Genesis 1:1-31
1 Pa chiyambi,+ Mulungu+ analenga+ kumwamba ndi dziko lapansi.+
2 Dziko lapansi linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso lopanda kanthu. Panali madzi akuya+ kwambiri ndipo pamwamba pake panali mdima wokhawokha. Ndipo mphamvu* ya Mulungu inali kuyendayenda+ pamwamba pa madzi akuyawo.+
3 Ndiyeno Mulungu anati:+ “Pakhale kuwala.” Ndipo kuwala kunakhalapo.+
4 Zitatero, Mulungu anaona kuti kuwalako kunali kwabwino. Kenako Mulungu analekanitsa kuwala ndi mdima.+
5 Ndiyeno Mulungu anatcha kuwalako Usana,+ koma mdimawo anautcha Usiku.+ Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku loyamba.
6 Mulungu tsopano anati: “Pakhale mlengalenga+ pakati pa madzi, ndiponso pakhale cholekanitsa pakati pa madzi ndi madzi.”+
7 Motero Mulungu anapanga mlengalenga. Anapanganso cholekanitsa madzi, kuti ena akhale pansi pa mlengalenga, ena akhale pamwamba pa mlengalenga.+ Ndipo zinaterodi.
8 Mulungu atatero, anatcha mlengalengawo Kumwamba.+ Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachiwiri.
9 Kenako Mulungu anati: “Madzi apansi pa thambo asonkhane malo amodzi, mtundanso uonekere.”+ Ndipo zinaterodi.
10 Tsopano Mulungu anatcha mtundawo Dziko,+ koma madzi osonkhanawo anawatcha Nyanja.+ Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.+
11 Ndiyeno Mulungu anati: “Dziko lapansi limere udzu, limere zomera zobala mbewu,+ limere mitengo yobala zipatso zokhala ndi mbewu yake, monga mwa mtundu wake.”+ Ndipo zinaterodi.
12 Motero dziko lapansi linamera udzu, zomera zobala mbewu monga mwa mtundu wake,+ mitengo yobala zipatso zokhala ndi mbewu zake monga mwa mtundu wake.+ Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino.
13 Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachitatu.
14 Kenako Mulungu anati: “Kukhale zounikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku+ ndipo zikhale zizindikiro, komanso kuti zisonyeze nyengo ndi masiku ndi zaka.+
15 Zikhale zounikira zakuthambo zowalitsa dziko lapansi.”+ Ndipo zinaterodi.
16 Motero Mulungu anapanga zounikira zikuluzikulu ziwiri. Chounikira chokulirapo anachipanga kuti chilamulire usana, ndi chocheperapo kuti chilamulire usiku, komanso nyenyezi.+
17 Mulungu atatero, anaziika kuthambo kuti ziunikire dziko lapansi,+
18 ndi kuti zilamulire usana ndi usiku, komanso zilekanitse kuwala ndi mdima.+ Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino.+
19 Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachinayi.
20 Kenako Mulungu anati: “M’madzi mukhale zamoyo zambirimbiri,+ ndiponso zolengedwa zouluka ziuluke m’mlengalenga mwa dziko lapansi.”+
21 Motero Mulungu analenga zilombo zikuluzikulu za m’nyanja+ ndi chamoyo chilichonse chokhala mmenemo.+ Nyanja inatulutsa zimenezi zambirimbiri monga mwa mitundu yake.+ Analenganso chamoyo chilichonse chouluka monga mwa mtundu wake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.
22 Mulungu atatero, anazidalitsa kuti: “Muswane, muchuluke, mudzaze nyanja zonse.+ Ndipo zolengedwa zouluka zichuluke padziko lapansi.”
23 Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku lachisanu.
24 Tsopano Mulungu anati: “Dziko lapansi+ likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake, nyama zoweta,+ nyama zokwawa,*+ komanso nyama zakutchire+ monga mwa mitundu yake.” Ndipo zinaterodi.
25 Motero Mulungu anapanga nyama zakutchire monga mwa mitundu yake. Anapanganso nyama zoweta monga mwa mitundu yake, komanso nyama iliyonse yokwawa panthaka monga mwa mtundu wake.+ Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.
26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu m’chifaniziro chathu,+ kuti akhale wofanana nafe.+ Ayang’anire nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso nyama zoweta. Ayang’anirenso dziko lonse lapansi ndi nyama zonse zokwawa padziko lapansi.”+
27 Motero Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake,+ m’chifaniziro cha Mulungu anam’lenga iye. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.+
28 Komanso, Mulungu anawadalitsa+ n’kuwauza kuti: “Muberekane,+ muchuluke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anire.+ Muyang’anirenso+ nsomba zam’nyanja ndi zolengedwa zouluka m’mlengalenga, komanso cholengedwa chilichonse chokwawa padziko lapansi.”
29 Tsopano Mulungu anati: “Taonani, ndakupatsani zomera zonse zobala mbewu zapadziko lonse lapansi, ndi mitengo yonse yobala zipatso za mbewu+ kuti zikhale chakudya chanu.+
30 Kwa nyama iliyonse yam’tchire ya padziko lapansi, ndi kwa cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga, komanso kwa chokwawa chilichonse cha padziko lapansi chimene chili ndi moyo, ndapereka zomera zonse kuti zikhale chakudya chawo.”+ Ndipo zinaterodi.
31 Ndiyeno Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.+ Panali madzulo ndiponso panali m’mawa, tsiku la 6.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “mzimu wa Mulungu.”
^ Mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “nyama zokwawa” amatanthauza zamoyo zimene zimayenda chokwawa monga nyama zing’onozing’ono, mbewa, abuluzi, njoka, ndi tizilombo tina ting’onoting’ono.