Genesis 27:1-46
27 Tsopano Isaki anakalamba moti maso ake sanali kuonanso.+ Ndiyeno anaitanitsa mwana wake wamkulu Esau,+ n’kumuuza kuti: “Mwana wanga!” Iye anayankha kuti: “Ine bambo!”
2 Isaki anapitiriza kuti: “Taona, ine tsopano ndakalamba.+ Tsiku lililonse ndikhoza kufa.+
3 Choncho tenga zida zako pompano. Utenge uta ndi kachikwama kako koikamo mivi ndipo upite kutchire ukandisakire nyama.+
4 Udzaikonze kuti ikome mmene ndimaikondera muja n’kundibweretsera. Ndikufuna ndikhwasule, ndipo ndikudalitse ndisanafe.”+
5 Koma pamene Isaki anali kulankhula ndi mwana wake Esau, Rabeka anali kumvetsera. Chotero Esau anapita kutchire kuti akaphe nyama n’kubwera nayo.+
6 Tsopano Rabeka anauza mwana wake Yakobo+ kuti: “Ndamva bambo ako akuuza mkulu wako Esau kuti,
7 ‘Ukandiphere nyama n’kuiphika bwino. Ndikufuna ndikhwasule, ndipo ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanafe.’+
8 Tsopano mwana wanga, tamvera mawu anga, ndipo uchite zimene ndikuuze.+
9 Pita kuli ziwetoko unditengereko ana a mbuzi awiri, onenepa bwino. Ndikufuna ndiwakonze mopatsa madyo mmene bambo ako amakondera muja.
10 Ndiye ukapereke kwa bambo ako akadye, kuti akudalitse asanamwalire.”
11 Pamenepo Yakobo anayankha Rabeka mayi ake kuti: “Koma m’bale wanga Esau ndi munthu wacheya,* pamene ine ndili ndi khungu losalala.+
12 Nanga bambo akakandikhudza?+ Ndithu andiona ngati wachipongwe.+ Ndikatero, ndithu ndidzitengera ndekha temberero, osati madalitso.”+
13 Koma mayi ake anamuyankha kuti: “Temberero limenelo libwere kwa ine m’malo mwa iwe mwana wanga.+ Ingomvera zimene ndanenazi. Pita ukanditengere ana a mbuziwo.”+
14 Chotero iye anawatenga n’kubwera nawo kwa mayi ake. Mayiwo anaphika nyamayo mopatsa madyo mmene bambo ake ankaikondera.
15 Zitatero, Rabeka anatenga zovala zokongola koposa za mwana wake wamkulu Esau,+ zimene anali nazo m’nyumba.+ Zovalazo anaveka mwana wake wamng’ono, Yakobo.+
16 Kenako, mayiwo anatenga zikopa za ana a mbuzi aja, n’kuveka Yakobo m’manja mwake ndi pakhosi pake popanda cheya.+
17 Ndiyeno anapatsa mwana wake Yakobo chakudya chokoma chimene anakonzacho, limodzi ndi mkate umene anaphika.+
18 Tsopano Yakobo anapita kumene kunali bambo ake n’kunena kuti: “Bambo!” Ndipo Isaki anayankha kuti: “Ine pano! Ndiwe ndani kodi mwana wanga?”
19 Yakobo anapitiriza kunena kwa bambo ake kuti: “Ndine Esau, mwana wanu woyamba.+ Ndachita zonse zimene munandituma. Dzukani, khalani pansi mudye nyama imene ndakupherani, kuti mundidalitse.”+
20 Pamenepo Isaki anafunsa mwana wake kuti: “Koma mwana wanga, waipeza bwanji mofulumira chonchi?” Iye anayankha kuti: “Yehova Mulungu wanu ndiye waikusira kwa ine kuti ndikumane nayo.”
21 Koma Isaki anauza Yakobo kuti: “Tayandikira ndikukhudze mwana wanga. Ndikufuna ndidziwe ngati ndiwedi mwana wanga Esau kapena ayi.”+
22 Chotero Yakobo anafika pafupi ndi Isaki bambo ake. Atamukhudza ananena kuti: “Mawu, akumveka kuti ndi a Yakobo, koma manja, akumveka kuti ndi a Esau.”+
23 Iye sanamuzindikire, chifukwa manja ake anali acheya ngati manja a Esau m’bale wake. Chotero anam’dalitsa.+
24 Kenako anamufunsanso kuti: “Koma ndiwedi mwana wanga Esau?” Iye anayankha kuti: “Ndine ndithu.”+
25 Tsopano Isaki anati: “Mwana wanga, ndipatsire nyama imene wandiphera ndidye kuti ndikudalitse.”+ Choncho anamupatsira ndipo anayamba kudya. Anamupatsiranso vinyo iye n’kumwa.
26 Kenako bambo akewo anamuuza kuti: “Ndiyandikire mwana wanga, undipsompsone.”+
27 Choncho anamuyandikira ndi kum’psompsona, ndipo anatha kumva kafungo ka zovala zake.+ Pamenepo anamudalitsa kuti:
“Eya, kafungo ka mwana wanga kakununkhira ngati fungo lokoma la munda umene Yehova waudalitsa.
