Genesis 47:1-31

47  Yosefe anafikadi kwa Farao n’kumuuza kuti:+ “Bambo anga ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi nkhosa zawo, ng’ombe zawo ndi zonse zimene ali nazo, ndipo afikira ku Goseni.”+  Pa abale ake onsewo, Yosefe anatengapo asanu kuti akawasonyeze kwa Farao.+  Ndiyeno Farao anafunsa abale ake a Yosefe aja kuti: “Kodi mumagwira ntchito yanji?”+ Iwo anayankha Farao kuti: “Akapolo anufe timaweta nkhosa+ monga ankachitira makolo athu.”+  Kenako anauza Farao kuti: “Tabwera kuno kudzakhala monga alendo,+ chifukwa akapolo anufe tilibe chakudya chopatsa ziwetozi,+ popeza njala yafika poipa kwambiri ku Kanani.+ Ndiye chonde, tiloleni ife akapolo anu tikhale ku Goseni.”+  Pamenepo Farao anauza Yosefe kuti: “Bambo ako ndi abale akowa abwera kuno kwa iwe.  Dziko la Iguputo lili m’manja mwako,+ chotero uwapatse malo abwino koposa.+ Auze akhale ku Goseni,+ ndipo ngati ukudziwapo amuna olimbikira ntchito pakati pawo,+ uwaike kukhala akapitawo oyang’anira ng’ombe zanga.”+  Kenako Yosefe anabweretsa bambo ake Yakobo n’kuwasonyeza kwa Farao. Ndipo Yakobo anadalitsa Farao.+  Ndiyeno Farao anafunsa Yakobo kuti: “Kodi muli ndi zaka zingati?”  Yakobo anayankha Farao kuti: “Zaka za moyo wanga monga mlendo m’malo osiyanasiyana zikukwana 130.+ Zaka zimenezi zakhala zowerengeka ndi zosautsa,+ ndipo sizinafike pa zaka za moyo wa makolo anga monga alendo m’malo osiyanasiyana.”+ 10  Atatero, Yakobo anadalitsa Farao n’kuchoka pamaso pake.+ 11  Chotero Yosefe anakhazika bambo ake ndi abale akewo ku Iguputo. Anawapatsa malo abwino koposa a dzikolo ku Ramese,+ monga mmene Farao analamulira. 12  Kumeneko, Yosefe anali kugawira chakudya bambo ake, abale ake ndi banja lonse la bambo ake,+ malinga ndi kuchuluka kwa ana.+ 13  Njala itafika poipa kwambiri,+ chakudya chinatheratu m’dziko lonselo. Anthu onse a ku Iguputo ndi a ku Kanani anali ofooka chifukwa cha njalayo.+ 14  Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene zinali m’dziko la Iguputo ndi la Kanani, zomwe anthu anali kugulira chakudya.+ Iye anali kutenga ndalamazo kuzipititsa kunyumba kwa Farao. 15  Potsirizira pake, ndalama zonse za m’dziko la Iguputo ndi dziko la Kanani zinatha. Pamenepo anthu onse a ku Iguputo anayamba kufika kwa Yosefe n’kunena kuti: “Tipatseni chakudya!+ Kodi tikufereni mukuona chifukwa choti ndalama zatithera?”+ 16  Ndiye Yosefe anati: “Ngati ndalama zakutherani, bweretsani ziweto zanu tidzasinthane ndi chakudya.” 17  Pamenepo anthuwo anayamba kubweretsa ziweto zawo kwa Yosefe. Yosefeyo anali kuwapatsa chakudya mosinthana ndi mahatchi* awo, nkhosa, ng’ombe ndi abulu.+ M’chaka chonsecho, Yosefe anali kuwagawira chakudya mosinthana ndi ziweto zawo. 18  Kenako, chakacho chinafika kumapeto, ndipo anthu anayamba kufika kwa iye chaka chotsatira. Iwo ankanena kuti: “Sitikubisirani mbuyathu, ndalama zathu ndi ziweto zonse zathera kwa inu.+ Zimene tangotsala nazo ndi matupi athuwa ndi nthaka yathuyi basi.+ 19  Tiferenji ife inu mukuona,+ ndipo minda yathu ikhalirenji yogonera? Mutigule limodzi ndi minda yathu potipatsa chakudya+ kuti tikhale akapolo a Farao. Mutipatse tirigu kuti tikhale ndi moyo tisafe, kutinso minda yathu isagonere.”+ 20  Choncho, Yosefe anagulira Farao nthaka yonse ya Aiguputo,+ chifukwa Mwiguputo aliyense anagulitsa munda wake. Anatero chifukwa njala inali itawapanikiza koopsa, moti nthaka yonse inakhala ya Farao. 21  Yosefe anasamutsira anthuwo m’mizinda, kuchokera kumalire a dziko la Iguputo mpaka kumalire ena.+ 22  Nthaka ya ansembe+ yokha ndi imene sanaigule, chifukwa chakudya chimene ansembe anali kudya chinali kuchokera kwa Farao.+ N’chifukwa chake ansembewo sanagulitse nthaka yawo.+ 23  Tsopano Yosefe anauza anthuwo kuti: “Onani, ndakugulani inu lero limodzi ndi nthaka yanu, kugulira Farao. Nayi mbewu, mubzale m’minda yanu.+ 24  Pa nthawi yokolola,+ muzipereka kwa Farao gawo limodzi mwa magawo asanu a zokololazo.+ Magawo anayi otsalawo muzigwiritsa ntchito monga mbewu yobzala m’minda yanu, chakudya chanu ndi cha a m’nyumba zanu, komanso cha ana anu.”+ 25  Iwo anayankha kuti: “Mwapulumutsa miyoyo yathu.+ Mwatikomera mtima mbuyathu, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.”+ 26  Chotero Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero lakuti, Farao azilandira gawo limodzi mwa magawo asanu a zokolola za minda yonse ya mu Iguputo. Koma ansembe, monga gulu lapadera, minda yawo sinakhale ya Farao.+ 27  Aisiraeliwo anakhazikika m’dziko la Iguputo, m’chigawo cha Goseni.+ Kumeneko anaberekana n’kuchulukana kwambiri.+ 28  Ndipo Yakobo anakhalabe ndi moyo m’dziko la Iguputo kwa zaka 17. Choncho masiku onse a moyo wa Yakobo anakwana zaka 147.+ 29  Tsopano nthawi inayandikira yakuti Isiraeli amwalire.+ Ndiye anaitana mwana wake Yosefe n’kumuuza kuti: “Ngati ungandikomere mtima, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga.+ Ulumbire kuti udzandisonyeza kukoma mtima kosatha ndipo udzakhala wokhulupirika kwa ine.+ Chonde, usadzandiike m’manda ku Iguputo kuno.+ 30  Ndikufuna ndikagone limodzi ndi makolo anga.+ Choncho udzandinyamule ku Iguputo kuno, ukandiike m’manda a makolo anga.”+ Yosefe anayankha kuti: “Ndidzachitadi monga mwa mawu anu.” 31  Ndiyeno Yakobo anati: “Lumbira kwa ine.” Yosefe analumbira kwa iye.+ Pamenepo Isiraeli anawerama n’kutsamira kumutu kwa bedi lake.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”