Genesis 9:1-29

9  Kenako Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.+  Ndipo cholengedwa chilichonse chamoyo cha padziko lapansi, cholengedwa chilichonse chouluka m’mlengalenga, chilichonse chokwawa padziko lapansi, ndi nsomba zonse za m’nyanja, zizikuopani. Tsopano ndapereka zonsezi m’manja mwanu.+  Nyama yamoyo iliyonse ikhale chakudya chanu.+ Komanso ndikukupatsani zamasamba zonse kuti zikhale chakudya chanu.+  Koma musadye+ nyama pamodzi ndi magazi+ ake, amene ndiwo moyo+ wake.  Kuwonjezera pamenepo, ndidzafunsa za magazi anu. Ngati magazi anu akhetsedwa ndi chamoyo chilichonse, chamoyocho chiyenera kuphedwa, ndipo ngati moyo wa munthu wachotsedwa ndi munthu mnzake ndidzaufuna kuchokera kwa iye.+  Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake.  Koma inuyo muberekane, muchuluke, mufalikire padziko lonse lapansi.”+  Ndipo Mulungu anauza Nowa ndi ana ake kuti:  “Tsopano ine ndikuchita pangano+ ndi inu, ndi ana obadwa pambuyo panu,+ 10  komanso ndi chamoyo chamtundu uliwonse chimene muli nacho limodzi, pakati pa mbalame ndi pakati pa nyama zonse zamoyo za padziko lapansi, kuyambira zonse zotuluka m’chingalawa, kufikira cholengedwa chamoyo chilichonse cha padziko lapansi.+ 11  Pangano limene ndikuchita nanu ndi ili: Zamoyo zonse sizidzawonongedwanso ndi madzi a chigumula, ndipo chigumula sichidzachitikanso n’kuwononga dziko lapansi.”+ 12  Mulungu anawonjezera kuti: “Nachi chizindikiro+ cha pangano limene ndikuika pakati pa inu ndi ine, ndi pakati pa chamoyo chilichonse chimene muli nacho limodzi, ku mibadwomibadwo mpaka kalekale. 13  Ndiika utawaleza+ mumtambo, kuti ukhale chizindikiro cha pangano pakati pa ine ndi dziko lapansi. 14  Ndikabweretsa mtambo padziko lapansi, utawaleza udzaonekeranso mumtambowo. 15  Ndipo ndizikumbukira ndithu pangano+ la pakati pa ine ndi inu ndi chamoyo chilichonse.+ Komanso madzi sadzachitanso chigumula ndi kuwononga zamoyo zonse.+ 16  Utawalezawo uzionekera mumtambo.+ Ndipo ine ndiziuona ndithu, n’kukumbukira pangano limene lidzakhale mpaka kalekale,+ la pakati pa ine ndi chamoyo chilichonse chimene chili padziko lapansi.”+ 17  Kenako Mulungu anabwereza kuuza Nowa kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndikukhazikitsa pakati pa ine ndi zamoyo zonse zimene zili padziko lapansi.”+ 18  Ana a Nowa+ amene anatuluka m’chingalawa anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Pambuyo pake, Hamu anakhala tate wake wa Kanani.+ 19  Atatuwa ndiwo anali ana a Nowa. Ndipo anthu onse amene ali padziko lapansi anachokera mwa iwowa.+ 20  Tsopano Nowa anakhala mlimi,+ ndipo analima munda wa mpesa.+ 21  Pambuyo pake, iye anamwa vinyo ndi kuledzera naye.+ Kenako, ali m’hema wake, anavula zovala zake. 22  Ndiyeno Hamu,+ bambo wake wa Kanani, anaona maliseche a bambo ake.+ Atatero, anapita panja n’kukauza abale ake awiri aja zimenezo.+ 23  Atamva zimenezo, Semu ndi Yafeti anatenga chofunda+ atachigwirira pa mapewa pawo, n’kuyenda chafutambuyo. Atatero, anafunditsa bambo awo iwo akuyang’ana kumbali, kuwabisa maliseche, moti sanaone maliseche a bambo awo.+ 24  Kenako, Nowa anagalamuka vinyo atamuthera m’mutu mwake, ndipo anamva zimene mwana wake wamng’ono anachita kwa iye. 25  Pamenepo iye anati: “Ndikutemberera Kanani.+ Akhale kapolo wapansi kwambiri kwa abale ake.”+ 26  Anawonjezera kuti:“Adalitsike Yehova,+ Mulungu wa Semu,Ndipo Kanani akhale kapolo kwa iye.+ 27  Mulungu apereke malo aakulu kwa Yafeti,Ndipo azikhala m’mahema a Semu.+Koma Kanani akhalenso kapolo wa Yafeti.” 28  Pambuyo pa chigumula,+ Nowa anakhalabe ndi moyo zaka zina 350. 29  Chotero, masiku onse a Nowa anakwana zaka 950, kenako anamwalira.+

Mawu a M'munsi