Genesis 44:1-34

44  Kenako Yosefe analamula woyang’anira nyumba yake+ uja kuti: “Udzaze chakudya m’matumba a anthuwa mpaka mlingo woti akhoza kunyamula. Aliyense umubwezere ndalama zake poziika pamwamba pa thumba lake.+  Koma uike kapu yanga yasiliva ija pamwamba pa thumba la wamng’onoyo limodzi ndi ndalama zake zogulira tirigu.” Choncho woyang’anira nyumba yakeyo anachita monga mmene Yosefe ananenera.+  M’mawa kutacha, abale ake a Yosefe aja analoledwa kupita+ pamodzi ndi abulu awo.  Iwo anatuluka mumzindawo koma asanapite patali, Yosefe anauza woyang’anira nyumba yake kuti: “Nyamuka, athamangire anthu aja. Ukawapeza uwafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwabwezera zoipa pa zabwino?+  N’chifukwa chiyani mwaba kapu yomwera mbuye wanga, imenenso amaombezera pofuna kudziwa zinthu?+ Mwachita chinthu choipa kwambiri.’”  Munthu uja atawapeza, anawafunsa zimenezo.  Koma iwo anamuyankha kuti: “N’chifukwa chiyani mukulankhula choncho mbuyathu? N’zosatheka kuti akapolo anufe tichite chinthu chotero.  Pajatu ndalama zimene tinazipeza pamwamba pa matumba athu kudziko la Kanani tinazibweza kwa inu.+ Ndiye zingatheke bwanji kuti tibe siliva ndi golide m’nyumba ya mbuye wanu?+  Amene apezeke ndi kapuyo mwa akapolo anufe aphedwe, ndipo enafe tikhale akapolo anu mbuyathu.”+ 10  Ndiyeno iye anati: “Chabwino, zichitike mmene mwaneneramo.+ Amene ati apezeke nacho akhala kapolo wanga,+ koma enanu mukhala opanda mlandu.” 11  Pamenepo, aliyense anatsitsa pansi thumba lake mwamsanga n’kulimasula. 12  Munthu uja anayamba kufufuza mosamala m’matumba awo, kuyambira la wamkulu kumalizira ndi la wamng’ono. Potsirizira pake, kapuyo inapezeka m’thumba la Benjamini.+ 13  Zitatero, iwo anang’amba zovala zawo.+ Kenako aliyense anakwezanso thumba lake pabulu wake n’kubwerera kumzinda kuja. 14  Atafika, Yuda+ ndi abale ake analowa m’nyumba ya Yosefe. Anamupeza akanali m’nyumbamo, ndipo anagwada n’kumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 15  Tsopano Yosefe anati: “Ndiye chiyani mwachitachi? Kodi inu simukudziwa kuti munthu ngati ine ndimatha kudziwa zinthu poombeza maula?”+ 16  Ndiyeno Yuda anadandaula kuti: “Kodi tinganene chiyani kwa inu mbuyathu? Tilankhule kuti chiyani? Titani kuti muone kuti sitinalakwe?+ Pamenepa Mulungu woona ndiye wapeza cholakwa mwa ife akapolo anu.+ Basi, titengeni ndife akapolo anu mbuyathu,+ ifeyo limodzi ndi amene mwam’peza ndi kapuyo.” 17  Koma Yosefe anati: “Sindingachite zimenezo!+ Amene wapezeka ndi kapu yangayo ndiye akhale kapolo wanga.+ Enanu mupite kwa bambo anu mwamtendere.”+ 18  Tsopano Yuda anayandikira kwa Yosefe n’kunena kuti: “Chonde mbuyanga, ndapota nanu. Lolani kuti kapolo wanune ndinene mawu amodzi okha.+ Chonde musandipsere mtima,+ pakuti inu muli ngati Farao+ yemwe. 19  Pajatu inu mbuyanga munatifunsa ife akapolo anu kuti: ‘Kodi muli ndi bambo kapena m’bale wanu wina?’ 20  Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, amene ndiye wamng’ono pa ife tonse.+ M’bale wake wa mimba imodzi anamwalira, moti anatsala yekha,+ ndipo bambo amam’konda kwambiri.’ 21  Titatero, inu munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Mukabwere naye kuno kuti ndidzamuone.’+ 22  Koma ife tinakuuzani inu mbuyanga kuti, ‘Mwanayo sangachoke kwa bambo. Atati achoke, ndithu bambo adzafa.’+ 23  Ndiyeno munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Musadzayese n’komwe kuonekeranso pamaso panga mukadzalephera kubwera naye m’bale wanuyo.’+ 24  “Ife tinapita kwa kapolo wanu, bambo athu, ndipo tinakawauza zimene munanena mbuyanga. 25  Patapita nthawi bambo athu anatiuza kuti, ‘Mubwerere, mukatigulire chakudya pang’ono.’+ 26  Koma ife tinati, ‘Sitingathe kutsikira kumeneko. Ngati tikhala naye limodzi mng’ono wathuyu tipitako, chifukwa sitingathe kukaonekeranso pamaso pa munthuyo tikapanda kupita naye.’+ 27  Ndiyeno kapolo wanu bambo athuwo anatiuza kuti, ‘Inuyo mukudziwa bwino ndithu kuti mkazi wanga anandiberekera ana awiri okha.+ 28  Koma mmodzi wa awiriwo anandisiya, ndipo ndinafuula kuti: “Kalanga ine! Ndithu wakhadzulidwa mwana wanga!”+ Mpaka lero sindinamuonenso. 29  Ndiye ngati uyunso mungapite naye, iye n’kukakumana ndi tsoka n’kufa, ndithu mudzatsitsira ku Manda+ imvi zangazi ndi chisoni.’ 30  “Choncho, ndikakangofika kwa kapolo wanu bambo anga, ndilibe mwanayu, amene bambo amam’konda kwambiri ngati mmene amakondera moyo wawo,+ 31  akakangoona kuti mwanayu palibe, basi akafa. Ndithu, akapolo anufe tidzakhala titatsitsira ku Manda imvi za kapolo wanu bambo athu ndi chisoni. 32  Ine kapolo wanu ndinadzipereka kukhala chikole+ cha moyo wa mwanayu pamene ali kutali ndi bambo ake. Ndinalonjeza kuti, ‘Ndikadzalephera kubwera naye kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu bambo anga moyo wanga wonse.’+ 33  Ndiye chonde mbuyanga, tengani ineyo ndikhale kapolo wanu m’malo mwa mwanayu, kuti iye apite ndi abale akewa.+ 34  Ndingathe bwanji kupita kwa bambo anga ndilibe mwanayu? Ayi, sindikufuna kukaona bambo anga akuzunzika ndi chisoni.”+

Mawu a M'munsi