Genesis 34:1-31
34 Dina, mwana wamkazi amene Leya+ anaberekera Yakobo, ankakonda kukacheza+ ndi ana aakazi a m’dzikolo.+
2 Kenako Sekemu anaona mtsikanayu. Sekemuyu anali mwana wamwamuna wa Hamori, Mhivi,+ mmodzi wa atsogoleri a m’dzikolo. Atamuona, anamutenga n’kumugwiririra.+
3 Atatero, nthawi zonse mtima wake unali kulakalaka Dina mwana wa Yakobo, ndipo anamukonda kwambiri m’tsikanayu, moti ankalankhula naye momunyengerera.
4 Potsirizira pake, Sekemu anauza bambo ake Hamori+ kuti: “Munditengere mtsikana ameneyu kuti akhale mkazi wanga.”+
5 Tsopano Yakobo anamva zakuti Sekemu wagwiririra mwana wake Dina. Pa nthawiyo n’kuti ana ake aamuna ali kubusa ndi ziweto zake.+ Choncho, Yakobo sananene kanthu kudikira kuti ana akewo abwere.+
6 Pambuyo pake, Hamori bambo ake a Sekemu, anapita kwa Yakobo kukakambirana naye.+
7 Koma ana a Yakobo anabwerako kubusa kuja atangomva za nkhaniyi. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa,+ pakuti Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chonyazitsa kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika m’pang’ono pomwe.+
8 Ndiyeno Hamori anawauza kuti: “Mwana wanga Sekemu wakonda mtsikana wanuyu ndi mtima wonse.+ Chonde, m’patseni kuti akhale mkazi wake.+
9 Tiyeni tichite mgwirizano wakuti tizikwatirana.+ Muzitipatsa ana anu aakazi, inunso muzitenga ana athu aakazi.+
10 Mukhale nafe kwathu kuno, dziko lino likhalanso lanu. Mukhazikike, ndipo muzichita malonda mwaufulu.”+
11 Pamenepo Sekemu anauza bambo ake a Dina ndi alongo ake kuti: “Ndikomereni mtima, ndikupatsani zonse zimene munganene.
12 Kwezani kwambiri ndalama za ukwati ndi mphatso zoti ndipereke,+ ndipo ndine wokonzeka kupereka zilizonse zimene munganene, malinga mundipatse mtsikanayu kuti akhale mkazi wanga.”
13 Koma ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi bambo ake Hamori mowapita pansi. Anatero chifukwa Sekemu anali atagwiririra Dina mlongo wawo.+
14 Kuwayankha kwake anati: “Sitingachite zimenezo. Sitingapereke mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa.+ Zimenezo n’zonyazitsa kwa ife.
15 Tikulolani pokhapokha mwamuna aliyense pakati panu atadulidwa, kuti mukhale ofanana ndi ife.+
16 Mukatero, ndithu tidzakupatsani ana athu aakazi ndipo ifenso tidzatenga ana anu aakazi. Tidzakhaladi ndi inu, ndipo tidzakhala anthu amodzi.+
17 Koma ngati simutsatira zimene tanena zakuti mudulidwe, mwana wathu wamkaziyo tikamutenga n’kubwera naye.”
18 Mawu awowa anakondweretsa Hamori ndi mwana wake Sekemu.+
19 Chotero mnyamatayu sanachedwe kuchita zimene anauzidwazo+ chifukwa anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. Sekemuyo anali wolemekezeka kwambiri+ m’nyumba yonse ya bambo ake.+
20 Choncho Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita kuchipata cha mzinda wawo, n’kuyamba kulankhula kwa anthu a mumzindawo+ kuti:
21 “Anthu awa n’ngofuna mtendere ndi ife.+ Ndiye aloleni akhale m’dzikoli ndi kuchitamo malonda, popeza dzikoli n’lalikulu moti atha kukhalamo.+ Tikhoza kukwatira ana awo aakazi, ndiponso tikhoza kuwapatsa ana athu aakazi.+
22 Koma pakufunika chinthu chimodzi kuti anthuwa alole kukhala nafe limodzi n’kukhala anthu amodzi ndi ife. Akuti adzatero pokhapokha mwamuna aliyense pakati pathu atadulidwa+ ngati mmene iwonso alili.
23 Tikatero, katundu wawo, chuma chawo ndi ziweto zawo zonse sizidzakhala zathu kodi?+ Tiyeni tilolere zimene akufunazo kuti azikhala nafe.”+
24 Chotero anthu onse otuluka pachipata cha mzindawo anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo amuna onse a mumzinda wakewo anadulidwa.
25 Koma pa tsiku lachitatu, pamene anthuwo anali pa ululu,+ ana awiri a Yakobo, Simiyoni ndi Levi,+ alongo ake a Dina,+ aliyense anatenga lupanga lake n’kukalowa mumzindawo mosaonetsera cholinga chawo. Kenako anayamba kupha mwamuna aliyense.+
26 Anaphanso Hamori ndi mwana wake Sekemu ndi lupanga.+ Kenako anatenga Dina m’nyumba ya Sekemu, n’kupita naye.+
27 Ana ena a Yakobo anamalizitsa amuna omwe anali atapwetekedwa koopsa, n’kutenga katundu yense wa mumzindamo. Anatero chifukwa anthuwo anagwiririra mlongo wawo.+
28 Anatenga nkhosa zawo, abulu awo ndi ziweto zina, ndi zonse zimene zinali mumzindawo, ndiponso zimene zinali kunja kwa mzindawo.+
29 Anatenga chuma chawo chonse, ndipo ana awo onse ang’onoang’ono ndi akazi awo anawagwira ndi kupita nawo. Anatenga zonse zimene zinali m’nyumba zawo.+
30 Yakobo ataona zimenezi anauza Simiyoni ndi Levi+ kuti: “Mwandiputira chidani, ndipo mwandinunkhitsa kwa anthu a m’dziko lino,+ Akanani ndi Aperezi. Ine ndili ndi anthu ochepa,+ ndipo iwowa ndithu asonkhana pamodzi n’kutiukira. Atithira nkhondo n’kutitha tonse, ine ndi banja langa.”
31 Koma anawo anayankha kuti: “Kodi ndi bwino kuti munthu azitenga mlongo wathu ngati hule?”+