Genesis 23:1-20
23 Sara anakhala ndi moyo zaka 127. Zimenezi ndizo zinali zaka za moyo wake.+
2 Sara anamwalirira ku Kiriyati-ariba,+ kapena kuti ku Heburoni,+ m’dziko la Kanani.+ Pamenepo Abulahamu analowa muhema kukamulira Sara.
3 Ndiyeno Abulahamu anachoka pamene panali mtembo wa mkazi wake n’kupita kukalankhula ndi ana a Heti,+ kuti:
4 “Ine ndinadzakhala kwanu kuno ngati mlendo.+ Choncho ndigawireniko malo kuti ndikhale ndi manda angaanga, ndiikemo mkazi wanga.”*+
5 Ana a Heti anayankha Abulahamu kuti:
6 “Timvereni mbuyathu.+ Inu ndinu mtsogoleri woikidwa ndi Mulungu.+ Sankhani manda abwino koposa pa manda amene tili nawo kuti muikemo malemuwo.+ Palibe aliyense wa ife amene angakanize manda ake kuti muikemo malemuwo.”+
7 Pamenepo Abulahamu anaimirira n’kugwada pansi pamaso pa eni dzikowo,+ ana a Heti.+
8 Iye analankhula nawo kuti: “Ngati mukuvomera kuti ndiike m’manda malemu mkazi wanga, ndimvereni ndipo mundipemphere kwa Efuroni mwana wa Zohari.+
9 Mundipemphere kuti andigulitse phanga lake la Makipela+ limene lili m’malire a malo ake. Andigulitse pa mtengo wake wonse inu mukuona, kuti ndiikemo malemu mkazi wanga.”+
10 Pa nthawiyi n’kuti Efuroni atakhala pansi pakati pa ana a Heti. Choncho Efuroni Mhiti+ anayankha Abulahamu, ana a Hetiwo akumva limodzi ndi onse amene analowa pachipata cha mzinda wake.+ Iye anati:
11 “Ayi mbuyanga! Ndimvereni. Malowo, pamodzi ndi phanga limene lili pamalopo, ndikupatsani pamaso pa anthu a mtundu wangawa.+ Kaikeni malemuwo.”
12 Pamenepo Abulahamu anagwada pamaso pa eni dzikowo.
13 Kenako iye analankhula kwa Efuroni pamaso pa eni dzikowo kuti: “Ndimvere chonde. Ine ndigulabe malowo. Landira silivayu+ kuti ndikaike mkazi wanga kumeneko.”
14 Ndiyeno Efuroni anayankha Abulahamu kuti:
15 “Ndimvereni mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi siliva wolemera masekeli* 400. Koma zimenezo sindiyo nkhani yaikulu pakati pa ine ndi inu. Kaikeni malemuwo.”+
16 Chotero Abulahamu anamveradi Efuroni, n’kumuyezera siliva wokwanira mtengo umene Efuroniyo ananena pamaso pa ana a Heti. Anamuyezera siliva wolemera masekeli 400, malinga ndi muyezo wovomerezeka ndi amalonda pa nthawiyo.+
17 Chotero malo a Efuroni amene anali ku Makipela moyang’anizana ndi Mamure, ndiponso phanga limene linali mmenemo, komanso mitengo yonse imene inali mkati mwa malire onse a malowo,+ anatsimikizirika+
18 pamaso pa ana a Heti ndi onse amene analowa pachipata cha mzinda, kuti Abulahamu ndiye wagula malowo ndipo ndi ake.+
19 Zitatero, Abulahamu anaika Sara mkazi wake m’manda kuphanga la Makipela, moyang’anizana ndi Mamure, kapena kuti Heburoni, m’dziko la Kanani.+
20 Chotero ana a Heti anagulitsa kwa Abulahamu malowo ndi phanga limene linali pamenepo, ndipo mkazi wake anamuika m’manda kumeneko.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ndiike malemu anga kuti ndisawaonenso.”
^ “Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndi wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.