Genesis 16:1-16

16  Tsopano Sarai, mkazi wa Abulamu, sanamuberekere ana.+ Koma Saraiyo anali ndi kapolo wake Mwiguputo, dzina lake Hagara.+  Choncho Sarai anauza Abulamu kuti: “Yehova ananditseka kuti ndisabereke ana.+ Tsopano gonani ndi kapolo wanga. Mwinatu ndingapeze ana kuchokera kwa iye.”+ Chotero Abulamu anamvera mawu a Sarai.+  Pamenepo Sarai mkazi wa Abulamu anapereka Hagara, kapolo wake Mwiguputo, kwa mwamuna wake Abulamu kuti akhale mkazi wake.+ Zimenezi zinachitika Abulamu atakhala zaka 10 m’dziko la Kanani.  Chotero Abulamu anagona ndi Hagara ndipo Hagara anatenga pakati. Hagara atazindikira kuti ali ndi pakati, anayamba kuchitira chipongwe mbuye wake Sarai.+  Sarai ataona zimenezi anauza Abulamu kuti: “Mlandu wa chipongwe chikundichitikirachi ukhale pa inu. Ine ndinapereka kapolo wanga kwa inu kuti akhale mkazi wanu, koma iye poona kuti watenga pakati wayamba kundichitira chipongwe. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu.”+  Poyankha, Abulamu anauza Sarai+ kuti: “Kapolo wakoyutu ali m’manja mwako. Chita chimene ukuchiona kuti n’chabwino.”+ Pamenepo Sarai anayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo anathawa kwa Sarai.+  Pambuyo pake, mngelo wa Yehova+ anakapeza Hagara m’chipululu ali pakasupe wamadzi wa panjira yopita ku Shura.+  Ndiyeno mngeloyo anati: “Hagara kapolo wa Sarai, kodi ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndikuthawa kwa mbuye wanga Sarai.”  Mngelo wa Yehovayo anauza Hagara kuti: “Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukadzichepetse kwa iye.”+ 10  Kenako mngelo wa Yehovayo anamuuzanso kuti: “Ndidzachulukitsa kwambiri mbewu yako,+ moti idzakhala yosawerengeka.”+ 11  Mngelo wa Yehovayo anapitiriza kulankhula ndi mkaziyo kuti: “Taona, panopo uli ndi pakati, ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo udzamutche Isimaeli,+ pakuti Yehova wamva kulira kwako.+ 12  Mwanayo adzakhala ngati mbidzi. Dzanja lake lidzalimbana ndi aliyense, ndipo dzanja la aliyense lidzalimbana naye.+ Iye adzamanga msasa pamaso pa abale ake onse.”+ 13  Ndiyeno Hagara anayamba kutchula dzina la Yehova n’kunena kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”*+ Anatinso: “Kodi nanenso pano ndaona wotha kundionayo?” 14  Chimenechi ndicho chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-lahai-roi,*+ ndipo chili pakati pa Kadesi ndi Beredi. 15  M’kupita kwa nthawi, Hagara anaberekera Abulamu mwana wamwamuna ndipo Abulamu anatcha mwanayo dzina lakuti Isimaeli.+ 16  Pamene Hagara anaberekera Abulamu Isimaeli, Abulamuyo n’kuti ali ndi zaka 86.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “amene akundiona,” kapena “amene amalola kuonedwa.”
Dzina lakuti “Beere-lahai-roi” limatanthauza “Chitsime cha Wamoyo Amene Amandionayo.”