Genesis 4:1-26

4  Kenako Adamu anagona ndi Hava mkazi wake, ndipo mkaziyo anatenga pakati.+ M’kupita kwa nthawi, mkaziyo anabereka Kaini*+ n’kunena kuti: “Ndabereka mwana wamwamuna ndi thandizo la Yehova.”+  Pambuyo pake, Hava anabereka Abele+ m’bale wake wa Kaini. Abele anakhala woweta nkhosa,+ koma Kaini anali mlimi.+  Patapita nthawi, Kaini anabweretsa zina mwa zokolola zake zakumunda,+ n’kuzipereka nsembe kwa Yehova.+  Abele nayenso anabweretsa ana oyamba+ a nkhosa zake n’kuwapereka nsembe, ndipo anaperekanso nsembe mafuta a nkhosazo.+ Yehova anakondwera ndi Abele ndipo analandira nsembe yake,+  koma sanakondwere naye Kaini ndi nsembe yake+ m’pang’ono pomwe. Chotero Kaini anapsa mtima kwambiri+ ndipo nkhope yake inagwa.  Pamenepo Yehova anafunsa Kaini kuti: “N’chifukwa chiyani wapsa mtima choncho, ndipo nkhope yako yagweranji?  Ukasintha n’kuchita chabwino, sindikuyanja kodi?+ Koma ngati susintha kuti uchite chabwino, uchimo wamyata pakhomo kukudikirira, ndipo ukulakalaka kukudya.+ Kodi iweyo suugonjetsa?”+  Zitatero, Kaini anauza Abele m’bale wake kuti: “Tiye tipite kumunda.” Ali kumeneko, Kaini anam’kantha Abele m’bale wake n’kumupha.+  Pambuyo pake, Yehova anafunsa Kaini kuti: “Kodi m’bale wako Abele ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Sindikudziwa. Kodi ndine mlonda wa m’bale wangayo?”+ 10  Pamenepo Mulungu anati: “N’chiyani chimene wachitachi? Tamvera tsono. Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.+ 11  Tsopano ndiwe wotembereredwa, ndipo ndikukupitikitsa m’dera limene nthaka+ yake yatsegula pakamwa ndi kulandira magazi a m’bale wako, amene iwe wakhetsa ndi manja ako.+ 12  Uziti ukalima, nthaka sizikubalira mokwanira.+ Udzakhala moyo woyendayenda ndi wothawathawa padziko lapansi.”+ 13  Kaini atamva zimenezi anadandaulira Yehova kuti: “Chilango cha kulakwa kwanga n’chachikulu kwambiri moti sindingathe kuchipirira. 14  Lero ndiye mukundipitikitsa pamalo ano ndi pamaso panu.+ Ndidzakhala woyendayenda+ ndi wothawathawa padziko lapansi, ndipo n’zoonekeratu kuti aliyense wondipeza, adzandipha ndithu.”+ 15  Yehova atamva zimenezi anauza Kaini kuti: “Pa chifukwa chimenechi, aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa maulendo 7.”+ Choncho Yehova anaikira Kaini chizindikiro kuti aliyense womupeza asamuphe.+ 16  Pamenepo Kaini anachoka pamaso pa Yehova+ n’kupita kukakhala kudera la kum’mawa kwa Edeni monga wothawa. 17  Patapita nthawi, Kaini anagona ndi mkazi wake+ ndipo mkaziyo anatenga pakati n’kubereka Inoki. Ndiyeno Kaini anayamba kumanga mzinda umene anautcha dzina la mwana wake lakuti Inoki.+ 18  Kenako Inoki anabereka Irade, Irade anabereka Mehuyaeli, Mehuyaeli anabereka Metusaeli, ndipo Metusaeli anabereka Lameki. 19  Lameki anakwatira akazi awiri. Woyamba anali Ada ndipo wachiwiri anali Zila. 20  M’kupita kwa nthawi Ada anabereka Yabala, amene anakhala tate wa anthu okhala m’mahema+ ndi oweta ziweto.+ 21  M’bale wake wa Yabala anali Yubala. Ameneyu ndiye anali tate wa onse oimba zeze+ ndi chitoliro.+ 22  Koma Zila anabereka Tubala-kaini, amene anali mmisiri wosula zipangizo zamtundu uliwonse, zamkuwa ndi zachitsulo.+ Ndipo mlongo wake wa Tubala-kaini anali Naama. 23  Kenako Lameki anakonzera akazi ake, Ada ndi Zila ndakatulo iyi: “Tamverani mawu anga inu akazi a Lameki.Tcherani khutu ku zonena zanga:Ndapha munthu chifukwa chondipweteka,Ndaphadi, mnyamata chifukwa chondimenya. 24  Ngati wopha Kaini ati adzalangidwe maulendo 7,+Ndiyetu wopha ine Lameki, adzalangidwa maulendo 77.” 25  Adamu anagonanso ndi mkazi wake Hava, ndipo mkaziyo anabereka mwana wamwamuna yemwe anamupatsa dzina lakuti Seti.*+ Hava anapereka dzina limeneli chifukwa chakuti Seti atabadwa, Havayo ananena kuti: “Mulungu wandipatsa* mbewu ina m’malo mwa Abele, popeza iye anaphedwa ndi Kaini.”+ 26  Nayenso Seti anabereka mwana wamwamuna n’kumutcha dzina lakuti Enosi.+ Pa nthawi imeneyi, anthu anayamba kuitanira pa dzina la Yehova.+

Mawu a M'munsi

Dzina limeneli limatanthauza “Woberekedwa.”
Dzina lachiheberi lakuti “Seti” limatanthauza “Kusankhidwa; Kuika; Kukhazikitsa,” m’lingaliro la kulowa m’malo.
Kapena “wandisankhira.”