Genesis 25:1-34

25  Tsopano Abulahamu anatenganso mkazi wina, dzina lake Ketura.+  M’kupita kwa nthawi, mkaziyo anamuberekera Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+  Yokesani anabereka Sheba+ ndi Dedani.+ Ana a Dedani anali Asurimu, Letusimu ndi Leumimu.  Ana a Midiyani anali Efa,+ Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.+ Onsewa anali ana aamuna a Ketura.  Pambuyo pake, Abulahamu anapatsa Isaki zonse zimene anali nazo.+  Koma ana a adzakazi amene Abulahamu anali nawo, anawapatsa mphatso.+ Kenako, iye adakali ndi moyo, anatumiza anawo+ Kum’mawa,+ kutali ndi mwana wake Isaki.  Masiku onse a moyo wa Abulahamu anali zaka 175.  Kenako, Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake.+  Chotero ana ake, Isaki ndi Isimaeli, anamuika iye m’manda. Anamuika m’phanga la Makipela, kumalo a Efuroni mwana wa Zohari Mheti, moyang’anana ndi Mamure.+ 10  Malo amenewa ndi omwe Abulahamu anagula kwa ana a Heti. Abulahamu anaikidwa kumeneko, komanso Sara mkazi wake.+ 11  Abulahamu atamwalira, Mulungu anapitiriza kudalitsa Isaki mwana wake.+ Isakiyo anali kukhala pafupi ndi Beere-lahai-roi.+ 12  Tsopano nayi mbiri ya Isimaeli+ mwana wa Abulahamu, amene Hagara Mwiguputo, kapolo wa Sara anaberekera Abulahamu.+ 13  Awa ndiwo mayina a ana a Isimaeli, amene kunachokera mabanja awo: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli, Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 14  Misima, Duma, Maasa, 15  Hadadi,+ Tema,+ Yeturi, Nafisi ndi Kedema.+ 16  Amenewa ndiwo ana a Isimaeli, potsata mayina awo, malinga ndi midzi yawo ndi misasa yawo yotchinga ndi mipanda.+ Anali atsogoleri okwanira 12 malinga ndi mafuko awo.+ 17  Zaka zonse zimene Isimaeli anakhala ndi moyo zinali 137. Kenako anamwalira, ndipo anaikidwa m’manda n’kugona ndi makolo ake.+ 18  Iwo anakhala m’mahema kuyambira ku Havila+ pafupi ndi Shura+ moyang’anana ndi Iguputo, mpaka ku Asuri. Anakhala pafupi ndi abale awo onse.+ 19  Tsopano nayi mbiri ya Isaki mwana wa Abulahamu.+ Abulahamu anabereka Isaki. 20  Isaki anali ndi zaka 40 pamene anakwatira Rabeka, mwana wa Betuele,+ Msiriya+ wa ku Padana-ramu, mlongo wake wa Labani, Msiriya. 21  Isaki anali kupembedzera Yehova mosalekeza, makamaka chifukwa cha mkazi wake,+ popeza iye anali wosabereka.+ Yehova anamva kupembedzera kwake,+ ndipo Rabeka mkazi wakeyo anakhala ndi pakati. 22  Ndiyeno ana amene anali m’mimba mwake anayamba kulimbana,+ moti iye anati: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, ndiye ndi bwino ndingofa.” Atatero anapita kukafunsira kwa Yehova.+ 23  Yehova anamuyankha kuti: “M’mimba mwako+ muli mitundu iwiri ya anthu, ndipo mitundu iwiri imene idzatuluka m’mimba mwakoyo idzakhala yosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamng’ono.”+ 24  Potsirizira pake, masiku oti Rabeka abereke anakwana, ndipo m’mimba mwake munali mapasa.+ 25  Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati wavala chovala chaubweya.+ Ndiye chifukwa chake anamutcha dzina lakuti Esau.*+ 26  Pambuyo pa iyeyu, panabadwa m’bale wake, dzanja lake litagwira chidendene cha Esau,+ choncho Isaki anapatsa mwanayo dzina lakuti Yakobo.+ Pamene Rabeka amabereka anawa n’kuti Isaki ali ndi zaka 60. 27  Anyamatawa anakula, ndipo Esau anakhala munthu wodziwa kusaka,+ munthu wokonda kuyenda m’tchire. Koma Yakobo anali kukhala nthawi yambiri m’mahema.+ Iye anali munthu wosalakwa.+ 28  Isaki anali kukonda kwambiri Esau chifukwa anali kum’phera nyama, koma Rabeka anali kukonda kwambiri Yakobo.+ 29  Tsiku lina Yakobo akuphika mphodza, Esau anafika kuchokera kutchire, ndipo anali atatopa. 30  Ndiyeno Esau anapempha Yakobo kuti: “Chonde, fulumira ndipatseko chakudya chofiiracho pang’ono, icho chofiiracho! Ndatopatu ine!” Ndiye chifukwa chake anatchedwa Edomu.*+ 31  Pamenepo Yakobo anayankha kuti: “Choyamba, undigulitse ukulu wako monga woyamba kubadwa.”+ 32  Esau anati: “Ine pano ndifa ndithu ndi njala, ndiye ukuluwo uli ndi phindu lanji kwa ine?” 33  Ndiyeno Yakobo anati: “Choyamba lumbira kwa ine!”+ Ndipo iye analumbiradi kwa Yakobo, n’kugulitsa kwa iye ukulu wake monga woyamba kubadwa.+ 34  Pamenepo Yakobo anapatsa Esau mkate ndi mphodza, ndipo iye anadya n’kumwa.+ Kenako, ananyamuka n’kumapita. Umu ndi mmene Esau ananyozera ukulu wake.+

Mawu a M'munsi

Dzina lakuti “Esau” limatanthauza “Wacheya.”
Dzina lakuti “Edomu” limatanthauza “Chofiira” kapena “Wofiira.”