Genesis 5:1-32
5 Tsopano nayi mbiri ya Adamu. M’tsiku limene Mulungu analenga Adamu, anam’panga iye m’chifaniziro cha Mulungu.+
2 Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Kenako, anawadalitsa ndi kuwatchula dzina lakuti Anthu,+ m’tsiku limene anawalenga.+
3 Adamu atakhala ndi moyo zaka 130, anabereka mwana wamwamuna m’chifaniziro chake, wofanana naye. Anamutcha dzina lake Seti.+
4 Adamu atabereka Seti, anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+
5 Chotero, masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalira.+
6 Seti atakhala ndi moyo zaka 105, anabereka Enosi.+
7 Atabereka Enosi, Seti anakhalabe ndi moyo zaka zina 807. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
8 Chotero, masiku onse a Seti anakwana zaka 912, kenako anamwalira.
9 Enosi atakhala ndi moyo zaka 90, anabereka Kenani.+
10 Atabereka Kenani, Enosi anakhalabe ndi moyo zaka zina 815. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
11 Chotero, masiku onse a Enosi anakwana zaka 905, kenako anamwalira.
12 Kenani atakhala ndi moyo zaka 70, anabereka Mahalalele.+
13 Atabereka Mahalalele, Kenani anakhalabe ndi moyo zaka zina 840. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
14 Chotero, masiku onse a Kenani anakwana zaka 910, kenako anamwalira.
15 Mahalalele atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Yaredi.+
16 Atabereka Yaredi, Mahalalele anakhalabe ndi moyo zaka zina 830. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
17 Chotero, masiku onse a Mahalalele anakwana zaka 895, kenako anamwalira.
18 Yaredi atakhala ndi moyo zaka 162, anabereka Inoki.+
19 Atabereka Inoki, Yaredi anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pazaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
20 Chotero, masiku onse a Yaredi anakwana zaka 962, kenako anamwalira.
21 Inoki atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Metusela.+
22 Atabereka Metusela, Inoki anayendabe ndi Mulungu woona kwa zaka 300. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
23 Chotero, masiku onse a Inoki anakwana zaka 365.
24 Inoki anayendabe+ ndi Mulungu woona.+ Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anam’tenga.+
25 Metusela atakhala ndi moyo zaka 187, anabereka Lameki.+
26 Atabereka Lameki, Metusela anakhalabe ndi moyo zaka zina 782. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
27 Chotero, masiku onse a Metusela anakwana zaka 969, kenako anamwalira.
28 Lameki atakhala ndi moyo zaka 182, anabereka mwana wamwamuna.
29 Mwanayo anamutcha dzina lakuti Nowa,+ ndipo anati: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.”+
30 Atabereka Nowa, Lameki anakhalabe ndi moyo zaka zina 595. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.
31 Chotero masiku onse a Lameki anakwana zaka 777, kenako anamwalira.
32 Nowa anakwanitsa zaka 500. Pambuyo pake iye anabereka Semu,+ Hamu+ ndi Yafeti.+