Genesis 43:1-34
43 Tsopano njala ija inakula kwambiri m’dzikomo.+
2 Tirigu amene anachokera naye ku Iguputo uja atatha,+ bambo awo anawauza kuti: “Pitaninso mukatigulireko chakudya pang’ono.”+
3 Koma Yuda anauza bambo ake kuti:+ “Munthu ujatu anatichenjeza mwamphamvu kuti, ‘Musadzayese n’komwe kuonekeranso pamaso panga mukadzalephera kubwera naye m’bale wanuyo.’+
4 Ngati mutilola kutenga m’bale wathuyu,+ ndife okonzeka kutsikira ku Iguputo kuti tikagule chakudya.
5 Koma ngati simutilola kupita naye, sititsikirako, chifukwa munthu uja ananenetsa kuti, ‘Musadzayese n’komwe kuonekeranso pamaso panga mukadzalephera kubwera naye m’bale wanuyo.’”+
6 Pamenepo Isiraeliyo anadandaula+ kuti: “N’chifukwa chiyani munandipweteka chotero, pomuuza munthuyo kuti muli ndi m’bale wanu wina?”
7 Koma iwo anayankha kuti: “Munthuyo anachita kufunsa za ife ndi banja lathu kuti, ‘Kodi bambo anu akali ndi moyo?+ Kodi muli ndi m’bale wanu wina?’ Ndipo ife tinayankha mogwirizana ndi zimene anafunsa.+ Nanga tikanadziwa bwanji zoti anena kuti, ‘Mukam’bweretse kuno m’bale wanuyo’?”+
8 Potsirizira pake, Yuda anauza Isiraeli bambo ake kuti: “M’perekeni kwa ine mnyamatayu+ kuti tinyamuke tizipita. Tipite kuti tikhalebe ndi moyo tisafe,+ inuyo ndi ife, limodzi ndi ana athu aang’onowa.+
9 Ineyo ndikhala chikole cha moyo wa mnyamatayu.+ Chilangocho chikabwere pa ine.+ Ndikadzalephera kubwera naye ndi kum’pereka kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu moyo wanga wonse.
10 Ndipotu tikanapanda kuzengereza, bwenzi pano titapita n’kubwerako maulendo awiri.”+
11 Ndiyeno bambo awo Isiraeli anawauza kuti: “Chabwino, ngati ndi choncho,+ chitani izi: Tengani zinthu zamtengo wapatali za dziko lino m’matumba anu, mukam’patse munthuyo monga mphatso.+ Tengani mafuta a basamu+ pang’ono, uchi+ pang’ono, mafuta onunkhira a labidanamu, khungwa la utomoni wonunkhira,+ mtedza wa pisitasho, ndi zipatso za amondi.+
12 Mutengenso ndalama kuwirikiza kawiri zoyamba zija. Komanso mutenge ndalama anakubwezerani zija, zimene munazipeza pamwamba pa matumba anu, mukazibweze.+ Mwina anangosokoneza.+
13 Mukatero, mutenge m’bale wanuyu mubwerere kwa munthuyo.
14 Mulungu Wamphamvuyonse apangitse munthuyo kukuchitirani chifundo,+ kuti akamasule m’bale wanu uja, ndipo mukabwere naye limodzi ndi Benjamini. Koma ngati ndingatayikidwe ana anga, chabwino, zikhale choncho!”+
15 Ndiyeno amunawo anatenga mphatso zija, ndalama zowirikiza kawiri zija, ndiponso Benjamini, n’kunyamuka kupita ku Iguputo. Kumeneko anakaonekera pamaso pa Yosefe.+
16 Yosefe atangoona Benjamini ali ndi amunawo, anauza mwamuna woyang’anira nyumba yake kuti: “Atengere kunyumba anthuwa. Uphe nyama ndi kukonza chakudya,+ chifukwa anthuwa adya ndi ine masana ano.”
