudya chamwanaalirenji, dzikolo linabereka chakudya chambiri.+
48 Pa zaka 7 zimenezo, Yosefe anasonkhanitsa chakudya chonse chimene anakolola m’dziko lonse la Iguputo, n’kuchisunga m’mizinda.+ Chakudya chonse chochokera m’minda yonse yozungulira mzinda uliwonse, anachisunga pakati pa mzindawo.+
49 Yosefe anapitiriza kusunga tirigu, mpaka anachuluka kwambiri+ ngati mchenga wa kunyanja. Tiriguyo anachuluka kwadzaoneni, moti sanathenso kumamuyeza chifukwa cha kuchuluka kwake.+
50 Chaka cha njala chisanafike, Yosefe anakhala ndi ana aamuna awiri,+ amene anam’berekera mkazi wake Asenati, mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.
51 Mwana woyambayo Yosefe anamutcha dzina lakuti Manase,*+ chifukwa anati, “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse, ndi nyumba yonse ya bambo anga.”+
52 Wachiwiriyo anamutcha Efuraimu,*+ chifukwa anati, “Mulungu wandipatsa ana m’dziko la masautso anga.”+
53 Kenako zaka 7 zosunga chakudya m’dziko la Iguputo zinatha.+
54 Tsopano zaka 7 za njala zinayamba, monga Yosefe ananenera.+ Njalayo inafalikira m’mayiko onse, koma dziko lonse la Iguputo linali ndi chakudya.+
55 Potsirizira pake, njala ija inafalikira mpaka m’dziko lonse la Iguputo, ndipo anthu anayamba kulirira Farao kuti awapatse chakudya.+ Koma Farao anauza Aiguputo onse kuti: “Pitani kwa Yosefe! Zilizonse zimene akuuzeni, chitani zomwezo.”+
56 Njala ija inafalikira padziko lonse lapansi.+ Zitatero, Yosefe anayamba kutsegula nkhokwe zonse zimene zinali pakati pawo n’kuyamba kugulitsa chakudyacho kwa Aiguputo,+ chifukwa njalayo inali itakula kwambiri m’dziko la Iguputo.
57 Komanso, anthu a padziko lonse lapansi anayamba kubwera ku Iguputo kudzagula chakudya kwa Yosefe, pakuti njalayo inali itafika poipa kwambiri padziko lonse lapansi.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mawu olembedwa m’Chiheberi kuti “A·vrékh!” anatengedwa ku Chiiguputo, koma tanthauzo lenileni silinadziwikebe bwinobwino.
^ Mawu ake enieni, “palibe aliyense amene anganyamule dzanja lake kapena phazi lake.”
^ Kwa Aheberi, dzina lakuti “Zafenati-panea” linali kutanthauza “Wovumbula Zinthu Zobisika.”
^ Dzina lakuti “Manase” limatanthauza “Wochititsa Kuiwala,” ndiponso “Woiwalitsa.”
^ Dzina lakuti “Efuraimu” limatanthauza “Wobereka Mowirikiza,” ndiponso “Dziko Lachonde.”