Genesis 18:1-33
18 Kenako Yehova anaonekera+ kwa Abulahamu pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure.+ Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu atakhala pansi pakhomo la hema wake masana dzuwa likutentha.+
2 Atakweza maso,+ anaona amuna atatu ataima chapatali ndi iye. Atawaona, ananyamuka pakhomo la hemayo n’kuthamanga kukakumana nawo. Atafika, anagwada n’kuwaweramira mpaka nkhope yake pansi.+
3 Ndiyeno anati: “Yehova, ngati mungandikomere mtima, chonde, musangondipitirira ine kapolo wanu.+
4 Mumweko madzi pang’ono, ndiponso tikusambitseni mapazi.+ Kenako, mupumeko pansi pa mtengo.+
5 Popeza mwadzera njira yodutsa kwa kapolo wanu, mundilole ndikukonzereni kachakudya kuti mutsitsimutse mitima yanu.+ Mukatero mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.”
6 Chotero Abulahamu anathamangira kwa Sara n’kumuuza kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu ya seya,* uukande, ndipo upange makeke ozungulira.”+
7 Kenako, Abulahamu anathamangira kumene kunali ziweto, n’kutengako ng’ombe yaing’ono yamphongo yonona. Atatero, anaipereka kwa wantchito wake, ndipo iye anaikonza mwamsanga.+
8 Ndiyeno Abulahamu anatenga mafuta a mkaka, mkaka, ndi ng’ombe yaing’ono yamphongo imene anakonza ija, n’kukaziika pamene panali alendowo.+ Pamene iwo anali kudya atakhala pansi pa mtengo, iye anaimirira chapafupi.+
9 Tsopano alendowo anati: “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Ali m’hemamu!”+
10 Ndiyeno mmodzi wa iwo anapitiriza kuti: “Ndidzabweranso kwa iwe ndithu chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Pa nthawiyi n’kuti Sara akumvetsera, ali pakhomo la hemayo. Ndipo mlendoyo anali atafulatira hemayo.
11 Abulahamu ndi Sara anali okalamba ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Sara anali atasiya kusamba.+
12 Chotero Sara anayamba kuseka mumtima mwake+ kwinaku akunena kuti: “Kodi mmene ndatheramu, zoona ndingakhaledi ndi chisangalalo chimenechi, komanso ndi mmene mbuyanga wakalambiramu?”+
13 Ndiyeno Yehova anafunsa Abulahamu kuti: “N’chifukwa chiyani Sara waseka, kuti, ‘Kodi n’zoona kuti ineyo, mmene ndakalambiramu, ndingaberekedi mwana?’+
14 Kodi pali chosatheka ndi Yehova?+ Pa nthawi yoikidwiratu ndidzabweranso kwa iwe chaka chamawa. Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
15 Koma Sara pochita mantha anakana kuti: “Sindinaseketu ine ayi!” Koma mlendoyo anati: “Ayi! Unaseka iwe.”+
16 Pambuyo pake amunawo anaimirira ndi kuyang’ana ku Sodomu,+ ndipo Abulahamu ananyamuka nawo n’kuwaperekeza.+
17 Kenako Yehova anati: “Kodi ndingamubisire Abulahamu zimene ndikufuna kuchita?+
18 Iyetu adzakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso* kudzera mwa iye.+
19 Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake kuyenda m’njira ya Yehova ndi kuchita chilungamo.+ Awaphunzitse kutero, kuti Yehova adzakwaniritse kwa Abulahamu zimene ananena zokhudza iye.”+
20 Chotero Yehova anati: “Kudandaula kokhumudwa chifukwa cha Sodomu ndi Gomora+ kwamveka kwambiri, ndipo tchimo lawo n’lalikulu kwambiri.+
21 Ndiye nditsikirako kuti ndikaone ngati akuchitadi monga mwa kudandaula kumene ndamva ndiponso ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho. Ndikufuna ndidziwe zimenezi.”+
22 Pamenepo, amunawo anatembenuka kulowera ku Sodomu, koma Yehova+ anatsala ataima ndi Abulahamu.+
23 Ndiyeno Abulahamu anamuyandikira n’kuyamba kumufunsa kuti: “Kodi zoona mungawononge olungama pamodzi ndi oipa?+
24 Bwanji ngati mumzindamo mutapezeka anthu olungama 50, kodi muwawonongabe? Kodi simukhululukira mzindawo chifukwa cha olungama 50 amenewo?+
25 Simungachite zimenezo, kupha munthu wolungama limodzi ndi woipa. Sizingatheke kuti wolungama aone zofanana ndi woipa.+ Simungachite zimenezo ayi.+ Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?”+
26 Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Ngati ndingapeze anthu olungama 50 mu Sodomu, ndikhululukira mzinda wonsewo chifukwa cha iwo.”+
27 Koma Abulahamu anapitiriza kuti: “Pepanitu, musaone ngati ndatha mantha kulankhula kwa Yehova pamene ndine fumbi ndi phulusa.+
28 Nanga ngati pa olungama 50 aja pataperewera asanu, kodi muwononga mzinda wonsewo chifukwa choti paperewera anthu asanu?” Pamenepo iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo ndikapezamo olungama 45.”+
29 Koma iye anafunsabe kuti: “Nanga mutapezeka 40?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga chifukwa cha 40 amenewo.”
30 Koma iye anapitiriza kuti: “Chonde Yehova, musandipsere mtima,+ koma ndiloleni ndilankhulebe.+ Nanga atapezeka 30?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga ndikapezamo 30.”
31 Iye anapitirizabe kuti: “Chonde, pepani musaone ngati ndatha mantha kulankhula kwa Yehova.+ Nanga mutapezeka 20?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 20 amenewo.”+
32 Potsirizira pake anati: “Chonde Yehova, pepani, musandipsere mtima,+ tandilolani ndilankhule komaliza kokhaka.+ Nanga mutapezeka 10?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 10 amenewo.”+
33 Ndiyeno Yehova+ atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, ananyamuka n’kumapita, ndipo Abulahamu anabwerera kunyumba kwake.
Mawu a M'munsi
^ Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita pafupifupi 8.