17 Nthawi yomweyo mwamuna uja anachita zimene Yosefe ananena.+ Anatengera anthu aja kunyumba kwa Yosefe.
18 Koma amunawo anachita mantha poona kuti awatengera kunyumba kwa Yosefe.+ Ndipo iwo anati: “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zimene tinabwerera nazo m’matumba athu pa ulendo woyamba uja. Ndithu amenewa akufuna atiukire, kuti atigwire tikhale akapolo, ndiponso kuti atilande abulu athu!”+
19 Pamenepo iwo anapita kwa munthu woyang’anira nyumba ya Yosefe uja, n’kulankhula naye pakhomo lolowera kunyumbako,
20 kuti: “Pepani mbuyathu! Ifetu tinabwera kuno kudzagula chakudya ulendo woyamba.+
21 Pobwerera, zinachitika n’zakuti, titafika pamalo ogona+ n’kumasula matumba athu, tinangoona kuti ndalama za aliyense zili pakamwa pa thumba lake, zonse malinga ndi kulemera kwake. Choncho tabwera nazo kuti tizibweze tokha.+
22 Tabweranso ndi ndalama zina zogulira chakudya. Koma ndithu sitikudziwa kuti ndani anatibwezera ndalama zathu poziika m’matumba athu.”+
23 Pamenepo mwamunayo anati: “Musachite mantha,+ simunalakwe kanthu. Mulungu wanu, Mulungu wa bambo anu ndiye anakupatsani chumacho m’matumba mwanu.+ Ndalama zanu zinafikira kwa ine.” Atatero mwamunayo anamasula Simiyoni n’kumubweretsa kwa iwo.+
24 Tsopano munthuyo analowetsa amunawo m’nyumba ya Yosefe. Anawapatsa madzi kuti asambe mapazi awo,+ n’kuwapatsanso chakudya choti adyetse abulu awo.+
25 Amunawo anakonzeratu mphatso+ zimene anabwera nazo zija kuti apatse Yosefe masanawo, popeza anali atamva kuti adyera nawo limodzi chakudya kumeneko.+
26 Ndiyeno Yosefe atafika n’kulowa m’nyumbamo, iwo anapereka mphatsozo kwa iye. Anamugwadira n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+
27 Kenako Yosefe anawafunsa ngati ali bwino.+ Anawafunsanso kuti: “Kodi bambo anu okalamba amene munkanena aja ali bwino? Kodi adakali ndi moyo?”+
28 Iwo anayankha kuti: “Kapolo wanu bambo athu ali bwino. Adakali ndi moyo.” Atatero anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+
29 Yosefe atakweza maso ake n’kuona mng’ono wake Benjamini, m’bale wake wa mimba imodzi,+ anati: “Kodi uyu ndiye mng’ono wanu amene munali kunena uja?”+ Ananenanso kuti: “Mulungu akukomere mtima+ mwana wanga.”
30 Tsopano Yosefe anachokapo mofulumira chifukwa anagwidwa chifundo mumtima poona m’bale wakeyo.+ Anafunafuna malo oti akalirire, ndipo analowa m’chipinda chamkati n’kukagwetsa misozi.+
31 Kenako, anasamba kumaso, n’kutuluka panja. Anadzilimbitsa+ n’kunena kuti: “Ikani chakudya.”+
32 Iwo anaikira Yosefe chakudya payekha. Abale akewo anawaikiranso paokha. Nawonso Aiguputo amene ankadya m’nyumba mwake anawaikira paokha. Aiguputo sankadya limodzi ndi Aheberi, chifukwa chinali chinthu chonyansa kwa iwo.+
33 Abale akewo anakhala pansi pamaso pake, kuyambira woyamba kubadwa malinga ndi ukulu wake,+ mpaka wamng’ono malinga ndi msinkhu wake. Iwo anali kuyang’anana modabwa.
34 Yosefe ankatapa chakudya patebulo pake n’kumapatsa operekera chakudya kuti aziwonjezera pachakudya cha abale akewo. Koma chakudya chowonjezera pa Benjamini anali kuchiwirikiza kasanu kuposa cha enawo.+ Choncho iwo anapitiriza kudya ndi kumwa naye limodzi pamadyererowo mosangalala.+