Genesis 49:1-33

49  Pambuyo pake, Yakobo anaitana ana ake n’kuwauza kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitika kwa inu m’masiku am’tsogolo.  Bwerani pamodzi nonse kuti mumvetsere, inu ana a Yakobo. Bwerani mumvetsere kwa Isiraeli bambo anu.+  “Rubeni, iwe ndiwe mwana wanga woyamba kubadwa,+ nyonga yanga ndi poyambira mphamvu zanga zobereka.+ Unayenera kukhala ndi ulemu wopambana ndi mphamvu zopambana.  Usakhale wopambana, chifukwa ndi khalidwe lako lotayirira ngati madzi osefukira,+ unakwera pogona bambo ako.+ Unaipitsa bedi langa pa nthawiyo.+ Anagonapo ndithu ameneyu!  “Simiyoni ndi Levi m’pachibale pawo.+ Malupanga awo ndiwo zida zochitira zachiwawa.+  Pagulu lawo, moyo wanga usakhale nawo.+ Maganizo anga asagwirizane ndi mpingo wawo,+ chifukwa atakwiya anapha anthu,+ ndipo mwankhanza zawo, anapundula* ng’ombe zamphongo.  Utembereredwe mkwiyo wawo+ chifukwa ndi wankhanza,+ ndi ukali wawo chifukwa umachita mwachiwawa.+ Ndidzawamwaza mwa Yakobo, ndipo ndidzawabalalitsa mwa Isiraeli.+  “Koma iwe Yuda,+ abale ako adzakutamanda.+ Dzanja lako lidzakhala pambuyo pa khosi la adani ako.+ Ana a bambo ako adzakugwadira.+  Yuda ndi mwana wa mkango.+ Umapha nyama n’kubwerako ndithu, mwana wanga. Iye amapinda mawondo ake n’kudziwongola ngati mkango utagona pansi. Ndipo monga mkango, ndani angamudzutse?+ 10  Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, kufikira Silo*+ atabwera. Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ 11  Atamanga bulu wake wamphongo pamtengo wa mpesa, ndi kamwana ka bulu wake wamkazi pamtengo wa mpesa wabwino, ndithu, adzachapa zovala zake m’vinyo, ndi malaya ake m’madzi ofiira a mphesa.+ 12  Maso ake ndi ofiira ndi vinyo, ndipo mano ake ndi oyera ndi mkaka. 13  “Zebuloni adzakhala kugombe la nyanja,+ pafupi ndi gombe lokochezapo zombo.+ Malire ake akutali adzakhala cha ku Sidoni.+ 14  “Isakara+ ndi bulu wa mafupa olimba, amagona pansi atasenza matumba a katundu uku ndi uku. 15  Adzaona kuti malo opumirawo ndi abwino, ndi kuti dzikolo n’losangalatsa. Adzaweramitsa phewa lake kuti anyamule akatundu, ndipo adzakakamizidwa kugwira ntchito yakalavulagaga ngati kapolo. 16  “Dani adzaweruza anthu a mtundu wake monga mmodzi wa mafuko a Isiraeli.+ 17  Dani adzakhala njoka yobisala m’mbali mwa msewu, njoka yokhala ndi tinyanga yobisala m’mphepete mwa njira, imene imaluma chidendene cha hatchi ndipo wokwerapo amagwa chagada.+ 18  Ndithu ndidzayembekezera chipulumutso kwa inu, Yehova.+ 19  “Kunena za Gadi, gulu la achifwamba lidzamuukira, koma iye adzawathira nkhondo, ndipo achifwambawo pothawa iye adzawakantha koopsa.+ 20  “Chakudya chochokera kwa Aseri chidzakhala chonona,+ ndipo chakudya chokoma cha mfumu chidzachokera kwa iye.+ 21  “Nafitali+ ndi mbawala yaikazi yopepuka miyendo, ndipo amanena mawu okoma.+ 22  “Yosefe ndi mphukira yamtengo wobala zipatso.+ Ndithu iye ndi mphukira yamtengo wobala zipatso pakasupe.+ Iye ndi mtengo woponya nthambi zake pamwamba pa khoma* la mpanda.+ 23  Oponya mivi ndi uta sanaleke kumuzunza, kumulasa ndi kumusungira chidani.+ 24  Koma uta wake unakhalabe pamalo ake achikhalire,+ ndipo manja ake anali amphamvu ndi ochenjera.+ M’busayo, Mwala wa Isiraeli,+ akuchokera m’manja mwa Wamphamvu wa Yakobo.+ M’busayo akuchokera kumeneko ndithu. 25  Iye ndi wochokera kwa Mulungu wa bambo ako,+ ndipo adzakuthandiza.+ Iye ali ndi Wamphamvuyonse,+ ndipo Mulunguyo adzakudalitsa ndi madalitso ochokera kumwamba,+ ndi madalitso a pansi pa madzi akuya,+ ndi madalitso a mabere a mkaka wambiri, ndi a mimba yobereka.+ 26  Madalitso a bambo ako adzapambana madalitso a mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.+ Adzapambananso ulemerero wa zitunda zosatha.+ Madalitsowo adzakhalabe pamutu pa Yosefe, paliwombo pa wosankhidwa pakati pa abale ake.+ 27  “Benjamini adzapitiriza kukhadzula ngati mmbulu.+ M’mawa adzadya nyama imene wagwira, ndipo madzulo adzagawa zimene wafunkha.”+ 28  Onsewa ndiwo mafuko 12 a Isiraeli, ndipo izi n’zimene bambo awo analankhula kwa iwo powadalitsa. Anapatsa aliyense wa iwo madalitso ake omuyenerera.+ 29  Atatero anawalamula kuti: “Ine uno ndi ulendo wopita kumene kunapita makolo anga.+ Mukandiike limodzi ndi makolo anga, m’phanga limene lili m’munda wa Efuroni, Mhiti.+ 30  Ndithu mukandiike m’phanga limene lili m’munda wa Makipela, umene uli moyang’anana ndi munda wa Mamure, m’dziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Mhiti, kuti akhale ndi manda.+ 31  Kumeneko n’kumene anaika Abulahamu ndi mkazi wake Sara.+ N’kumene anaika Isaki ndi Rabeka mkazi wake,+ ndipo n’kumene ndinaika Leya. 32  Munda umene anaugulawo, ndiponso phanga limene lili mmenemo, zinali za ana a Heti.”+ 33  Yakobo atamaliza kulangiza ana akewo, anabwezeranso miyendo yake pabedi, n’kumwalira. Kenako anaikidwa m’manda n’kugona limodzi ndi makolo ake.+

Mawu a M'munsi

Anali kuzipundula mwa kudula mtsempha wakuseri kwa mwendo wam’mbuyo.
Dzina lakuti “Silo” limatanthauza “Mwini Wake.”
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”