Genesis 13:1-18

13  Chotero Abulamu anachoka ku Iguputo, iye ndi mkazi wake ndi zonse zimene anali nazo, limodzinso ndi Loti, n’kulowera ku Negebu.+  Abulamu anali ndi chuma chambiri. Anali ndi ziweto, siliva ndi golide.+  Kenako Abulamu anachoka ku Negebu. Anali kumanga misasa ndi kusamuka mpaka kukafika ku Beteli, kumene kunali hema wake poyamba, pakati pa Beteli ndi Ai.+  Kumeneko n’kumene anamangako guwa lansembe poyamba paja.+ Abulamu atafika kumeneko, anayamba kuitana pa dzina la Yehova.+  Loti, yemwe anali limodzi ndi Abulamu, nayenso anali ndi nkhosa, ng’ombe ndi mahema.  Choncho, chifukwa chokhala ndi katundu wambiri, malo anawachepera moti sakanatha kukhala limodzi.+  Kenako panabuka mkangano pakati pa abusa a Abulamu ndi abusa a Loti. Pa nthawiyo, n’kuti Akanani ndi Aperizi akukhala m’dzikomo.+  Chotero Abulamu anauza Loti+ kuti: “Chonde, pasakhale mkangano uliwonse pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa abusa anga ndi abusa ako, pajatu ndife pachibale.+  Tiye tipatukane. Ukhoza kutenga mbali iliyonse ya dzikoli. Iwe ukapita kumanzere, ine ndipita kumanja, koma iwe ukapita kumanja, ine ndipita kumanzere.”+ 10  Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora. 11  Pamenepo, Loti anasankha Chigawo chonse cha Yorodano, ndipo anasamutsira msasa wake kum’mawa. Motero iwo anapatukana. 12  Abulamu anakakhala kudziko la Kanani, koma Loti anakakhala pakati pa mizinda ya m’Chigawocho.+ Potsirizira pake, anakamanga hema wake pafupi ndi Sodomu. 13  Koma anthu a ku Sodomu anali oipa, ndipo anali ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.+ 14  Abulamu atapatukana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyang’ane kumpoto ndi kum’mwera, komanso kum’mawa ndi kumadzulo.+ 15  Dziko lonse limene ukulionali, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako, kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 16  Ndidzachulukitsa mbewu yako ngati mchenga wa padziko lapansi, kotero kuti ngati munthu angathe kuwerenga mchengawo, ndiye kuti mbewu yako idzatha kuwerengedwa.+ 17  Nyamuka, uyendere dziko lonselo, m’litali mwake ndi m’lifupi mwake, chifukwa ndidzalipereka kwa iwe.”+ 18  Choncho Abulamu anapitiriza kukhala m’mahema. M’kupita kwa nthawi, anakakhala pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure,+ ku Heburoni.+ Kumeneko, anamangira Yehova guwa lansembe.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “kumunsi kwa chigwa cha Yorodano.”