Genesis 36:1-43

36  Mbiri ya Esau, kapena kuti Edomu,+ ili motere:  Esau anatenga akazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+ Anatenga Ada,+ mwana wamkazi wa Eloni, Mhiti.+ Anatenganso Oholibama,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Ana, komanso anali mdzukulu wa Zibeoni, Mhivi.  Anatenganso Basemati,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Isimaeli, komanso anali mlongo wake wa Nebayoti.+  Ada anaberekera Esau mwana dzina lake Elifazi, ndipo Basemati anam’berekera Reueli.  Ana amene Oholibama anaberekera Esau ndiwo Yeusi, Yalamu ndi Kora.+ Amenewa anali ana a Esau amene anabereka m’dziko la Kanani.  Pambuyo pake, Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ena onse a m’nyumba yake, ziweto zake zonse ndi chuma chake+ chonse chimene anachipeza m’dziko la Kanani, n’kupita kudziko lina kutali ndi Yakobo m’bale wake.+  Iye anachoka chifukwa chuma chawo chinali chitawachulukira kwambiri, moti sakanathanso kukhala limodzi. Dziko lachilendo limene anali kukhalalo linali litawachepera chifukwa cha kuchuluka kwa ziweto zawo.+  Chotero Esau anakakhazikika kudera lamapiri ku Seiri.+ Esau analinso kutchedwa Edomu.+  Tsopano nayi mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu, amene anali kukhala kudera lamapiri la Seiri.+ 10  Mayina a ana a Esau ndi awa: Elifazi, mwana wamwamuna wobadwa kwa Ada mkazi wake wa Esau, komanso Reueli, mwana wamwamuna wobadwa kwa Basemati mkazi wake wa Esau.+ 11  Ana a Elifazi anali Temani,+ Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.+ 12  Elifazi mwana wa Esau anali ndi mdzakazi dzina lake Timina.+ Patapita nthawi, mdzakaziyu anaberekera Elifazi mwana wamwamuna dzina lake Amaleki.+ Amenewa ndiwo anali ana a Ada mkazi wa Esau. 13  Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Shama ndi Miza.+ Amenewa ndiwo anali ana a Basemati+ mkazi wa Esau. 14  Oholibama, mkazi wake wa Esau, anaberekera Esau ana aamuna awa: Yeusi, Yalamu ndi Kora.+ Oholibamayu anali mwana wa Ana, komanso mdzukulu wa Zibeoni. 15  Nawa mafumu+ a mafuko a ana a Esau: Ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau, anali: Mfumu Temani,+ mfumu Omari, mfumu Zefo, mfumu Kenazi, 16  mfumu Kora, mfumu Gatamu ndi mfumu Amaleki. Amenewa ndiwo anali mafumu a kubanja la Elifazi+ m’dziko la Edomu. Iwowa anali ana obadwa kwa Ada. 17  Nawa ana a Reueli, mwana wamwamuna wa Esau: Mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Shama ndi mfumu Miza. Amenewa ndiwo anali mafumu a kubanja la Reueli m’dziko la Edomu.+ Iwowa anali ana obadwa kwa Basemati mkazi wa Esau. 18  Potsiriza, nawa ana a Oholibama mkazi wa Esau: Mfumu Yeusi, mfumu Yalamu ndi mfumu Kora. Amenewa ndiwo anali mafumu a kubanja la Oholibama mkazi wa Esau, mwana wa Ana. 19  Amenewa ndiwo anali ana a Esau kapena kuti Edomu,+ ndi mafumu awo. 20  Nawa ana a Seiri Mhori, eni dzikolo:+ Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,+ 21  Disoni, Ezeri ndi Disani.+ Amenewa anali ana a Seiri, mafumu a fuko la Ahori, m’dziko la Edomu. 22  Ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu, ndipo Lotani anali ndi mlongo wake dzina lake Timina.+ 23  Ana a Sobala anali Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. 24  Ana a Zibeoni anali Aya ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi otentha m’chipululu, pamene anali kudyetsa abulu a Zibeoni bambo ake.+ 25  Ana anabereka Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana. 26  Ana a Disoni anali Hemadani, Esibani, Itirani ndi Kerana.+ 27  Ana a Ezeri anali Bilihani, Zavani ndi Ekani. 28  Ana a Disani anali Uzi ndi Arani.+ 29  Nawa mafumu a fuko la Ahori: Mfumu Lotani, mfumu Sobala, mfumu Zibeoni, mfumu Ana, 30  mfumu Disoni, mfumu Ezeri ndi mfumu Disani.+ Amenewa ndiwo anali mafumu a fuko la Ahori monga mwa ufumu wawo m’dziko la Seiri. 31  Nawa tsopano mafumu aakulu amene analamulira dziko la Edomu,+ ana a Isiraeli asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse:+ 32  Bela mwana wa Beori analamulira Edomu,+ ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 33  Bela atamwalira, Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozira,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 34  Yobabi atamwalira, Husamu wa kudziko la Atemani,+ anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 35  Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi amene anagonjetsa Amidiyani+ m’dziko la Mowabu,+ anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti.+ 36  Hadadi atamwalira, Samila wa ku Masereka anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 37  Samila atamwalira, Shauli wa ku Rehoboti mzinda wa m’mphepete mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 38  Shauli atamwalira, Baala-hanani mwana wa Akibori, anayamba kulamulira m’malo mwake.+ 39  Baala-hanani mwana wa Akibori atamwalira, Hadari anayamba kulamulira m’malo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Pau. Mkazi wake dzina lake anali Mehetabele, mwana wa Matiredi. Matiredi anali mwana wamkazi wa Mezahabu.+ 40  Mayina a mafumu a Esau monga mwa mabanja awo, mwa madera awo, ndi monga mwa mayina awo, ndi awa: Mfumu Timina, mfumu Aliva, mfumu Yeteti,+ 41  mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni,+ 42  mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibezari,+ 43  mfumu Magidieli ndi mfumu Iramu. Amenewa ndiwo anali mafumu a Edomu+ monga mwa madera awo m’dziko lawo.+ Iyi ndiyo mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.