28 Mulungu woona akupatse mame akumwamba,+ ndi nthaka yachonde ya dziko lapansi.+ Achulukitsenso zokolola zako ndi vinyo wako watsopano.+
29 Mafuko akutumikire ndipo mitundu ya anthu ikugwadire.+ Ukhale mbuye wa abale ako, ndipo ana a mayi ako akugwadire.+ Aliyense wokutemberera atembereredwe, ndipo aliyense wokudalitsa adalitsidwe.”+
30 Tsopano Isaki atangomaliza kudalitsa Yakobo, ndipo Yakoboyo atangotuluka kumene kwa Isaki bambo ake, Esau m’bale wake anafika kuchokera kokasaka nyama.+
31 Iyenso anakonzera bambo ake nyama ija mopatsa madyo. Kenako anapita nayo kwa bambo ake n’kuwauza kuti: “Bambo, dzukani mudye nyama imene ndakupherani ine mwana wanu, kuti mundidalitse.”+
32 Ndiyeno Isaki, bambo ake, anati: “Nanga iwenso ndiwe ndani?” Ndipo iye anayankha kuti: “Ndine mwana wanu, mwana wanu woyamba Esau.”+
33 Pamenepo Isaki anayamba kunjenjemera koopsa, ndipo anati: “Nanga ndani uja wandiphera nyama kutchire, imene wandibweretsera kuti ndidye? Ine ndadya yonse iwe usanabwere, moti ndamudalitsa iyeyo. Ndipo adzadalitsikadi!”+
34 Atamva mawu a bambo ake, Esau anayamba kulira ndi kukuwa mogonthetsa m’khutu, komanso mowawidwa mtima kwambiri.+ Iye anachonderera bambo ake kuti: “Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde!”+
35 Pamenepo Isaki anapitiriza kunena kuti: “M’bale wako wabwera mwachinyengo, ndipo walandira madalitso omwe anali ako.”+
36 Ndiyeno Esau anati: “Aka tsopano n’kachiwiri akundichenjerera amene uja!+ Kodi si chifukwa chake dzina lake ndi Yakobo?* Ukulu wanga anatenga kale,+ apa tsopano watenganso madalitso anga!”+ Iye anapitiriza kuti: “Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?”
37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsanso abale ake onse kuti akhale atumiki ake.+ Komanso ndam’dalitsira zokolola zake ndi vinyo wake watsopano.+ Nanga chatsalanso n’chiyani choti ndikuchitire mwana wanga?”
38 Pamenepo Esau anafunsa bambo ake kuti: “Bambo, ngakhale limodzi dalitso silinatsaleko? Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde!”+ Esau atatero analira mofuula kwambiri, misozi ili mbwembwembwe.+
39 Koma Isaki bambo ake anamuuza kuti:
“Taona, udzakhala kutali ndi nthaka yachonde, kotalikirana ndi mame akumwamba.+
40 Udzakhalira moyo lupanga+ ndipo udzatumikira m’bale wako.+ Koma ukadzatopa ndi goli lake, udzalithyola ndi kulichotsa m’khosi mwako.”+
41 Choncho, Esau anasunga chidani kwa Yakobo mumtima mwake.+ Anamuda chifukwa cha madalitso amene bambo ake anamupatsa. Iye anapitiriza kunena mumtima mwake+ kuti: “Masiku olira maliro a bambo anga ali pafupi.+ Pambuyo pake, ndidzamupha m’bale wanga Yakobo.”+
42 Pamene Rabeka anauzidwa zimene mwana wake wamkulu Esau ananena, nthawi yomweyo anaitanitsa mwana wake wamng’ono Yakobo n’kumuuza kuti: “M’bale wako Esau akufuna akhazike mtima wake pansi pokubwezera. Iye akufuna kuti akuphe.+
43 Tsopano, tamvera zimene ndikuuze mwana wanga.+ Nyamuka, thawira kwa Labani mlongo wanga, ku Harana.+
44 Ukakhale naye kwa masiku ndithu, kufikira ukali wa m’bale wako utatha.+
45 Ukakhaleko kufikira mkwiyo wa m’bale wako utaphwa, mpaka ataiwala zimene unamuchitira.+ Pamenepo ndidzatuma anthu kuti adzakutenge kumeneko. Kodi nditayirenji ana awiri pa tsiku limodzi?”
46 Zitatha izi, Rabeka anali kuuza Isaki nthawi ndi nthawi kuti: “Ndafika ponyansidwa nawo moyo wanga chifukwa cha ana aakazi achihetiwa.+ Ngati Yakobo atenga mkazi kuno pakati pa ana achiheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!”+
Mawu a M'munsi
^ “Cheya” ndi ubweya wa pathupi la munthu.
^ Dzina lakuti “Yakobo” limatanthauza “Kugwira Chidendene” ndiponso kuti “Wochenjerera Mnzake.”