Genesis 28:1-22
28 Choncho, Isaki anaitana Yakobo ndipo anamudalitsa n’kumulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+
2 Nyamuka, pita ku Padana-ramu kunyumba ya Betuele bambo a mayi ako. Kumeneko ukatenge mkazi pakati pa ana a Labani mlongo wa mayi ako.+
3 Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+
4 Adzakupatsa iwe ndi mbewu zako+ madalitso amene analonjeza Abulahamu,+ kuti udzakhale mwini dziko limene ukukhalamo ngati mlendo,+ limene Mulungu anapatsa Abulahamu.”+
5 Chotero Isaki anatumiza Yakobo, ndipo iye ananyamuka ulendo wopita ku Padana-ramu. Anapita kwa Labani mwana wa Betuele, Msiriya.+ Labaniyo anali mlongo wake wa Rabeka,+ mayi ake a Yakobo ndi Esau.+
6 Esau anaona kuti Isaki wadalitsa Yakobo, ndiponso kuti wam’tumiza ku Padana-ramu kukatenga mkazi kumeneko. Anaona kuti pomudalitsa anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.”+
7 Anaonanso kuti Yakobo wamvera bambo ake ndi mayi ake ndipo wapita ku Padana-ramu.+
8 Pamenepo Esau anazindikira kuti, Isaki bambo ake, anali kuipidwa nawo ana aakazi a ku Kanani.+
9 Chotero Esau anapita kwa Isimaeli* n’kukatengako mkazi kuwonjezera pa akazi amene anali nawo.+ Mkaziyo dzina lake anali Mahalati, ndipo anali mlongo wake wa Nebayoti. Mahalati anali mwana wa Isimaeli, mwana wa Abulahamu.
10 Yakobo anapitiriza ulendo wake wochokera ku Beere-seba kupita ku Harana.+
11 Kenako anafika pamalo ena n’kuganiza zogona, popeza dzuwa linali litalowa. Chotero, anatenga mwala umodzi pamalopo n’kuuchita mtsamiro, n’kugona pamenepo.+
12 Kenako anayamba kulota.+ M’malotowo anaona makwerero ochokera pansi mpaka kumwamba. Angelo a Mulungu anali kukwera ndi kutsika pamakwereropo.+
13 Pamwamba pa makwererowo anaonapo Yehova, amene anamuuza kuti:+
“Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abulahamu kholo lako, ndi Mulungu wa Isaki.+ Dziko limene wagonapoli ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako.+
14 Mbewu yako ndithu idzachuluka ngati mchenga wa padziko lapansi,+ ndipo ana ako adzafalikira kumadzulo, kum’mawa, kumpoto ndi kum’mwera.+ Komanso kudzera mwa iwe ndi mwa mbewu yako, mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso*+ ndithu.
15 Ine ndili nawe ndipo ndikuyang’anira pa ulendo wako wonse, kufikira ndidzakubwezera kumalo ano.+ Sindidzakusiya kufikira nditachitadi zimene ndanena kwa iwe.”+
16 Kenako Yakobo anagalamuka ku tulo take n’kunena kuti: “Ndithudi Yehova ali pamalo pano, koma ine sindinadziwe.”
17 Iye anachita mantha n’kunenanso kuti:+ “Malo ano ndi oopsa!+ Ndithu malo ano ndi nyumba ya Mulungu,+ ndiponso ndi khomo la kumwamba.”
18 Tsopano Yakobo anadzuka m’mawa kwambiri, n’kutenga mwala umene anautsamira uja, n’kuuimika monga mwala wachikumbutso. Atatero anauthira mafuta pamwamba.+
19 Kenako, malowo anawatcha Beteli.+ Koma dzina lakale la mzindawo linali Luzi.+
20 Yakobo analonjeza+ kuti: “Ndithu ngati Mulungu adzakhalabe nane n’kundisungabe pa ulendo wangawu, ndiponso ngati adzandipatsadi chakudya ndi zovala,+
21 komanso ngati ndidzabwereradi mwamtendere kunyumba ya bambo anga, pamenepo Yehova adzakhala atasonyezadi kuti ndi Mulungu wanga.+
22 Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatsa, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi chake.”+